1 Mbiri 7:1-40

7  Ana a Isakara analipo anayi: Tola,+ Puwa,+ Yasubi, ndi Simironi.+  Ana a Tola anali Uzi, Refaya, Yerieli, Yahamai, Ibisamu, ndi Semuyeli. Amenewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo. Pa mbadwa za Tola panali amuna amphamvu ndi olimba mtima. M’masiku a Davide,+ amunawa analipo 22,600.  Mwana wa Uzi anali Izirahiya. Ana a Izirahiya anali Mikayeli, Obadiya, Yoweli, Isiya, ndi [?]* Anawo analipo asanu ndipo onsewa anali atsogoleri a mabanja awo.  Pa mibadwo ya amenewa, motsatira nyumba ya makolo awo, panali asilikali 36,000, chifukwa anali ndi akazi ndi ana ambiri.+  Abale awo a mabanja onse a Isakara, anali amuna amphamvu ndi olimba mtima+ okwana 87,000 pamndandanda wa mayina awo onse wotsatira makolo awo.+  Ana a Benjamini+ analipo atatu: Bela,+ Bekeri,+ ndi Yediyaeli.+  Ana a Bela+ analipo asanu: Eziboni, Uzi, Uziyeli, Yerimoti, ndi Iri. Iwo anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, amuna amphamvu ndi olimba mtima, ndipo pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo,+ analipo 22,034.  Ana a Bekeri anali Zemira, Yowasi, Eliezere, Elioenai, Omuri, Yeremoti, Abiya, Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri.  Pamndandanda wa mayina a atsogoleri a nyumba ya makolo awo, malinga ndi mibadwo yawo,+ panali amuna amphamvu ndi olimba mtima okwanira 20,200. 10  Mwana wa Yediyaeli+ anali Bilihani. Ana a Bilihani anali Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisi, ndi Ahisahara. 11  Onsewa anali ana a Yediyaeli, atsogoleri a nyumba ya makolo awo. Anali amuna 17,200, amuna amphamvu ndi olimba mtima,+ opita ku nkhondo. 12  Mabanja a Supimu+ ndi Hupimu+ anali mbadwa za Iro,+ ndipo ana a Husimu anali mbadwa za Aheri. 13  Ana a Nafitali+ anali Yazieli,+ Guni,+ Yezera, ndi Salumu,+ ana a Biliha.+ 14  Mwana wa Manase+ yemwe mdzakazi wake wachisiriya anam’berekera, anali Asiriyeli. (Mdzakaziyo anabereka Makiri,+ bambo wa Giliyadi. 15  Makiri anapezera akazi Hupimu ndi Supimu, ndipo dzina la mlongo wake linali Maaka.) Mwana wake wachiwiri dzina lake linali Tselofekadi,+ koma Tselofekadi anali ndi ana aakazi okhaokha.+ 16  Patapita nthawi, Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina loti Peresi. M’bale wake wa Peresi dzina lake linali Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rekemu. 17  Mwana wa Ulamu anali Bedani. Amenewa anali ana a Giliyadi. Giliyadi anali mwana wa Makiri, ndipo Makiri anali mwana wa Manase. 18  Mlongo wake wa Giliyadi anali Hamoleketi. Iye anabereka Isihodi, Abi-ezeri,+ ndi Mala. 19  Ana a Semida anali Ahiyani, Sekemu, Liki, ndi Aniamu. 20  Mwana wa Efuraimu+ anali Sutela.+ Sutela anabereka Beredi, Beredi anabereka Tahati, Tahati anabereka Eleada, Eleada anabereka Tahati, 21  Tahati anabereka Zabadi, ndipo Zabadi anabereka Sutela. Efuraimu anaberekanso Ezeri ndi Eleadi. Iwo anaphedwa ndi amuna a ku Gati+ amene anabadwira m’dzikolo, chifukwa anabwera kudzalanda ziweto zawo. 22  Bambo wawo Efuraimu anawalira kwa masiku ambiri,+ ndipo abale ake ankabwera kudzam’tonthoza. 23  Kenako Efuraimu anagona ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo anatenga pakati+ n’kubereka mwana wamwamuna. Koma Efuraimu anatcha mwanayo dzina lakuti Beriya,* chifukwa mkaziyo anabereka pa nthawi imene tsoka+ linagwera nyumba ya Efuraimu. 24  Mwana wake wamkazi anali Seera, ndipo iye anamanga mzinda wa Beti-horoni,+ wakumunsi+ ndi wakumtunda.+ Anamanganso mzinda wa Uzeni-seera. 25  Efuraimu anabereka Refa ndi Resefe.* Resefe anabereka Tela, Tela anabereka Tahani, 26  Tahani anabereka Ladani, Ladani anabereka Amihudi, Amihudi anabereka Elisama, 27  Elisama anabereka Nuni,+ ndipo Nuni anabereka Yehoswa.*+ 28  Cholowa chawo ndiponso malo awo okhala anali Beteli+ ndi midzi yake yozungulira. Kum’mawa kunali Naarani,+ kumadzulo kunali Gezeri+ ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Sekemu+ ndi midzi yake yozungulira, mpaka kukafika ku Gaza ndi midzi yake yozungulira. 29  Pafupi ndi ana a Manase panali Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, Megido+ ndi midzi yake yozungulira, ndiponso Dori+ ndi midzi yake yozungulira. Ana a Yosefe+ mwana wa Isiraeli ankakhala m’mizinda imeneyi. 30  Ana a Aseri+ anali Imuna,+ Isiva, Isivi,+ ndi Beriya,+ ndipo mlongo wawo anali Sera. 31  Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli, yemwe anali bambo wa Birizaiti. 32  Hiberi anabereka Yafuleti, Someri,* Hotamu, ndi Sua mlongo wawo. 33  Ana a Yafuleti anali Pasaki, Bimali, ndi Asivati. Amenewa anali ana a Yafuleti. 34  Ana a Semeri anali Ahi, Roga, Yehuba, ndi Aramu. 35  Ana a m’bale wake Helemu anali Zofa, Imina, Selesi, ndi Amali. 36  Ana a Zofa anali Suya, Harineferi, Suwali, Beri, Imura, 37  Bezeri, Hodi, Samima, Silisa, Itirani, ndi Beera. 38  Ana a Yeteri anali Yefune, Pisipa, ndi Era. 39  Ana a Ula anali Ara, Hanieli, ndi Riziya. 40  Onsewa anali ana a Aseri, atsogoleri+ a nyumba ya makolo awo, amuna ochita kusankhidwa, amphamvu ndi olimba mtima.+ Iwo anali akuluakulu a atsogoleri, ndipo mndandanda wa mayina awo+ anaugwiritsa ntchito powalemba usilikali, pokonzekera nkhondo. Analipo amuna 26,000.+

Mawu a M'munsi

M’Malemba achiheberi mulibe dzina lake.
Kutanthauza, “Ndi Tsoka.”
N’kutheka kuti “Refa” ndi “Resefe” anali ana a Beriya.
Kapena kuti “Yoswa.”
Pavesi 34 akutchedwa Semeri.