1 Samueli 15:1-35

15  Ndiyeno Samueli anauza Sauli kuti: “Yehova anatuma ine kudzakudzoza+ kukhala mfumu ya anthu ake Aisiraeli, choncho imva zimene Yehova wanena.+  Yehova wa makamu+ wanena kuti, ‘Ndibwezera+ Aamaleki chifukwa choukira Aisiraeli panjira, pamene Aisiraeliwo anali kutuluka mu Iguputo.+  Tsopano pita ukaphe Aamaleki+ ndi kuwawononga+ pamodzi ndi zonse zimene ali nazo. Usakawamvere chisoni, ukawaphe ndithu. Ukaphe+ mwamuna ndi mkazi, mwana wamng’ono ndi mwana woyamwa,+ ng’ombe ndi nkhosa, ngamila ndi bulu.’”+  Motero, Sauli anaitanitsa anthu ku Telayimu+ ndi kuwawerenga. Iye anapeza kuti panali amuna oyenda pansi 200,000 ndiponso amuna a ku Yuda 10,000.+  Kenako, Sauli anafika kumzinda wa Amaleki ndi kuubisalira kuchigwa.*  Zili choncho, Sauli anauza Akeni+ kuti: “Nyamukani,+ muchoke pakati pa Aamaleki kuti ndisakuwonongeni pamodzi nawo. Inuyo munasonyeza kukoma mtima kosatha kwa ana onse a Isiraeli+ atatuluka mu Iguputo.”+ Choncho Akeni anachokadi pakati pa Aamaleki.  Atachoka, Sauli anapha Aamaleki+ kuyambira ku Havila+ mpaka ku Shura,+ kufupi ndi Iguputo.  Iye anagwira Agagi+ mfumu ya Amaleki ali wamoyo, ndipo anthu ena onse anawapha ndi lupanga.+  Koma Sauli ndi anthu ake anamvera chisoni Agagi ndipo sanaphe nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambiri,+ ziweto zonenepa, nkhosa zamphongo ndi zina zonse zimene zinali zabwino. Iwo sanafune kupha zimenezi,+ koma anawononga zinthu zina zonse zimene zinali zonyansa ndi zonyozeka. 10  Ndiyeno Yehova anauza Samueli kuti: 11  “Ndikumva chisoni+ kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu. Iye watembenuka,+ wasiya kunditsatira, ndipo sakumvera mawu anga.”+ Samueli anavutika maganizo kwambiri ndi nkhani imeneyi+ moti anafuulira Yehova usiku wonse.+ 12  Kenako Samueli anadzuka m’mawa kwambiri kuti akaonane ndi Sauli. Koma uthenga unam’peza Samueli wonena kuti: “Sauli anabwera ku Karimeli,+ ndipotu waimika chipilala+ cha chikumbutso chake, kenako watembenuka ndipo wapita ku Giligala.” 13  Patapita nthawi Samueli anam’peza Sauli, ndipo Sauli anauza Samueli kuti: “Yehova akudalitseni.+ Ndachita zimene Yehova ananena.”+ 14  Koma Samueli anati: “Nanga kulira kwa nkhosa ndi ng’ombe kumene ndikumvaku kukutanthauza chiyani?”+ 15  Poyankha Sauli anati: “Anthuwa+ azitenga kwa Aamaleki, chifukwa sanaphe nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambirizi n’cholinga chofuna kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+ Koma zina zonse zotsala taziwononga.” 16  Pamenepo Samueli anauza Sauli kuti: “Khala chete! Ndikuuza zimene Yehova walankhula nane usiku wapitawu.”+ Sauli anayankha kuti: “Lankhulani!” 17  Ndiyeno Samueli anati: “Kodi sunali kudziona ngati ndiwe mwana+ utakhala mtsogoleri wa mafuko onse a Isiraeli, pamene Yehova anakudzoza+ kuti ukhale mfumu ya Isiraeli? 18  Kenako Yehova anakutuma kuti, ‘Pita ukaphe anthu ochimwa,+ Aamaleki, ndi kumenyana nawo kufikira utawafafaniza.’+ 19  Ndiye n’chifukwa chiyani sunamvere mawu a Yehova, koma unathamangira zofunkha mosusuka+ ndi kuyamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova?”+ 20  Sauli anayankha Samueli kuti: “Komatu ndamvera+ mawu a Yehova, chifukwa ndachita ntchito imene Yehova anandituma, ndipo ndabweretsa Agagi,+ mfumu ya Amaleki. Koma Aamalekiwo ndawapha.+ 21  Anthuwa+ atenga pa zofunkha, nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambiri, pa zinthu zimene zinayenera kuwonongedwa, kuti azipereke nsembe+ kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”+ 22  Poyankha Samueli anati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza+ ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera+ kuposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kuposa mafuta+ a nkhosa zamphongo. 23  Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+ 24  Pamenepo Sauli anayankha Samueli kuti: “Ndachimwa,+ ndaphwanya lamulo la Yehova komanso sindinamvere mawu anu, chifukwa ndinaopa anthu+ ndipo ndamvera mawu awo. 25  Tsopano ndikhululukireni+ tchimo langa chonde, ndipo mubwerere nane kuti ndikagwade ndi kuweramira pansi+ pamaso pa Yehova.” 26  Samueli anamuyankha kuti: “Sindibwerera nawe chifukwa wakana mawu a Yehova, ndipo Yehova wakukana kuti upitirize kukhala mfumu ya Isiraeli.”+ 27  Pamene Samueli anali kutembenuka kuti azipita, nthawi yomweyo Sauli anagwira m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Samueli, koma malayawo anang’ambika.+ 28  Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wang’amba+ ndi kuchotsa ufumu wa Isiraeli kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa mnzako, munthu woyenerera kuposa iwe.+ 29  Kuwonjezera apo, Wolemekezeka wa Isiraeli+ sadzalephera kukwaniritsa mawu ake,+ ndipo sadzadzimva kuti ali ndi mlandu, pakuti Iye si munthu kuti adzimve wamlandu.”+ 30  Pamenepo Sauli anati: “Ndachimwa. Komabe, ndilemekezeni+ chonde pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Isiraeli. Mubwerere nane ndipo ndidzagwada ndi kuweramira pansi pamaso pa Yehova Mulungu wanu.”+ 31  Choncho Samueli anabwerera akuyenda pambuyo pa Sauli. Ndipo Sauli anagwada ndi kuweramira pansi pamaso pa Yehova. 32  Kenako Samueli anati: “M’bweretseni kuno Agagi mfumu ya Amaleki.” Atatero, Agagi anapita kwa Samueli mwamantha ndi mokayikira.* Mumtima mwake Agagi anayamba kunena kuti: “Ndithudi, ululu wa imfa wachoka.” 33  Koma Samueli anati: “Monga mmene akazi anaferedwera ana awo chifukwa cha lupanga lako,+ momwemonso mayi ako+ aferedwa ana koposa akazi onse.”+ Pamenepo Samueli anadula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.+ 34  Tsopano Samueli ananyamuka kupita ku Rama, koma Sauli anapita kunyumba kwake ku Gibeya.+ 35  Samueli analirira+ Sauli ndipo sanaonanenso naye mpaka tsiku la imfa yake. Koma Yehova anamva chisoni kuti anaika Sauli kukhala mfumu ya Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mawu ake achiheberi angatanthauzenso “m’matangadza” kapena “mokondwera.”