1 Samueli 13:1-23

13  Sauli anali ndi zaka [?]* pamene anayamba kulamulira,+ ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri.  Ndiyeno Sauli anadzisankhira amuna 3,000 a mu Isiraeli. Amuna 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi+ ndi kudera lamapiri la Beteli. Amuna 1,000 anali ndi Yonatani+ ku Gibeya+ wa ku Benjamini, ndipo anthu ena onse otsalawo anawabweza kumahema awo.  Kenako Yonatani anakantha mudzi wa asilikali+ a Afilisiti+ umene unali ku Geba,+ ndipo Afilisiti anamva zimenezi. Zitatero Sauli analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ m’dziko lonse n’kunena kuti: “Imvani Aheberi inu!”  Isiraeli yense anamva anthu akukamba kuti: “Sauli wakantha mudzi wa asilikali a Afilisiti, ndipo tsopano Isiraeli wakhala chinthu chonunkha+ kwa Afilisiti.” Choncho anasonkhanitsa anthu onse pamodzi kuti atsatire Sauli ku Giligala.+  Afilisiti nawonso anasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi Isiraeli. Iwo anali ndi magaleta ankhondo 30,000,*+ asilikali okwera pamahatchi 6,000 ndi anthu ochuluka kwambiri ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Chotero anapita ku Mikimasi ndi kumanga misasa kum’mawa kwa Beti-aveni.+  Ndipo amuna a Isiraeli anaona kuti zinthu zawathina,+ chifukwa anthu onse anali atapanikizika. Anthuwo anapita kukabisala m’mapanga,+ m’maenje, kumatanthwe, m’zipinda za pansi ndi m’zitsime zopanda madzi.  Aheberi ena mpaka anawoloka Yorodano+ kupita m’dera la Gadi+ ndi la Giliyadi. Koma Sauli anali adakali ku Giligala, ndipo anthu onse anali kunjenjemera pamene anali kum’tsatira.+  Sauli anapitiriza kudikira kwa masiku 7 kufikira nthawi yoikidwiratu imene Samueli ananena.+ Koma Samueli sanafikebe ku Giligala, moti anthu anayamba kubalalika kum’siya Sauli.  Kenako Sauli anati: “Bweretsani kuno nsembe yopsereza ndi nsembe zachiyanjano.” Pamenepo iye anapereka nsembe yopserezayo.+ 10  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo anaona Samueli akubwera. Choncho Sauli anatuluka kukakumana naye ndi kumulonjera.+ 11  Kenako Samueli anati: “N’chiyani chimene wachita?”+ Poyankha Sauli anati: “Nditaona kuti anthu akubalalika kundisiya ndekha,+ ndipo inu simunabwere m’masiku amene munanena aja,+ komanso kuti Afilisiti anali kusonkhana pamodzi ku Mikimasi,+ 12  ndinaganiza+ kuti, ‘Tsopano Afilisitiwa abwera ku Giligala kuno kudzamenyana nane, ndipo sindinakhazike pansi mtima wa Yehova kuti atikomere mtima.’ Choncho ndakakamizika+ kupereka nsembe yopsereza.” 13  Pamenepo Samueli anauza Sauli kuti: “Wachita chinthu chopusa.+ Sunatsatire lamulo+ limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.+ Ukanatsatira lamulo limeneli, Yehova akanalimbitsa ufumu wako pa Isiraeli mpaka kalekale. 14  Tsopano ufumu wako sukhalitsa.+ Yehova apeza munthu wapamtima pake,+ ndipo Yehova amuika kukhala mtsogoleri+ wa anthu ake chifukwa iwe sunasunge zimene Yehova anakulamula.”+ 15  Kenako Samueli ananyamuka kuchoka ku Giligala kupita ku Gibeya wa ku Benjamini. Ndiyeno Sauli anayamba kuwerenga anthu amene anali nayebe limodzi, ndipo anapeza amuna pafupifupi 600.+ 16  Choncho Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi anthu amene anali nawo aja, anali kukhala ku Geba+ wa ku Benjamini. Koma Afilisiti anali atamanga msasa ku Mikimasi.+ 17  Anthu olanda katundu anali kutuluka mumsasa wa Afilisiti m’magulu atatu.+ Gulu loyamba linali kulowera kumsewu wopita ku Ofira,+ kudera la Suwali. 18  Gulu lachiwiri linali kulowera kumsewu wa ku Beti-horoni,+ ndipo gulu lachitatu linali kulowera kumsewu wopita kumalire oyang’anana ndi chigwa cha Zeboyimu, molunjika kuchipululu. 19  Ndipo m’dziko lonse la Isiraeli munalibe wosula zitsulo. Izi zinali choncho chifukwa Afilisiti anati: “Aheberi asasule lupanga kapena mkondo.”+ 20  Choncho Aisiraeli onse akafuna kunola pulawo, khasu, nkhwangwa kapena chikwakwa, aliyense wa iwo anali kupita kwa Afilisiti kuti amunolere.+ 21  Ndipo malipiro onoletsera mapulawo, makasu, mafoloko a mano atatu ndi nkhwangwa, ndiponso kukonza chisonga chotosera ng’ombe anali pimu* imodzi.+ 22  Ndiye zinali kuchitika kuti, pa tsiku lankhondo panalibe munthu aliyense mwa anthu amene anali ndi Sauli ndi Yonatani, amene anali ndi lupanga+ kapena mkondo m’manja mwake. Koma Sauli+ yekha ndi mwana wake Yonatani ndi amene anali ndi zida. 23  Tsopano gulu la asilikali+ a Afilisiti linali kutuluka mumsasa ndi kupita kumalo owolokera a ku Mikimasi.+

Mawu a M'munsi

M’Malemba achiheberi mulibe nambala yake.
Mipukutu ina ya Septuagint ndiponso Syriac Peshitta imati panali magaleta ankhondo “atatu.”
“Pimu” ndi muyezo wakale wolemera pafupifupi magalamu 8 a siliva.