1 Mbiri 5:1-26

5  Mwana woyamba wa Isiraeli anali Rubeni.+ Iye anali woyamba kubadwa+ koma chifukwa chakuti anaipitsa bedi la bambo wake,+ udindo wake monga woyamba kubadwa unaperekedwa kwa ana a Yosefe,+ mwana wa Isiraeli. Choncho iye sanalembedwe monga woyamba kubadwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo.  Chifukwa chakuti Yuda+ anali wamphamvu pakati pa abale ake, mwa iye munachokera mtsogoleri,+ koma udindo wa woyamba kubadwa unali wa Yosefe.+  Ana a Rubeni mwana woyamba wa Isiraeli, anali: Hanoki,+ Palu,+ Hezironi, ndi Karami.+  Mwana wa Yoweli anali Semaya. Semaya anabereka Gogi, Gogi anabereka Simeyi,  Simeyi anabereka Mika, Mika anabereka Reyaya, Reyaya anabereka Baala,  Baala anabereka Beeraha yemwe Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri inam’tenga kupita naye ku ukapolo. Iye anali mtsogoleri wa Arubeni.  Abale ake potsata mabanja awo pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo,+ anali Yeyeli yemwe anali mtsogoleri, Zekariya,  ndi Bela. Bela anali mwana wa Azazi, Azazi anali mwana wa Sema, Sema anali mwana wa Yoweli.+ Bela anali kukhala m’dera loyambira ku Aroweli+ mpaka kukafika ku Nebo+ ndi ku Baala-meoni.+  Dera lake linakafika mpaka kum’mawa pamalo olowera m’chipululu pamtsinje wa Firate,+ chifukwa ziweto zawo zinachuluka kwambiri m’dziko la Giliyadi.+ 10  M’masiku a Sauli, iwo anachita nkhondo ndi Ahagara+ n’kuwagonjetsa. Kenako anayamba kukhala m’mahema awo m’dera lonse lakum’mawa kwa Giliyadi. 11  Ana a Gadi+ omwe anali pafupi nawo, anali kukhala m’dziko la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12  Mtsogoleri wawo anali Yoweli, wachiwiri wake anali Safamu. Panalinso Yanai ndi Safati ku Basana. 13  Abale awo a nyumba ya makolo awo analipo 7 ndipo amenewo anali Mikayeli, Mesulamu, Sheba, Yorai, Yakani, Ziya, ndi Ebere. 14  Amenewa anali ana a Abihaili. Abihaili anali mwana wa Huri, Huri anali mwana wa Yarowa, Yarowa anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Mikayeli, Mikayeli anali mwana wa Yesisai, Yesisai anali mwana wa Yado, Yado anali mwana wa Buza. 15  Panalinso Ahi mwana wa Abidieli, mwana wa Guni, yemwe anali mtsogoleri wa nyumba ya makolo awo. 16  Iwo anapitiriza kukhala ku Giliyadi,+ ku Basana,+ ndi m’midzi yake yozungulira+ komanso m’malo onse odyetsera ziweto a ku Sharoni, mpaka kumapeto kwa malo amenewa. 17  Onsewa analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo, m’masiku a Yotamu+ mfumu ya Yuda ndi m’masiku a Yerobowamu*+ mfumu ya Isiraeli. 18  Ana a Rubeni, Agadi, ndi hafu ya fuko la Manase amene anali amuna amphamvu,+ onyamula chishango ndi lupanga, odziwa kupinda uta, ndi odziwa kumenya nkhondo, analipo asilikali 44,760.+ 19  Iwo anayamba kumenyana ndi Ahagara,+ Yeturi,+ Nafisi,+ ndi Nodabu. 20  Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+ 21  Iwo analanda ziweto zawo.+ Analanda ngamila 50,000, nkhosa 250,000, abulu 2,000, ndipo anatenganso anthu 100,000.+ 22  Amene anafa analipo ambiri chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu woona.+ Iwo anapitiriza kukhala m’malo a anthuwo kufikira nthawi imene anatengedwa kupita kudziko lina.+ 23  Ana a hafu ya fuko la Manase+ anakhala m’dera loyambira ku Basana+ mpaka ku Baala-herimoni,+ ku Seniri,+ ndi kuphiri la Herimoni,+ ndipo iwo anachulukana kwambiri. 24  Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo awo: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya, ndi Yahadieli. Onsewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, amuna amphamvu, olimba mtima, ndiponso otchuka. 25  Iwo anayamba kuchita zinthu zosakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo, ndipo anayamba kuchita chiwerewere+ ndi milungu+ ya anthu a m’dzikolo, amene Mulungu anawachotsa pamaso pawo. 26  Choncho, Mulungu wa Isiraeli analimbikitsa mtima+ wa Puli+ mfumu ya Asuri,+ ndithu analimbikitsa mtima wa Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri, moti anatenga+ Arubeni, Agadi, ndi hafu ya fuko la Manase n’kuwapititsa ku Hala,+ ku Habori, ku Hara, ndi kumtsinje wa Gozani, ndipo akukhalabe kumeneko mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, Yerobowamu Wachiwiri.