1 Samueli 17:1-58

17  Ndiyeno Afilisiti+ anayamba kusonkhanitsa anthu a m’misasa yawo kuti akamenye nkhondo. Atasonkhana pamodzi ku Soko,+ m’dera la Yuda, anakamanga msasa pakati pa Soko ndi Azeka+ ku Efesi-damimu.+  Koma Sauli ndi amuna a Isiraeli anasonkhana pamodzi n’kumanga msasa m’chigwa cha Ela,+ ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi Afilisiti.  Afilisitiwo anaimirira paphiri kumbali ina, ndipo Aisiraeli anaimirira paphiri kumbali inanso. Pakati pawo panali chigwa.  Ndiyeno kumsasa wa Afilisiti kunatuluka ngwazi, dzina lake Goliyati,+ wa ku Gati.+ Iye anali wamtali mikono 6 ndi chikhatho chimodzi.*+  Anali atavala chisoti chamkuwa kumutu kwake ndi chovala chamamba achitsulo. Mkuwa wa chovala chamamba chimenecho+ unali wolemera masekeli* 5,000.  Mwamunayu anali atavalanso zoteteza miyendo zamkuwa ndipo anali atanyamula nthungo*+ yamkuwa kumsana kwake.  Mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu,+ ndipo mutu wachitsulo wa mkondowo unali wolemera masekeli 600. Munthu womunyamulira chishango chake chachikulu anali kuyenda patsogolo pake.  Choncho iye anaima n’kuyamba kufuulira asilikali a Isiraeli+ kuti: “N’chifukwa chiyani mukufola mwa dongosolo lomenyera nkhondo? Ine ndabwera kudzamenyera nkhondo Afilisiti. Inuyo ndinu antchito+ a Sauli. Ndiye sankhani munthu woti amenyane nane, ndipo abwere kuno.  Ngati angathe kumenyana nane n’kundipha, ndiye kuti tidzakhala antchito anu. Koma ngati ndingalimbane naye mpaka kumupha, inuyo mudzakhala antchito athu, ndipo muzititumikira.”+ 10  Ndiyeno Mfilisiti uja anapitiriza kunena kuti: “Ine ndikutonza+ asilikali a Isiraeli lero. Ndipatseni mwamuna woti ndimenyane naye!”+ 11  Sauli+ ndi Aisiraeli onse atamva mawu a Mfilisitiwa anaopsezedwa ndipo anachita mantha kwambiri.+ 12  Tsopano Davide anali mwana wamwamuna wa Jese, Mwefurata+ wina wa ku Betelehemu, ku Yuda. Jese anali ndi ana aamuna 8+ ndipo m’masiku a Sauli iye anali atakalamba kale. 13  Ndiyeno ana atatu aakulu a Jese anatsatira Sauli kunkhondo.+ Mayina a ana ake atatu amene anapita kunkhondowo anali Eliyabu,+ woyamba kubadwa, Abinadabu+ mwana wake wachiwiri, ndi Shama,+ wachitatu. 14  Davide anali wamng’ono kwambiri pa ana onse aamuna,+ ndipo ana atatu aakulu a Jese anatsatira Sauli. 15  Davide anali kupita kwa Sauli ndi kubwerera ku Betelehemu kukaweta nkhosa+ za bambo ake. 16  Kwa masiku 40, Mfilisiti uja anali kubwera m’mawa kwambiri ndi madzulo kudzadzionetsera. 17  Kenako Jese anauza Davide mwana wake kuti: “Tenga tirigu wokazinga+ uyu wokwana muyezo umodzi wa efa ndi mitanda ya mkate 10, upite nazo mofulumira kwa abale ako kumsasa. 18  Magawo 10 awa a mkaka* ukapatse mtsogoleri wa gulu la anthu 1,000.+ Ukafufuzenso kuti abale ako ali bwanji,+ ndipo akakupatse chizindikiro chosonyeza kuti ali bwino.” 19  Pa nthawiyi, Sauli, ana a Jese ndi amuna ena onse a Isiraeli anali m’chigwa cha Ela+ kuti amenyane ndi Afilisiti.+ 20  Choncho Davide anadzuka m’mawa kwambiri, atasiya nkhosa zake m’manja mwa wozisamalira. Iye ananyamula katundu wake ndi kunyamuka monga mmene Jese, bambo ake, anamuuzira.+ Atafika mkati mwa mpanda wa msasa,+ anapeza asilikali akupita kumalo omenyera nkhondo,+ akufuula mfuwu ya nkhondo. 21  Pamenepo asilikali a Isiraeli ndi asilikali a Afilisiti anafola kuti akumane. 22  Nthawi yomweyo, Davide anasiya katundu+ wake m’manja mwa munthu wosamalira katundu,+ ndipo anathamangira kumalo omenyera nkhondo. Atafika kumeneko, anayamba kufunsa za abale ake ngati ali bwino.+ 23  Pamene anali kulankhula ndi asilikaliwo, anangoona ngwazi ija yatulukira kuchokera pakati pa asilikali a Afilisiti. Dzina la ngwaziyo linali Goliyati,+ Mfilisiti wa ku Gati.