1 Mbiri 6:1-81

6  Ana a Levi+ anali Gerisoni,+ Kohati,+ ndi Merari.+  Ana a Kohati anali Amuramu,+ Izara,+ Heburoni,+ ndi Uziyeli.+  Ana a Amuramu+ anali Aroni,+ Mose,+ ndi Miriamu.+ Ana a Aroni anali Nadabu,+ Abihu,+ Eleazara,+ ndi Itamara.+  Eleazara+ anabereka Pinihasi,+ Pinihasi anabereka Abisuwa,+  Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi,+  Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti,+  Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu,+  Ahitubu anabereka Zadoki,+ Zadoki anabereka Ahimazi,+  Ahimazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani, 10  ndipo Yohanani anabereka Azariya.+ Iye ndiye anali wansembe m’nyumba imene Solomo anamanga ku Yerusalemu. 11  Azariya anabereka Amariya,+ Amariya anabereka Ahitubu,+ 12  Ahitubu anabereka Zadoki, Zadoki+ anabereka Salumu, 13  Salumu anabereka Hilikiya,+ Hilikiya anabereka Azariya, 14  Azariya anabereka Seraya,+ ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.+ 15  Yehozadaki ndiye anapita ku ukapolo pamene Yehova anatengera Yuda ndi Yerusalemu ku ukapolo kudzera mwa Nebukadinezara. 16  Ana a Levi+ anali Gerisomu, Kohati, ndi Merari. 17  Ana a Gerisomu mayina awo anali Libini+ ndi Simeyi.+ 18  Ana a Kohati+ anali Amuramu,+ Izara, Heburoni, ndi Uziyeli.+ 19  Ana a Merari anali Mali ndi Musi.+ Mabanja a Alevi potsatira mayina a makolo awo ndi awa:+ 20  Mwana wa Gerisomu anali Libini,+ mwana wa Libini anali Yahati, mwana wa Yahati anali Zima, 21  mwana wa Zima anali Yowa,+ mwana wa Yowa anali Ido, mwana wa Ido anali Zera, ndipo mwana wa Zera anali Yeaterai. 22  Mwana wa Kohati anali Aminadabu, mwana wa Aminadabu anali Kora,+ ana a Kora anali Asiri, 23  Elikana, ndi Ebiasafu.+ Mwana wa Ebiasafu anali Asiri, 24  mwana wa Asiri anali Tahati, mwana wa Tahati anali Uriyeli, mwana wa Uriyeli anali Uziya, ndipo mwana wa Uziya anali Shauli. 25  Ana a Elikana+ anali Amasai ndi Ahimoti. 26  Mwana wa Elikana anali Zofai,+ mwana wa Zofai anali Nahati, 27  mwana wa Nahati anali Eliyabu,+ mwana wa Eliyabu anali Yerohamu, ndipo mwana wa Yerohamu anali Elikana.+ 28  Ana a Samueli+ anali awa: woyamba Yoweli, wachiwiri Abiya.+ 29  Mwana wa Merari anali Mali,+ mwana wa Mali anali Libini, mwana wa Libini anali Simeyi, mwana wa Simeyi anali Uza, 30  mwana wa Uza anali Simeya, mwana wa Simeya anali Hagiya, mwana wa Hagiya anali Asaya. 31  Nawa anthu amene Davide+ anawapatsa udindo wotsogolera kuimba panyumba ya Yehova ataikapo Likasa.+ 32  Anthuwa anali ndi udindo+ woyang’anira oimba+ pachihema chopatulika kapena kuti chihema chokumanako, mpaka pamene Solomo anamanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.+ Iwo anapitiriza kutumikira malinga ndi ntchito yawo.+ 33  Awa ndiwo anali kutumikira, komanso ana awo: Pa ana a Akohati, Hemani+ woimba, mwana wa Yoweli.+ Yoweli anali mwana wa Samueli,+ 34  Samueli anali mwana wa Elikana,+ Elikana anali mwana wa Yerohamu, Yerohamu anali mwana wa Elieli,+ Elieli anali mwana wa Towa, 35  Towa anali mwana wa Zufi,+ Zufi anali mwana wa Elikana, Elikana anali mwana wa Mahati, Mahati anali mwana wa Amasai, 36  Amasai anali mwana wa Elikana, Elikana anali mwana wa Yoweli, Yoweli anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Zefaniya, 37  Zefaniya anali mwana wa Tahati, Tahati anali mwana wa Asiri, Asiri anali mwana wa Ebiasafu,+ Ebiasafu anali mwana wa Kora,+ 38  Kora anali mwana wa Izara,+ Izara anali mwana wa Kohati, Kohati anali mwana wa Levi, Levi anali mwana wa Isiraeli. 39  M’bale wake Asafu+ anali kutumikira mbali ya kumanja kwake. Asafu anali mwana wa Berekiya,+ Berekiya anali mwana wa Simeya, 40  Simeya anali mwana wa Mikayeli, Mikayeli anali mwana wa Baaseya, Baaseya anali mwana wa Malikiya, 41  Malikiya anali mwana wa Etini, Etini anali mwana wa Zera, Zera anali mwana wa Adaya, 42  Adaya anali mwana wa Etani, Etani anali mwana wa Zima, Zima anali mwana wa Simeyi, 43  Simeyi anali mwana wa Yahati,+ Yahati anali mwana wa Gerisomu,+ Gerisomu anali mwana wa Levi. 44  Pa ana a Merari,+ abale awo amene anali kumanzere kwawo, panali Etani+ mwana wa Kisa.+ Kisa anali mwana wa Abidi, Abidi anali mwana wa Maluki, 45  Maluki anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Amaziya, Amaziya anali mwana wa Hilikiya, 46  Hilikiya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Bani, Bani anali mwana wa Semeri, 47  Semeri anali mwana wa Mali, Mali anali mwana wa Musi,+ Musi anali mwana wa Merari,+ Merari anali mwana wa Levi. 48  Abale awo Alevi+ ndiwo anapatsidwa utumiki wonse+ wa pachihema chopatulika, chimene chili nyumba ya Mulungu woona. 