1 Samueli 12:1-25

12  Pamapeto pake Samueli anauza Aisiraeli onse kuti: “Ndamva mawu anu onse amene munandiuza,+ kuti ndikuikireni mfumu yokulamulirani.+  Tsopano si iyi mfumu ikuyenda patsogolo panu!+ Koma ine, ndakalamba+ ndipo ndachita imvi.+ Ana anga aamuna, si awa ali pakati panu,+ ndipo ine ndatumikira Mulungu ndi kukutsogolerani kuyambira pa ubwana wanga, mpaka lero.+  Ine ndaima pamaso panu. Munditsutse pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa+ wake: Alipo kodi amene ndinam’tengerapo ng’ombe kapena bulu wake?+ Alipo kodi amene ndinam’chitirapo chinyengo, kapena kum’pondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisaone zimene anachita?+ Ndili wokonzeka kukubwezerani anthu inu.”+  Poyankha iwo anati: “Sunatichitire chinyengo, kutipondereza, kapena kulandira chilichonse kwa aliyense wa ife.”+  Atatero, iye anawayankha kuti: “Yehova ndi mboni yokutsutsani, ndipo wodzozedwa+ wake ndi mboni lero kuti simunandipeze ndi mlandu uliwonse.”+ Pamenepo iwo anati: “Inde, iyedi ndi mboni.”  Ndiyeno Samueli anauza anthuwo kuti: “Yehova ndiye mboni, iye amene anagwiritsa ntchito Mose ndi Aroni, amenenso anatulutsa makolo anu m’dziko la Iguputo.+  Tsopano imani pomwepa, kuti ndikuweruzeni pamaso pa Yehova ndi kukusimbirani ntchito zonse zolungama+ za Yehova, zimene wachitira inuyo ndi makolo anu.  “Yakobo atangofika mu Iguputo,+ makolo anu n’kuyamba kupempha thandizo+ kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose+ ndi Aroni kuti atsogolere makolo anu potuluka mu Iguputo, ndipo anawapatsa dziko lino kuti akhalemo.+  Atatero iwo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anawagulitsa+ kwa Sisera+ mkulu wa gulu lankhondo la Hazori, komanso kwa Afilisiti+ ndi kwa mfumu ya Mowabu,+ ndipo onsewa anapitiriza kumenyana nawo. 10  Choncho anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize,+ ndipo anati, ‘Tachimwa,+ pakuti tasiya Yehova kuti titumikire Abaala+ ndi zifaniziro za Asitoreti.+ Tsopano tilanditseni+ m’manja mwa adani athu, kuti tikutumikireni.’ 11  Pamenepo Yehova anatumiza Yerubaala,+ Bedani, Yefita+ ndi Samueli+ ndipo anakulanditsani m’manja mwa adani anu onse okuzungulirani, kuti mukhale popanda chokuopsani.+ 12  Mutaona kuti mfumu ya ana a Amoni, Nahasi,+ yabwera kudzamenyana nanu, munayamba kundiuza kuti, ‘Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira!’+ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mfumu yanu.+ 13  Tsopano mfumu imene mwasankha ndi imeneyi, mfumu imene mwapempha.+ Ndipotu Yehova wakuikiranidi mfumu+ yoti izikulamulirani. 14  Ngati mudzaopa Yehova,+ n’kumutumikiradi+ ndi kumvera mawu ake,+ ndipo ngati simudzapandukira+ malamulo a Yehova, Yehova Mulungu wanu adzakhala nanu, inuyo pamodzi ndi mfumu yokulamuliraniyo. 15  Koma ngati simudzamvera mawu a Yehova,+ moti n’kupandukiradi malamulo a Yehova,+ dzanja la Yehova lidzatsutsana ndi inu ndi abambo anu.+ 16  Tsopano, imani pomwepa kuti muonenso chinthu chachikuluchi chimene Yehova achite pamaso panu. 17  Kodi ino si nyengo yokolola tirigu?+ Ndifuulira+ Yehova kuti abweretse mabingu ndi mvula.+ Pamenepo mudziwa ndi kuona kuti choipa chimene mwachita pamaso pa Yehova n’chachikulu,+ pakuti mwapempha kuti mukhale ndi mfumu.” 18  Choncho Samueli anafuulira Yehova,+ moti Yehova anadzetsa mabingu ndi mvula tsiku limenelo.+ Pamenepo anthu onse anachita mantha kwambiri ndi Yehova ndiponso ndi Samueli. 19  Zitatero, anthu onse anayamba kuuza Samueli kuti: “Pempherera+ atumiki ako kwa Yehova Mulungu wako, chifukwa sitikufuna kufa. Pakuti tawonjeza choipa china pa machimo athu onse, mwa kupempha kuti tikhale ndi mfumu.” 20  Pamenepo Samueli anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Inuyo mwachita choipa chachikulu chimenechi. Ngakhale kuti zili choncho, musapatuke n’kusiya kutsatira Yehova,+ koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse.+ 21  Musapatuke kuti mutsatire milungu yopanda pake,+ yopanda phindu,+ imene singakulanditseni, pakuti ndi yopanda pake. 22  Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya+ anthu ake, pakuti Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+ 23  Komanso, n’zosatheka kuti ineyo ndichimwire Yehova mwa kusiya kukupemphererani.+ Ndipo ndiyenera kukulangizani+ za njira yabwino+ ndi yolondola. 24  Koma muziopa+ Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse m’choonadi.+ Kumbukirani zinthu zazikulu zimene Yehova wakuchitirani.+ 25  Koma mukachita zinthu zoipa mouma khosi, mudzasesedwa,+ inu pamodzi ndi mfumu yanuyo.”+

Mawu a M'munsi