+ Iye anayamba kulankhula mawu omwe aja amene analankhula poyamba,+ moti Davide anamva nawo. 24  Koma amuna onse a Isiraeli atangoona mwamunayu anayamba kuthawa, chifukwa anachita naye mantha kwambiri.+ 25  Pamenepo amuna a Isiraeli anayamba kunena kuti: “Mukumuona mwamuna amene akubwerayu? Iye akubwera kudzatonza+ Isiraeli. Munthu amene angamukanthe ndi kumupha, mfumu idzam’patsa chuma chochuluka ndi kum’patsanso mwana wake wamkazi.+ Komanso, mfumu idzamasula nyumba ya bambo ake a munthuyo kuti isamapereke chilichonse mwa zinthu zimene Aisiraeli ayenera kupereka kwa mfumu.”+ 26  Ndiyeno Davide anayamba kufunsa amuna amene anali ataimirira pafupi naye kuti: “Kodi munthu amene angakaphe Mfilisiti+ ameneyu ndi kuchotsa chitonzo pa Isiraeli+ amuchitira chiyani? Kodi Mfilisiti wosadulidwa+ ameneyu ndani kuti azinyoza+ asilikali a Mulungu wamoyo?”+ 27  Ndiyeno anthu anamuuzanso mawu amene anamuuza poyamba aja, kuti: “Munthu amene angaphe Mfilisiti ameneyu am’chitira zimenezi.” 28  Tsopano Eliyabu,+ m’bale wake wamkulu kwambiri wa Davide anamva zimene Davideyo anali kulankhula ndi amunawo. Eliyabu anapsa mtima kwambiri chifukwa cha Davide,+ moti anati: “N’chifukwa chiyani wabwera kuno? Nanga nkhosa zochepa za bambo wasiyira ndani kuchipululu?+ Ine ndikudziwa bwino kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako,+ chifukwa wabwera kuno kuti udzaonerere nkhondo.”+ 29  Poyankha Davide anati: “Tsopano ndachita chiyani? Inetu ndangofunsa chabe.”+ 30  Atatero, anatembenuka ndi kum’chokera kupita kwa munthu wina. Kwa munthu ameneyu anafunsanso funso lomwe lija,+ ndipo anthu anamuyankhanso chimodzimodzi ngati poyamba paja.+ 31  Anthu anamva zimene Davide ananena, ndipo anapita kukauza Sauli. Choncho Sauli anamuitanitsa. 32  Davide anauza Sauli kuti: “Musalole kuti aliyense agwidwe ndi mantha mumtima mwake.+ Ine mtumiki wanu ndipita kukamenyana ndi Mfilisiti ameneyu.”+ 33  Koma Sauli anauza Davide kuti: “Sungapite kukamenyana ndi Mfilisiti ameneyu,+ chifukwa ndiwe mwana,+ ndipo Mfilisiti ameneyu wakhala akumenya nkhondo kuyambira ubwana wake.” 34  Davide anauza Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala m’busa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango+ komanso chimbalangondo moti chilichonse mwa zilombo zimenezi chinagwira nkhosa ya m’gululo. 35  Pamenepo ine ndinatsatira chilombocho n’kuchipha,+ ndipo ndinapulumutsa nkhosa m’kamwa mwake. Chitayamba kundiukira, ndinagwira ndevu zake, n’kuchikantha ndi kuchipha. 36  Mtumiki wanu anapha zonse ziwiri, mkangowo ndi chimbalangondocho. Mfilisiti wosadulidwayu+ akhalanso ngati chimodzi mwa zilombo zimenezi, chifukwa watonza+ asilikali+ a Mulungu wamoyo.”+ 37  Ndiyeno Davide anawonjezera kuti: “Yehova amene anandilanditsa m’kamwa mwa mkango ndi m’kamwa mwa chimbalangondo andilanditsanso m’manja mwa Mfilisiti ameneyu.”+ Pamenepo Sauli anauza Davide kuti: “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.”+ 38  Tsopano Sauli anayamba kuveka Davide zovala zake. Anamuveka chisoti chamkuwa kumutu kwake, komanso chovala chamamba achitsulo. 39  Kenako Davide anamangirira lupanga pazovala zake. Pamene anafuna kunyamuka, iye analephera kuyenda chifukwa zovalazo sanazizolowere. Ndiyeno Davide anauza Sauli kuti: “Sinditha kuyenda nazo zovala zimenezi chifukwa sindinazizolowere.” Atatero, Davide anavula zovalazo.+ 40  Ndiyeno anatenga ndodo m’manja mwake ndi kusankha miyala isanu yosalala kwambiri ya m’chigwa.* Iye anaika miyalayi m’chikwama chake cha kubusa mmene anali kusungiramo zinthu, ndipo m’manja mwake munali gulaye.