1 Samueli 11:1-15

11  Ndiyeno Nahasi Muamoni+ anapita kukamanga msasa kuti amenyane ndi mzinda wa Yabesi+ ku Giliyadi. Zitatero, amuna onse a ku Yabesi anauza Nahasi kuti: “Chita nafe pangano kuti tizikutumikira.”+  Kenako Nahasi Muamoni ananena kuti: “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditaboola diso+ la kudzanja lamanja la aliyense wa inu, kuti chikhale chinthu chotonzetsa Aisiraeli onse.”+  Poyankha akulu a ku Yabesi anati: “Utipatse masiku 7 kuti titumize amithenga m’dziko lonse la Isiraeli, ndipo ngati sipapezeka wotipulumutsa,+ pamenepo tibwera kwa iwe.”  Mithengayo inafika ku Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, ndi kuuza anthu uthengawo. Anthu onse atamva uthengawo anayamba kulira mokweza mawu.+  Ndiyeno Sauli anatulukira kuchokera kutchire, akuyenda pambuyo pa ziweto. Kenako anati: “Kodi chachitika n’chiyani kuti anthuwa azilira?” Motero anayamba kum’fotokozera mawu a amuna a ku Yabesi.  Sauli atamva mawu amenewa mzimu+ wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo anapsa mtima kwambiri.+  Iye anatenga ng’ombe ziwiri zamphongo n’kuziduladula. Kenako anatumiza amithenga kukapereka zigawo za ng’ombezo m’dziko lonse la Isiraeli+ ndipo anati: “Aliyense amene satsatira Sauli ndi Samueli, izi n’zimene zichitikire ng’ombe zake.”+ Anthu atamva mawu amenewa anagwidwa ndi mantha+ ochokera kwa Yehova,+ moti onse anapita mogwirizana.+  Ndiye anatenga onsewo+ ndi kupita nawo ku Bezeki. Ana a Isiraeli analipo 300,000, ndipo amuna a ku Yuda analipo 30,000.  Tsopano iwo anauza amithenga amene anabwerawo kuti: “Anthu a ku Yabesi ku Giliyadi mukawauze kuti, ‘Mawa mulandira chipulumutso dzuwa litatentha.’”+ Pamenepo amithenga aja anafika ku Yabesi ndi kuuza anthu a kumeneko uthengawo moti anthuwo anasangalala kwambiri. 10  Choncho anthu a ku Yabesi anati: “Mawa tifika kwa inu, ndipo mutichitire chilichonse chimene chingakukomereni m’maso mwanu.”+ 11  Tsiku lotsatira, Sauli+ anagawa anthuwo m’magulu atatu.+ Amenewa analowa pakati pa msasawo pa ulonda wa m’mawa.*+ Atatero, anayamba kukantha Aamoni+ kufikira dzuwa litatentha. Otsala anawabalalitsa moti sipanatsale anthu awiri ali limodzi.+ 12  Tsopano anthuwo anayamba kuuza Samueli kuti: “Ndani akunena kuti, ‘Sauli sangakhale mfumu yathu?’+ Tipatseni anthu amenewo tiwaphe.”+ 13  Koma Sauli anayankha kuti: “Lero pasaphedwe munthu aliyense,+ chifukwa Yehova watipulumutsa mu Isiraeli.”+ 14  Kenako Samueli anauza anthuwo kuti: “Tiyeni tipite ku Giligala+ kuti tikachitenso mwambo wolonga mfumu.”+ 15  Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo analonga Sauli kukhala mfumu pamaso pa Yehova ku Giligalako. Kenako anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova+ kumeneko, ndipo Sauli pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli anali osangalala kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 14:24.