1 Samueli 19:1-24

19  Patapita nthawi, Sauli anauza mwana wake Yonatani ndi atumiki ake onse kuti akufuna kupha Davide.+  Koma Yonatani, mwana wa Sauli, anali kukonda kwambiri Davide.+ Choncho Yonatani anauza Davide kuti: “Sauli, bambo anga, akufuna kukupha. Chonde, mawa m’mawa ukhale wosamala. Ukakhale pamalo obisika ndipo ukabisalebe choncho.+  Ine ndipita nawo kutchire kumene ukabisaleko ndipo ndikaima pafupi ndi bambo anga. Bambo anga ndilankhula nawo za iwe, ndipo ndionetsetsa zimene zichitike. Zilizonse zimene ndaonazo ndidzakuuza, sindilephera.”+  Chotero Yonatani analankhula zabwino+ za Davide kwa Sauli bambo ake, kuti: “Mfumu isachimwire+ mtumiki wake Davide, chifukwa iye sanakuchimwireni, ndipo wakhala akukuchitirani zinthu zabwino kwambiri.+  Iye anaika moyo wake pangozi*+ n’kupha Mfilisiti uja,+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu+ kwa Aisiraeli onse. Inuyo munaona zimenezi zikuchitika, ndipo munasangalala. Ndiye n’chifukwa chiyani mukufuna kuchimwira magazi osalakwa, mwa kupha Davide+ popanda chifukwa?”+  Sauli anamvera mawu a Yonatani, ndipo analumbira kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ Davide saphedwa.”  Pambuyo pake, Yonatani anaitana Davide ndi kumuuza mawu onsewa. Kenako, Yonatani anatenga Davide ndi kupita naye kwa Sauli, moti Davide anapitiriza kukhala ndi Sauli monga kale.+  Patapita nthawi, nkhondo inayambanso ndi Afilisiti. Davide anapita kukamenya nkhondoyo ndipo anakantha ndi kupha Afilisiti ochuluka,+ moti Afilisitiwo anathawa pamaso pake.+  Ndiyeno mzimu woipa wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa Sauli ali m’nyumba mwake, atatenga mkondo m’manja mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kumuimbira nyimbo. 10  Zitatero, Sauli anafuna kulasa Davide kuti amukhomerere kukhoma ndi mkondo.+ Koma Davide anaulewa+ pamaso pa Sauli, moti mkondowo unalasa khoma. Pamenepo, Davide anathawa kuti adzipulumutse usiku umenewo.+ 11  Kenako Sauli anatumiza amithenga+ kunyumba ya Davide kuti akaizungulire ndi kupha Davide m’mawa mwa tsiku limenelo.+ Koma Mikala mkazi wa Davide anauza Davideyo kuti: “Ngati supulumutsa moyo wako usiku uno, mawa ukhala utaphedwa.” 12  Nthawi yomweyo, Mikala anathandiza Davide kutulukira pawindo kuti athawe ndi kupulumuka.+ 13  Ndiyeno Mikala anatenga fano la terafi+ n’kuliika pabedi. Iye anaika ukonde waubweya wa mbuzi pamene Davide anali kutsamiritsa mutu wake, kenako anafunditsa fanolo ndi chovala. 14  Tsopano Sauli anatuma amithenga kuti akagwire Davide, koma Mikala anati: “Akudwala.”+ 15  Choncho Sauli anatuma amithengawo kuti akaone Davide, ndipo anawauza kuti: “Mubwere naye kuno pabedi lakelo kuti adzaphedwe.”+ 16  Amithengawo atalowa, anangopeza fano la terafi lili pabedi, ukonde waubweya wa mbuzi uli pamene Davide anali kutsamiritsa mutu wake. 17  Zitatero Sauli anauza Mikala kuti: “N’chifukwa chiyani wandipusitsa+ chotere mwa kuthawitsa mdani wanga+ kuti apulumuke?” Poyankha, Mikala anauza Sauli kuti: “Iyeyo anandiuza kuti, ‘Ndilole ndipite! Apo ayi, ndikupha.’” 18  Choncho Davide anathawa ndi kupulumuka,+ moti anafika kwa Samueli ku Rama.+ Atafika kumeneko anasimbira Samueli zonse zimene Sauli anam’chitira. Kenako Davide ndi Samueli anachoka ndi kupita kukakhala ku Nayoti.+ 19  Patapita nthawi, uthenga unam’peza Sauli wonena kuti: “Davide alitu ku Nayoti, ku Rama.” 20  Nthawi yomweyo, Sauli anatumiza amithenga kuti akagwire Davide. Amithengawo ataona aneneri achikulire akunenera, Samueli ataima pakati pawo kuwatsogolera, mzimu+ wa Mulungu unafika pa amithenga a Sauli aja, ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri.+ 21  Sauli atamuuza zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza amithenga ena, ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. Zitatero, Sauli anatumiza amithenga enanso, gulu lachitatu, koma amenewanso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. 22  Pamapeto pake, Sauli nayenso anapita ku Rama. Atafika pachitsime chachikulu chimene chili ku Seku, anayamba kufunsa kuti: “Kodi Samueli ndi Davide ali kuti?” Poyankha, iwo anati: “Iwo ali ku Nayoti,+ ku Rama.” 23  Pamenepo anapitiriza ulendo wake wopita ku Nayoti, ku Rama, ndipo mzimu+ wa Mulungu unafika ngakhalenso pa iye. Zitatero, iye anapitiriza kuyenda ndi kuchita zinthu ngati mneneri mpaka kukafika ku Nayoti, ku Rama. 24  Sauli nayenso anavula zovala zake, ndipo nayenso anayamba kuchita zinthu ngati mneneri pamaso pa Samueli. Iye anagwa pansi ndi kugona pomwepo ali wosavala* usana wonse ndi usiku wonse.+ N’chifukwa chake pali mawu okuluwika akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anaika moyo wake m’dzanja lake.”
Kapena kuti, “atavala zovala zamkati zokha.”