1 Mbiri 9:1-44

9  Aisiraeli onse analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo+ m’Buku la Mafumu a Isiraeli. Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo+ ku Babulo chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.  Oyamba kubwerera n’kukakhala ku cholowa chawo m’mizinda yawo anali Aisiraeli,+ ansembe,+ Alevi,+ ndi Anetini.+  Ku Yerusalemu+ kunkakhala ana ena a Yuda,+ Benjamini,+ Efuraimu ndi Manase.  Pa anawo panali Utai mwana wa Amihudi. Amihudi anali mwana wa Omuri, Omuri anali mwana wa Imiri, ndipo Imiri anali mwana wa Bani. Amenewa anali mbadwa za Perezi+ mwana wa Yuda.+  Pa anthu otchedwa Asilo,+ panali Asaya woyamba kubadwa ndiponso ana ake.  Pa ana a Zera+ panali Yeweli. Panalinso abale ake a Zera okwana 690.  Pa ana a Benjamini panali Salelu mwana wa Mesulamu. Mesulamu anali mwana wa Hodaviya, ndipo Hodaviya anali mwana wa Hasenuwa.  Panalinso Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi. Uzi anali mwana wa Mikiri. Panalinso Mesulamu mwana wa Sefatiya. Sefatiya anali mwana wa Reueli, ndipo Reueli anali mwana wa Ibiniya.  Abale awo potsatira mibadwo yawo analipo 956. Onsewa anali amuna amene anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo. 10  Pa ansembe panali Yedaya, Yehoyaribu, Yakini,+ 11  ndi Azariya+ mwana wa Hilikiya. Hilikiya anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Merayoti, ndipo Merayoti anali mwana wa Ahitubu. Ahitubu anali mtsogoleri wa nyumba ya Mulungu woona. 12  Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu. Yerohamu anali mwana wa Pasuri, ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya. Komanso panali Maasai mwana wa Adieli. Adieli anali mwana wa Yahazera, Yahazera anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Mesilemiti,+ ndipo Mesilemiti anali mwana wa Imeri. 13  Panalinso abale awo. Onse anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, ndipo analipo 1,760. Iwo anali amuna amphamvu, omwe anali kugwira ntchito+ yotumikira panyumba ya Mulungu woona. 14  Pa Alevi panali Semaya mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu, ndipo Azirikamu anali mwana wa Hasabiya.+ Amenewa anali ochokera kwa ana a Merari. 15  Panalinso Bakabakara, Heresi, Galali, ndi Mataniya+ mwana wa Mika.+ Mika anali mwana wa Zikiri,+ ndipo Zikiri anali mwana wa Asafu.+ 16  Komanso panali Obadiya mwana wa Semaya.+ Semaya anali mwana wa Galali, Galali anali mwana wa Yedutuni.+ Ndiye panalinso Berekiya mwana wa Asa mwana wa Elikana, amene anali kukhala m’midzi ya Anetofa.+ 17  Alonda a pazipata+ anali Salumu,+ Akubu, Talimoni, ndi Ahimani. Salumu m’bale wawo ndiye anali mtsogoleri. 18  Kufikira nthawi imeneyo, iye anali kukhala pachipata cha mfumu+ kum’mawa. Amenewa anali alonda a pazipata za misasa ya ana a Levi.+ 19  Panalinso Salumu mwana wa Kore. Kore anali mwana wa Ebiasafu+ ndipo Ebiasafu anali mwana+ wa Kora.+ Salumu ndi abale ake a nyumba ya makolo ake, Akora,+ anali oyang’anira ntchito pochita utumiki wawo pamodzi ndi makolo awo, monga alonda+ a pachihema pamsasa wa Yehova. Iwo anali alonda a pachipata. 20  Pinihasi+ mwana wa Eleazara+ ndiye anali mtsogoleri wawo kalekale, ndipo Yehova anali naye.