49  Aroni+ ndi ana ake anali kufukiza nsembe yautsi+ paguwa lansembe zopsereza+ ndi paguwa lansembe zofukiza+ kuti akwaniritse ntchito zonse zokhudzana ndi zinthu zopatulika kwambiri, ndiponso kuti aphimbe machimo+ a Aisiraeli,+ malinga ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu woona analamula. 50  Tsopano awa ndiwo ana a Aroni:+ Aroni anabereka Eleazara,+ Eleazara anabereka Pinihasi,+ Pinihasi anabereka Abisuwa,+ 51  Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi, Uzi anabereka Zerahiya,+ 52  Zerahiya anabereka Merayoti,+ Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu,+ 53  Ahitubu anabereka Zadoki,+ ndipo Zadoki anabereka Ahimazi.+ 54  Otsatirawa ndiwo malo amene ankakhala ana a Aroni a m’banja la Akohati,+ m’misasa yawo yokhala ndi mipanda m’madera awo,+ chifukwa maere anagwera iwowo: 55  anapatsidwa mzinda wa Heburoni+ m’dziko la Yuda, ndi malo ake odyetserako ziweto kuzungulira mzinda wonsewo. 56  Malo ozungulira mzindawo ndi midzi yake,+ anawapereka kwa Kalebe+ mwana wa Yefune.+ 57  Ana a Aroni anawapatsa mzinda* wothawirako+ wa Heburoni,+ mzinda wa Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Yatiri,+ mzinda wa Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 58  mzinda wa Hileni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 59  mzinda wa Asani+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Beti-semesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 60  Kuchokera ku fuko la Benjamini, anawapatsa mzinda wa Geba+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Alemeti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Mizinda yonse ya mabanja awo inalipo 13.+ 61  Ana a Kohati amene anatsala anawapatsa mizinda yochokera ku banja la fuko lina ndi hafu ya fuko la Manase, atachita maere. Anawapatsa mizinda 10.+ 62  Ana a Gerisomu+ potsata mabanja awo anapatsidwa mizinda kuchokera ku fuko la Isakara,+ fuko la Aseri,+ fuko la Nafitali,+ ndi fuko la Manase+ ku Basana. Anapatsidwa mizinda 13. 63  Ana a Merari+ potsata mabanja awo anapatsidwa mizinda kuchokera ku fuko la Rubeni,+ fuko la Gadi,+ ndi fuko la Zebuloni.+ Anapatsidwa mizinda 12 atachita maere. 64  Chotero ana a Isiraeli anapatsa Alevi+ mizindayo ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 65  Komanso, atachita maere anawapatsa mizinda imeneyi kuchokera ku fuko la ana a Yuda,+ fuko la ana a Simiyoni,+ ndi fuko la ana a Benjamini.+ Mizindayo anachita kuitchula mayina. 66  Mabanja ena a ana a Kohati anapatsidwa mizinda m’dera lawo kuchokera ku fuko la Efuraimu.+ 67  Chotero anawapatsa mzinda wothawirako wa Sekemu+ ndi malo ake odyetserako ziweto m’dera lamapiri la Efuraimu, mzinda wa Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 68  mzinda wa Yokimeamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 69  mzinda wa Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Gati-rimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 70  Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anapatsa mabanja a ana a Kohati amene anatsala,+ mzinda wa Aneri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Bileamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 71  Kuchokera ku banja la hafu ya fuko la Manase, anapatsa ana a Gerisomu+ mzinda wa Golani+ ku Basana ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Asitaroti+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 72  Kuchokera ku fuko la Isakara, anawapatsa mzinda wa Kedesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 73  mzinda wa Ramoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Anemu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 74  Kuchokera ku fuko la Aseri anawapatsa mzinda wa Masala ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Abidoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 75  mzinda wa Hukoki+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 76  Kuchokera ku fuko la Nafitali+ anawapatsa mzinda wa Kedesi+ ku Galileya+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Hamoni ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Kiriyataimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 77  Kuchokera ku fuko la Zebuloni,+ anapatsa ana a Merari amene anatsala, mzinda wa Rimono+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Tabori ndi malo ake odyetserako ziweto. 78  Kuchokera ku fuko la Rubeni,+ anawapatsa mzinda wa Bezeri+ m’chipululu ndi malo ake odyetserako ziweto. Mzindawo unali m’chigawo cha Yorodano pafupi ndi Yeriko chakum’mawa kwa Yorodano. Anawapatsanso mzinda wa Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 79  mzinda wa Kademoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Mefaata+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 80  Kuchokera ku fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 81  mzinda wa Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mizinda.”