1 Mbiri 3:1-24

3  Ana amene Davide+ anabereka ku Heburoni+ anali awa: woyamba Aminoni,+ wobadwa kwa Ahinowamu+ wa ku Yezereeli,+ wachiwiri Danieli, wobadwa kwa Abigayeli+ wa ku Karimeli,+  wachitatu Abisalomu,+ wobadwa kwa Maaka+ mwana wamkazi wa Talimai+ mfumu ya Gesuri,+ wachinayi Adoniya,+ wobadwa kwa Hagiti,+  wachisanu Sefatiya, wobadwa kwa Abitali,+ wa 6 Itireamu, wobadwa kwa Egila+ mkazi wake.  Davide anabereka ana 6 ku Heburoni ndipo analamulira kumeneko zaka 7 ndi miyezi 6. Kenako analamulira zaka 33 ku Yerusalemu.+  Ku Yerusalemu+ iye anabereka ana awa: Simeya,+ Sobabu,+ Natani,+ ndi Solomo,+ ana anayi obadwa kwa Bati-seba+ mwana wamkazi wa Amiyeli.+  Anaberekanso Ibara,+ Elisama,+ Elifeleti,+  Noga, Nefegi, Yafiya,+  Elisama,+ Eliyada, ndi Elifeleti,+ ana 9.  Amenewa ndiwo anali ana onse a Davide, kuwonjezera pa ana a adzakazi ake, ndipo Tamara+ anali mlongo wawo. 10  Mwana wa Solomo anali Rehobowamu.+ Rehobowamu anabereka Abiya,+ Abiya anabereka Asa,+ Asa anabereka Yehosafati,+ 11  Yehosafati anabereka Yehoramu,+ Yehoramu anabereka Ahaziya,+ Ahaziya anabereka Yehoasi,+ 12  Yehoasi anabereka Amaziya,+ Amaziya anabereka Azariya,+ Azariya anabereka Yotamu,+ 13  Yotamu anabereka Ahazi,+ Ahazi anabereka Hezekiya,+ Hezekiya anabereka Manase,+ 14  Manase anabereka Amoni,+ ndipo Amoni anabereka Yosiya.+ 15  Ana a Yosiya anali awa: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu,+ wachitatu Zedekiya,+ ndipo wachinayi anali Salumu. 16  Mwana wa Yehoyakimu anali Yekoniya.+ Yekoniya anabereka Zedekiya. 17  Ana amene Yekoniya anabereka ali mkaidi anali Salatiyeli,+ 18  Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama, ndi Nedabiya. 19  Ana a Pedaya anali Zerubabele+ ndi Simeyi. Ana a Zerubabele anali Mesulamu ndi Hananiya, (Selomiti anali mlongo wawo), 20  Hasuba, Oheli, Berekiya, Hasadiya, ndi Yusabi-hesedi, ana asanu. 21  Ana a Hananiya anali Pelatiya+ ndi Yesaiya, mwana wa Yesaiya anali Refaya, mwana wa Refaya anali Arinani, mwana wa Arinani anali Obadiya, mwana wa Obadiya anali Sekaniya, 22  mwana wa Sekaniya anali Semaya, ndipo ana a Semaya anali Hatusi, Igali, Bariya, Neariya, ndi Safati, ana 6. 23  Ana a Neariya anali Elioenai, Hizikiya, ndi Azirikamu, ana atatu. 24  Ana a Elioenai anali Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya, ndi Anani, ana 7.

Mawu a M'munsi