1 Samueli 18:1-30

18  Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula ndi Sauli, Yonatani+ anagwirizana kwambiri+ ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.+  Tsiku limenelo Sauli anatenga Davide, ndipo sanamulole kubwerera kunyumba ya bambo ake.+  Yonatani ndi Davide anachita pangano,+ chifukwa Yonatani anali kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera.+  Pamenepo Yonatani anavula malaya ake akunja odula manja ndi kupatsa Davide. Anam’patsanso zovala zina ngakhalenso lupanga, uta ndi lamba wake.  Choncho Davide anayamba kupita kunkhondo. Kulikonse kumene Sauli wamutumiza anali kuchita zinthu mwanzeru,+ moti Sauli anamuika kukhala woyang’anira asilikali.+ Zimenezi zinasangalatsa anthu onse komanso atumiki a Sauli.  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene asilikali anali kubwerera, Davide atakantha Mfilisiti uja, akazi anayamba kutuluka m’mizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ ndi kuvina. Iwo anali kupita kukachingamira mfumu Sauli mosangalala,+ akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu.  Akazi amene anali kusangalalawo anali kuimba molandizana mawu kuti:“Sauli wakantha adani ake masauzande,Ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi.”+  Sauli atamva zimenezi anakwiya kwambiri+ ndipo mawu amenewa anamuipira, moti anayamba kuganiza kuti: “Davide amupatsa masauzande makumimakumi, koma ine angondipatsa masauzande okha. Ndiye kuti kwangotsala kum’patsa ufumuwu basi!”+  Kuyambira tsiku limenelo, Sauli anayamba kuyang’ana Davide ndi diso loipa.+ 10  Tsiku lotsatira,+ mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa Sauli,+ moti anayamba kuchita zinthu ngati mneneri+ m’nyumba mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kuimba nyimbo+ ngati kale ndipo Sauli anali ndi mkondo m’manja mwake.+ 11  Ndiyeno Sauli anaponya mkondo uja+ ndi kunena kuti: “Ndilasa Davide ndi kumukhomerera kukhoma* ndi mkondowu!”+ Koma Davide anamuthawa, ndipo zimenezi zinachitika kawiri konse.+ 12  Zitatero, Sauli anachita mantha+ ndi Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo,+ koma Sauliyo anali atam’chokera.+ 13  Chotero Sauli anachotsa Davide kuti asamakhale naye pafupi,+ ndipo anamuika kukhala mtsogoleri wa gulu la asilikali 1,000, moti Davide anali kutsogolera asilikali amenewo.+ 14  Davide anali kuchita zinthu mwanzeru+ nthawi zonse m’njira zake zonse, ndipo Yehova anali naye.+ 15  Sauli nayenso anali kuona kuti Davide akuchita zinthu mwanzeru,+ moti anali kuchita naye mantha. 16  Anthu onse a mu Isiraeli ndi Yuda anali kum’konda Davide, chifukwa iye anali kuwatsogolera. 17  Ndiyeno Sauli anauza Davide kuti: “Mwana wanga wamkazi wamkulu Merabu+ alipo. Ndidzakupatsa ameneyu kuti akhale mkazi wako.+ Koma iwe undisonyeze kulimba mtima kwako ndi kumenya nkhondo za Yehova.”+ Mumtima mwake Sauli anati: “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisiti.”+ 18  Koma Davide anayankha Sauli kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?”+ 19  Ndiyeno itafika nthawi yopereka Merabu mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, anali atam’pereka kale kwa Adiriyeli+ Mmeholati+ kuti akhale mkazi wake. 20  Tsopano Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anali kukonda Davide, ndipo anthu anauza Sauli zimenezi. Sauli atamva nkhani imeneyi anasangalala. 21  Chotero Sauli anati: “Ndidzam’patsa Mikala kuti akhale msampha kwa iye,+ ndi kuti Afilisiti amuphe.” Zitatero Sauli anauza Davide kuti: “Lero uchite nane mgwirizano wa ukwati mwa kutenga mmodzi mwa akazi awiriwa.” 22  Kuwonjezera pamenepo, Sauli analamula atumiki ake kuti: “Mukalankhule ndi Davide mwachinsinsi kuti, ‘Mfumutu ikusangalala nawe, ndipo atumiki ake onse akukonda kwambiri. Ndiye chita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu.’” 23  Atumiki a Sauli anapita kukauza Davide mawu amenewa, koma Davide anawayankha kuti: “Kodi mukuona ngati ndi nkhani yaing’ono kuchita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu, pamene ine ndine munthu wosauka+ ndi wonyozeka?”+ 24  Ndiyeno atumikiwo anauza Sauli kuti: “Izi n’zimene Davide anatiyankha.” 25  Pamenepo Sauli anati: “Amuna inu, mukauze Davide kuti, ‘Sikuti mfumu ikufuna ndalama za ukwati,+ koma ikufuna makungu 100 akunsonga + a Afilisiti, kuti ibwezere+ adani ake.’” Koma Sauli anali atakonza chiwembu kuti Davide aphedwe ndi Afilisiti. 26  Choncho atumiki a Sauliwo anauza Davide uthengawo, ndipo Davide anavomera kuchita mgwirizano wa ukwati+ ndi mfumu. Masiku oti apereke makunguwo kwa mfumuyo asanathe, 27  Davide pamodzi ndi asilikali ake ananyamuka, ndipo anakapha+ amuna 200 achifilisiti. Ndiyeno Davide anabwerako atatenga makungu awo a kunsonga,+ ndipo makungu onsewo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Pamenepo Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi, kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+ 28  Sauli anaona ndi kudziwa kuti Yehova ali ndi Davide.+ Ndipo Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, anam’konda kwambiri Davide.+ 29  Apanso Sauli anachita mantha kwambiri ndi Davide, moti anali kudana ndi Davide nthawi zonse.+ 30  Ndiyeno akalonga+ a Afilisiti akatuluka kudzamenya nkhondo, Davide anali kuchita zinthu mwanzeru kwambiri+ mwa atumiki onse a Sauli, moti dzina la Davide linatchuka kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”