1 Samueli 10:1-27

10  Ndiyeno Samueli anatenga+ botolo ladothi la mafuta ndi kutsanulira mafutawo pamutu wa Sauli, n’kumupsompsona+ ndi kunena kuti: “Yehova wakudzoza iwe kukhala mtsogoleri+ wa cholowa chake.+  Lero ukasiyana ndi ine, ukumana ndi amuna awiri pafupi ndi manda a Rakele+ pa Zeliza, m’dera la Benjamini. Iwo akuuza kuti, ‘Abulu aakazi+ amene unapita kukafunafuna anapezeka, moti bambo ako sakuganiziranso za abulu aakaziwo koma ayamba kudera nkhawa za inuyo, moti akunena kuti: “Nditani ine pakuti mwana wanga sakuoneka?”’+  Kuchoka pamenepo upitirize ulendo wako mpaka kukafika kumtengo waukulu wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi amuna atatu akupita ku Beteli+ kukapembedza Mulungu woona. Mmodzi wa iwo akhala atanyamula ana atatu a mbuzi,+ wina atanyamula mitanda yobulungira itatu ya mkate,+ ndipo winayo atanyamula mtsuko waukulu wa vinyo.+  Amunawo akulonjera+ ndi kukupatsa mitanda iwiri ya mkate, ndipo uilandire.  Ukachoka pamenepo ufika kuphiri la Mulungu woona,+ kumene kuli mudzi wa asilikali+ a Afilisiti. Ndiyeno zimene zichitike n’zakuti, poyandikira mzindawo, ukumana ndi kagulu ka aneneri+ akuchokera kumalo okwezeka,+ akulankhula monga aneneri. Patsogolo pawo pakhala pali choimbira cha zingwe,+ maseche,+ chitoliro+ ndi zeze.+  Pamenepo mzimu+ wa Yehova uyamba kugwira ntchito pa iwe, moti iweyo uyamba kulankhula monga mneneri+ pamodzi ndi aneneriwo, ndiponso usinthika kukhala wina.  Ndiyeno zizindikiro+ zimenezi zikachitika pa iwe, uchite chilichonse chimene ungathe,+ chifukwa Mulungu woona ali ndi iwe.+  Choncho utsogole kupita ku Giligala.+ Inenso ndipita kumeneko kuti ndikapereke nsembe zopsereza ndi kupereka nsembe zachiyanjano.+ Ukandidikire masiku 7+ mpaka nditakupeza, ndipo ndikadzafika ndidzakuuza zoti uchite.”  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Sauli atangotembenuka kuti asiyane ndi Samueli, Mulungu anayamba kusintha mtima wake kukhala wina,+ moti zizindikiro+ zonsezi zinayamba kuchitikadi pa tsiku limenelo. 10  Chotero Sauli ndi mtumiki wake ananyamuka kupita kuphiri kuja, ndipo kumeneko anakumana ndi kagulu ka aneneri. Nthawi yomweyo, mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anayamba kulankhula ngati mneneri+ pakati pa aneneriwo. 11  Ndiyeno onse amene anali kumudziwa atamuona, anadabwa kuona kuti ali pakati pa aneneri ndipo akulankhula ngati mneneri. Choncho anthuwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi chachitikira mwana wa Kisi n’chiyani? Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+ 12  Mmodzi wa iwo poyankha anati: “Koma kodi bambo wawo ndani?” N’chifukwa chake pali mawu okuluwika+ akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?” 13  Patapita nthawi anamaliza kulankhula ngati mneneri, ndipo anafika kumalo okwezeka. 14  Kenako m’bale wa bambo ake a Sauli anafunsa Sauli pamodzi ndi mtumiki wake kuti: “Kodi munapita kuti?” Poyankha iye anati: “Tinapita kukafunafuna abulu aakazi,+ moti tinali kungoyendabe kuwafufuza, koma sitinawapeze. Choncho tinapita kwa Samueli.” 15  Pamenepo m’bale wa bambo ake a Sauli anati: “Ndiuzeni chonde, Kodi Samueli anakuuzani chiyani?” 16  Sauli anayankha m’bale wa bambo akeyo kuti: “Anatiuza mosaphonyetsa kuti abulu aakazi anali atapezeka.” Koma iye sananene za nkhani ya ufumu imene Samueli anamuuza.+ 17  Tsopano Samueli anasonkhanitsa anthu onse pamodzi pamaso pa Yehova ku Mizipa+ 18  ndi kuuza ana a Isiraeliwo kuti: “Mverani zimene Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena,+ ‘Ndine amene ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo,+ amenenso ndinakupulumutsani m’manja mwa Aiguputo ndi m’manja mwa maufumu onse amene anali kukuponderezani.+ 19  Koma inu, lero mwakana Mulungu wanu+ amene anakupulumutsani m’masautso anu onse ndi m’zowawa zanu, kufika ponena kuti: “Ife tikufuna kuti utiikire mfumu yoti izitilamulira.” Tsopano imani pamaso pa Yehova malinga ndi mafuko anu+ ndi mabanja anu.’”* 20  Chotero Samueli anabweretsa mafuko onse a Isiraeli pafupi,+ ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa.+ 21  Kenako anabweretsa pafupi fuko la Benjamini malinga ndi mabanja awo, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa.+ Pamapeto pake, Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa.+ Choncho anayamba kum’funafuna, koma sanam’peze. 22  Motero anafunsiranso+ kwa Yehova, kuti: “Kodi mwamunayu wafika kale pano?” Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Uyu wabisala+ pakati pa katunduyu.” 23  Choncho anthu anathamanga kukam’tenga kumeneko. Ataimirira pakati pa anthuwo, anali wam’tali kwambiri moti panalibe munthu aliyense amene anali kum’pitirira m’mapewa ake.+ 24  Ndiyeno Samueli anauza anthu onsewo kuti: “Kodi mwaona amene Yehova wam’sankha,+ kuti palibe aliyense pakati pa anthu onse wofanana naye?” Pamenepo anthu onsewo anayamba kufuula, kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+ 25  Zitatero, Samueli anauza anthuwo zinthu zimene mfumu iyenera kulandira kwa iwo+ ndipo anazilemba m’buku limene analiika pamaso pa Yehova. Kenako Samueli anauza anthuwo kuti aliyense abwerere kwawo. 26  Koma Sauli anapita kwawo ku Gibeya,+ ndipo amuna olimba mtima amene Mulungu anakhudza mitima yawo anapita naye pamodzi.+ 27  Koma anthu opanda pake+ anali kunena kuti: “Kodi ameneyu angatipulumutse bwanji?”+ Chotero anamunyoza,+ moti sanam’bweretsere mphatso iliyonse.+ Koma Sauli anangokhala chete.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mabanja anu” anganenedwenso kuti, “magulu anu a anthu 1,000.”