*+ Kenako anayamba kupita kumene kunali Mfilisiti uja. 41  Mfilisiti uja anayamba kupita kumene kunali Davide, ndipo anali kumuyandikirabe. Patsogolo pake panali munthu amene anali kumunyamulira chishango chake chachikulu. 42  Mfilisitiyo ataona Davide, anayamba kumuderera+ chifukwa anali mnyamata+ wamaonekedwe ofiirira,+ ndiponso wokongola.+ 43  Choncho iye anafunsa Davide kuti: “Kodi ine ndine galu+ kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Atatero, anatemberera Davide m’dzina la milungu yake.+ 44  Iye anapitiriza kuuza Davide kuti: “Tangoyerekeza kubwera kuno, ndipereka mnofu wako kwa mbalame zam’mlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire.”+ 45  Poyankha Davide anauza Mfilisitiyo kuti: “Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo,+ koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu,+ Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.+ 46  Lero Yehova akupereka m’manja mwanga,+ ndipo ndikupha ndi kukudula mutu. Lero ndipereka mitembo ya anthu a m’misasa ya Afilisiti kwa mbalame zam’mlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire.+ Anthu onse a padziko lapansi adzadziwa kuti Isiraeli ali ndi Mulungu.+ 47  Ndipo mpingo wonsewu udziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo,+ chifukwa Yehova ndiye mwini nkhondo,+ moti apereka anthu inu m’manja mwathu.”+ 48  Ndiyeno zinachitika kuti Mfilisiti uja anayamba kuyenda, kuyandikira Davide. Nayenso Davide anayamba kuyenda mofulumira ndi kuthamangira kumalo omenyera nkhondo kuti akakumane naye.+ 49  Pamenepo Davide anapisa dzanja m’chikwama chake ndi kutengamo mwala. Kenako anauponya ndi gulaye moti unamenya+ Mfilisiti uja pamphumi n’kuloweratu m’mutu mwake, ndipo anagwa pansi chafufumimba.+ 50  Choncho Davide, mwa kugwiritsa ntchito gulaye ndi mwala, anali wamphamvu kuposa Mfilisiti. Iye anamukantha ndi kumupha, ndipo m’manja mwa Davide munalibe lupanga.+ 51  Pamenepo Davide anapitiriza kuthamanga ndipo anakaima pambali pake. Kenako anatenga lupanga la Mfilisitiyo,+ kulisolola m’chimake ndi kum’pheratu mwa kum’dula mutu.+ Afilisiti ena onse ataona kuti ngwazi yawo yamphamvu ija yafa, anayamba kuthawa.+ 52  Zitatero, amuna a Isiraeli ndi Yuda anayamba kufuula ndi kuthamangitsa+ Afilisiti kukafika kuchigwa,+ mpaka kuzipata za mzinda wa Ekironi.+ Afilisiti amene anavulazidwa mosachiritsika anali kugwa m’njira yochokera ku Saaraimu,+ moti mitembo yawo inali paliponse mpaka kumizinda ya Gati ndi Ekironi. 53  Kenako ana a Isiraeli anasiya kuthamangitsa Afilisiti ndipo anabwerera n’kukafunkha+ zinthu za m’misasa yawo. 54  Kenako Davide anatenga mutu+ wa Mfilisiti uja ndi kupita nawo ku Yerusalemu, ndipo zida za Mfilisiti uja anaziika muhema wake.+ 55  Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisiti uja, anafunsa Abineri,+ mkulu wa asilikali, kuti: “Kodi ameneyu ndi mwana+ wa ndani,+ Abineri?” Poyankha Abineri anati: “Ndikulumbira pali moyo wanu mfumu, ine sindikudziwa ngakhale pang’ono!” 56  Choncho mfumuyo inati: “Ufufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa ndani.” 57  Chotero Davide atangofika kuchokera kumene anapha Mfilisiti, Abineri anam’tenga ndi kupita naye kwa Sauli, ali ndi mutu+ wa Mfilisiti uja m’manja mwake. 58  Ndiyeno Sauli anamufunsa kuti: “Mnyamata iwe, bambo wako ndani?” Poyankha Davide anati: “Ndine mwana wa mtumiki wanu Jese,+ wa ku Betelehemu.”+

Mawu a M'munsi

“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Choncho iye anali wamtali pafupifupi mamita atatu.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “mphumphu 10 za tchizi.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.