1 Samueli 1:1-28

1  Tsopano panali mwamuna wina wa ku Ramatayimu-zofimu,+ kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Elikana.+ Iye anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufi+ Mwefuraimu.*  Elikana anali ndi akazi awiri. Mkazi wina dzina lake anali Hana ndipo wina anali Penina. Penina anabereka ana koma Hana analibe ana.+  Chaka ndi chaka mwamuna ameneyu anali kutuluka mumzinda wake n’kupita ku Silo,+ kukagwada ndi kuweramira pansi+ pamaso pa Yehova wa makamu ndi kupereka nsembe zake. Kumeneko n’kumene ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ anali kutumikira monga ansembe a Yehova.+  Ndiyeno tsiku lina Elikana anali kupereka nsembe, ndipo anapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi,+  koma Hana anangom’patsa gawo limodzi. Komabe, iye anali kukonda kwambiri Hana+ ngakhale kuti Yehova anali atatseka mimba yake.+  Mkazi mnzake wa Hana anali kum’sautsa+ kwambiri n’cholinga choti amukhumudwitse, chifukwa chakuti Yehova anali atatseka mimba yake.  Chaka ndi chaka+ iye anali kuchita zimenezi nthawi zonse akapita kunyumba ya Yehova.+ Umu ndi mmene Penina anali kusautsira Hana, moti Hana anali kulira ndiponso sankadya.  Ndiyeno Elikana mwamuna wake anati: “Hana, n’chifukwa chiyani ukulira, ndipo n’chifukwa chiyani sukudya? Komanso n’chifukwa chiyani ukupwetekedwa mtima?+ Kodi sindine woposa ana aamuna 10 kwa iwe?”+  Pamenepo Hana anaimirira atadya ndi kumwa ku Silo. Apa n’kuti Eli wansembe atakhala pampando, pakhomo la kachisi+ wa Yehova. 10  Hana anali wokhumudwa kwabasi,+ ndipo anayamba kupemphera kwa Yehova+ ndi kulira kwambiri.+ 11  Iye anayamba kulonjeza+ kuti: “Inu Yehova wa makamu, mukaona nsautso yanga, ine kapolo wanu wamkazi,+ ndi kundikumbukira,+ ndiponso ngati simudzaiwala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo lezala silidzadutsa m’mutu mwake.”+ 12  Pamene anali kupemphera choncho kwa Yehova kwa nthawi yaitali,+ Eli anali kuyang’anitsitsa pakamwa pake. 13  Koma Hana anali kulankhula mumtima mwake.+ Milomo yake inali kugwedera koma sanali kutulutsa mawu. Eli ataona zimenezo anaganiza kuti waledzera.+ 14  Choncho Eli anamuuza kuti: “Kodi ukhala woledzera mpaka liti?+ Pita kaye, kuledzera kwakoku kuyambe kwatha.” 15  Pamenepo Hana anayankha kuti: “Ayi mbuyanga! Ine ndine mkazi wopsinjika maganizo. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa ayi, koma ndikufotokoza nkhawa zanga zonse kwa Yehova.+ 16  Musachititse kapolo wanu wamkazi kukhala ngati mkazi wopanda pake,+ popeza ndikulankhulabe mpaka pano chifukwa cha kuchuluka kwa nkhawa ndi nsautso.”+ 17  Pamenepo Eli anamuyankha kuti: “Pita mu mtendere,+ ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wam’pempha.”+ 18  Poyankha anati: “Pitirizani kundikomera mtima ine kapolo wanu.”+ Ndiyeno mkaziyo anachoka ndi kupita kukadya,+ ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.+ 19  Kenako anadzuka m’mawa kwambiri n’kugwada ndi kuwerama mpaka nkhope zawo pansi pamaso pa Yehova. Atatero anabwerera kunyumba kwawo ku Rama.+ Ndiyeno Elikana anagona+ ndi mkazi wake Hana, ndipo Yehova anayamba kum’kumbukira.+ 20  Pamene chaka chinkatha, Hana anatenga pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna n’kumutcha dzina lake+ Samueli,* chifukwa anati, “ndinam’pempha+ kwa Yehova.” 21  Patapita nthawi, mwamunayu Elikana anapita pamodzi ndi banja lake lonse kukapereka kwa Yehova nsembe ya pachaka+ ndi nsembe yake yalonjezo.+ 22  Koma Hana sanapite nawo,+ pakuti anali atauza mwamuna wake kuti: “Mwanayu akangosiya kuyamwa,+ ndiyenera kupita naye kuti akaonekere pamaso pa Yehova ndi kukhala kumeneko mpaka kalekale.”*+ 23  Pamenepo Elikana mwamuna wake+ anamuuza kuti: “Chita zimene ukuona kuti n’zabwino kwa iwe.+ Ukhale pakhomo kufikira mwanayo atasiya kuyamwa, ndipo Yehova akwaniritse mawu ake.”+ Choncho mkaziyo anakhalabe pakhomo ndipo anapitiriza kulera mwana wake kufikira atasiya kuyamwa.+ 24  Mwanayo atangosiya kuyamwa, Hana anapita naye ku Silo atatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo yazaka zitatu, ufa wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi mtsuko waukulu wa vinyo.+ Iye analowa m’nyumba ya Yehova ku Silo,+ ndipo mwanayo anali naye limodzi. 25  Kenako anapha ng’ombe yaing’ono yamphongoyo ndipo anabweretsa mwana wake wamwamunayo kwa Eli.+ 26  Pamenepo Hana anati: “Pepani mbuyanga! Pali moyo wanu+ mbuyanga, ine ndine mkazi amene ndinaima ndi inu pamalo ano n’kupemphera kwa Yehova.+ 27  Ndinali kupemphera kuti Yehova andipatse mwana uyu, kuti andipatse+ chimene ndinam’pempha.+ 28  Ndipo ine ndikum’pereka* kwa Yehova.+ Ndam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.” Pamenepo iye* anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa Yehova.+

Mawu a M'munsi

Akutchedwa Mwefuraimu chifukwa anali kukhala kudera la Efuraimu, koma kwenikweni Elikana anali Mlevi. Onani 1Mb 6:19, 22-28.
Onani mawu a mmunsi pa Mutu wa buku lino.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Chiheberi, “kubwereketsa.”
Ameneyu ndi Elikana. Onani 1Sa 2:11.