1 Mbiri 8:1-40

8  Benjamini+ anabereka Bela+ mwana wake woyamba, wachiwiri anali Asibeli,+ wachitatu anali Ahara,+  wachinayi anali Noha,+ ndipo wachisanu anali Rafa.  Ana a Bela anali Adara, Gera,+ Abihudi,  Abisuwa, Namani, Ahowa,  Gera, Sefufani,+ ndi Huramu.+  Panalinso ana a Ehudi amene anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Geba.+ Iwowa anagwira anthu ndi kuwatengera ku Manahati.  Atsogoleriwo anali Namani, Ahiya, ndi Gera. Gera ndiye anatengera anthuwo ku ukapolo, ndipo iye anabereka Uziza ndi Ahihudi.  Saharaimu anabereka ana m’dziko+ la Mowabu atathamangitsako Amowabu. Akazi ake anali Husimu ndi Baara.  Kwa Hodesi mkazi wake, anabereka Yobabi, Zibia, Mesa, Malikamu, 10  Yeuzi, Sakiya, ndi Mirima. Amenewa anali ana ake, atsogoleri a nyumba za makolo awo. 11  Kwa Husimu anabereka Abitubu ndi Elipaala. 12  Ana a Elipaala anali Ebere, Misamu, ndi Semedi. Semedi ndiye anamanga mzinda wa Ono+ ndiponso mzinda wa Lodi,+ ndi midzi yake yozungulira. 13  Elipaala anaberekanso Beriya ndi Sema. Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Aijaloni.+ Iwo ndiwo anathamangitsa anthu a ku Gati. 14  Panalinso Ahiyo, Sasaki, Yeremoti, 15  Zebadiya, Aradi, Ederi, 16  Mikayeli, Isipa, ndi Yoha. Amenewa anali ana a Beriya.+ 17  Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Hiberi, 18  Isimerai, Iziliya, ndi Yobabi anali ana a Elipaala. 19  Yakimu, Zikiri, Zabidi, 20  Elianai, Ziletai, Elieli, 21  Adaya, Beraya, ndi Simirati, anali ana a Simeyi.+ 22  Isipani, Ebere, Elieli, 23  Abidoni, Zikiri, Hanani, 24  Hananiya, Elamu, Antotiya, 25  Ifideya, ndi Penueli, anali ana a Sasaki. 26  Samuserai, Sehariya, Ataliya, 27  Yaaresiya, Eliya, ndi Zikiri, anali ana a Yerohamu. 28  Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo motsatira mzere wa mabanja awo. Iwowa ndi amene anali kukhala ku Yerusalemu.+ 29  Yeyeli bambo wa Gibeoni+ anali kukhala ku Gibeoni, ndipo dzina la mkazi wake linali Maaka.+ 30  Mwana wake woyamba anali Abidoni. Anaberekanso Zuri, Kisi, Baala, Nadabu,+ 31  Gedori, Ahiyo, ndi Zekeri.+ 32  Mikiloti anabereka Simeya.+ Amenewa ndiwo anali kukhala ku Yerusalemu pamodzi ndi abale awo ena, moyang’anizana ndi abale awo. 33  Nera+ anabereka Kisi,+ Kisi anabereka Sauli,+ Sauli anabereka Yonatani,+ Malikisuwa,+ Abinadabu,+ ndi Esibaala.+ 34  Mwana wa Yonatani anali Meribi-baala,+ ndipo Meribi-baala anabereka Mika.+ 35  Ana a Mika anali Pitoni, Meleki, Tarea,+ ndi Ahazi. 36  Ahazi anabereka Yehoada. Yehoada anabereka Alemeti, Azimaveti, ndi Zimiri. Zimiri anabereka Moza. 37  Moza anabereka Bineya, Bineya anabereka Rafa,+ Rafa anabereka Eleasa, ndipo Eleasa anabereka Azeli. 38  Azeli anali ndi ana 6. Mayina awo anali, Azirikamu, Bokeru, Isimaeli, Seariya, Obadiya, ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli. 39  Ana a m’bale wake Ezeki anali awa: woyamba Ulamu, wachiwiri Yeusi, wachitatu Elifeleti. 40  Ana a Ulamu anali amuna amphamvu ndi olimba mtima,+ amuna odziwa kupinda uta.+ Iwo anali ndi ana ambiri+ ndiponso zidzukulu zambiri. Onse analipo 150. Onsewa anali ana a Benjamini.

Mawu a M'munsi