+ 21  Zekariya+ mwana wa Meselemiya anali mlonda wa pachipata cholowera kuchihema chokumanako. 22  Onse amene anasankhidwa kuti akhale alonda a pamakomo analipo 212. Iwo anakhala m’midzi yawo+ mogwirizana ndi mndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.+ Davide+ ndi Samueli wamasomphenya+ anaika amenewa pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo.+ 23  Iwo ndi ana awo anali kuyang’anira zipata za nyumba ya Yehova, kapena kuti chihema chopatulika,* ndipo ankachita utumiki waulonda.+ 24  Alonda a pazipatawo anali kukhala mbali zonse zinayi, kum’mawa,+ kumadzulo,+ kumpoto,+ ndi kum’mwera.+ 25  Abale awo amene anali kukhala m’midzi yawo, ankabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito limodzi nawo kwa masiku 7.+ 26  Pa alonda a pazipatawo panali amuna anayi amphamvu amene anali pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Amunawo anali Alevi, ndipo anali kuyang’anira zipinda zodyera+ ndi chuma+ cha m’nyumba ya Mulungu woona. 27  Usiku anali kukhala mozungulira nyumba yonse ya Mulungu woona chifukwa anali pa utumiki wawo waulonda.+ Iwo ndiwo anali kusunga kiyi kuti azitsegula zipata m’mawa uliwonse.+ 28  Ena a iwo anali oyang’anira ziwiya+ za utumiki, chifukwa anali kuziwerenga pozitulutsa ndi pozilowetsa. 29  Ena a iwo anali amuna osankhidwa kuti aziyang’anira ziwiya zina, ziwiya zonse zopatulika,+ ufa wosalala,+ vinyo,+ mafuta,+ lubani,*+ ndi mafuta a basamu.+ 30  Ena mwa ana a ansembe anali opanga mafuta onunkhira+ osakaniza ndi mafuta a basamu. 31  Matitiya Mlevi, yemwe anali mwana woyamba wa Salumu+ Mkora, anali ndi udindo woyang’anira zinthu zophikidwa m’ziwaya,+ umene anapatsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwake. 32  Ena mwa ana a Akohati, abale awo, anali oyang’anira mikate yosanjikiza,+ kuti aziikonza sabata ndi sabata.+ 33  Amenewa ndiwo anali oimba,+ atsogoleri a makolo a Alevi m’zipinda zodyera.+ Iwo sanali kupatsidwa ntchito zina+ chifukwa usana ndi usiku anali ndi udindo wogwira ntchito yawo.+ 34  Amenewa anali atsogoleri a Alevi potsata mibadwo yawo. Iwo ndi amene anali kukhala ku Yerusalemu.+ 35  Yeyeli bambo wa Gibeoni+ anali kukhala ku Gibeoni, ndipo dzina la mkazi wake linali Maaka. 36  Mwana wake woyamba anali Abidoni. Anaberekanso Zuri, Kisi, Baala, Nera, Nadabu, 37  Gedori, Ahiyo, Zekariya,+ ndi Mikiloti. 38  Mikiloti anabereka Simeamu. Amenewa ndi amene anali kukhala ku Yerusalemu pamodzi ndi abale awo ena, moyang’anizana ndi abale awo. 39  Nera+ anabereka Kisi,+ Kisi anabereka Sauli,+ Sauli anabereka Yonatani,+ Malikisuwa,+ Abinadabu,+ ndi Esibaala.+ 40  Mwana wa Yonatani anali Meribi-baala,+ ndipo Meribi-baala anabereka Mika.+ 41  Ana a Mika anali Pitoni, Meleki, Tareya, ndi Ahazi.+ 42  Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti, ndi Zimiri. Zimiri anabereka Moza. 43  Moza anabereka Bineya, Bineya anabereka Refaya,+ Refaya anabereka Eleasa, ndipo Eleasa anabereka Azeli. 44  Azeli anali ndi ana 6. Mayina awo anali Azirikamu, Bokeru, Isimaeli, Seariya, Obadiya, ndi Hanani. Amenewa anali ana a Azeli.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “nyumba ya chihema.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.