1 Mbiri 29:1-30

29  Tsopano mfumu Davide inauza mpingo wonse+ kuti: “Solomo mwana wanga, amene Mulungu wamusankha,+ ndi wamng’ono+ ndi wosakhwima. Koma ntchitoyi ndi yaikulu chifukwa chinyumba chachikuluchi, si cha munthu ayi,+ koma ndi cha Yehova Mulungu.  Ine ndakonzekera nyumba ya Mulungu wanga ndi mphamvu zanga zonse.+ Ndakonzekera+ golide+ wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa, zitsulo+ zopangira zinthu zachitsulo, ndi matabwa+ opangira zinthu zamatabwa. Ndakonzekeranso miyala ya onekisi,+ miyala yomanga ndi simenti yolimba, miyala yokongoletsera, miyala yamitundumitundu yamtengo wapatali, ndi miyala yambirimbiri ya alabasitala.  Chifukwa chakuti ndikusangalala+ ndi nyumba ya Mulungu wanga, ndili ndi chuma chapadera+ chomwe ndi golide ndi siliva. Ndikupereka chuma chimenechi kunyumba ya Mulungu wanga kuwonjezera pa zonse zimene ndakonzera nyumba yopatulikayo.+  Chumacho chili motere: Matalente* 3,000 a golide wa ku Ofiri,+ matalente 7,000 a siliva woyengedwa bwino wokutira makoma a nyumbazo,  golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, ndi siliva woti amisiri adzagwirire ntchito zonse. Ndani lero ali wokonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?”+  Pamenepo, akalonga+ a nyumba za makolo,+ akalonga+ a mafuko a Aisiraeli, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ ndi a magulu a anthu 100,+ ndiponso atsogoleri oyang’anira ntchito+ za mfumu, anayamba kupereka zinthu mwa kufuna kwawo.  Chotero iwo anapereka golide wokwanira matalente 5,000, madariki* 10,000, siliva wokwanira matalente 10,000, mkuwa wokwanira matalente 18,000, ndi zitsulo zokwanira matalente 100,000.+ Anapereka zonsezi kuti zigwire ntchito panyumba ya Mulungu woona.  Miyala iliyonse yamtengo wapatali imene munthu aliyense anali nayo, anaipereka ku chuma cha panyumba ya Yehova, chomwe Yehiela+ Mgerisoni+ anali kuyang’anira.  Anthuwo anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, pakuti anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.+ Nayonso mfumu Davide inasangalala kwambiri.+ 10  Kenako Davide anatamanda+ Yehova pamaso pa mpingo wonse,+ kuti: “Mudalitsike+ inu Yehova Mulungu wa Isiraeli+ atate wathu, kuyambira kalekale mpaka kalekale. 11  Inu Yehova, ukulu,+ mphamvu,+ kukongola,+ ulemerero,+ ndi ulemu+ ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu.+ Ufumu+ ndi wanu, inu Yehova, ndinunso Wokwezeka monga mutu pa onse.+ 12  Chuma+ ndi ulemerero+ zimachokera kwa inu. Inu mumalamulira+ chilichonse. M’dzanja lanu muli mphamvu+ ndi nyonga,+ ndipo dzanja lanu limatha kukweza+ ndiponso kupereka mphamvu kwa onse.+ 13  Tsopano inu Mulungu wathu, tikukuyamikani+ ndi kutamanda+ dzina lanu lokongola.+ 14  “Ndine ndani ine,+ ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupereka nsembe zaufulu ngati zimenezi?+ Pakuti chilichonse n’chochokera kwa inu,+ ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu. 15  Ifetu ndife alendo pamaso panu, komanso okhala m’dziko la eni+ monga analili makolo athu onse. Masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi,+ ndipo ndife osakhalitsa. 16  Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zochuluka zonsezi zimene takonzekera kuti tikumangireni nyumba, nyumba ya dzina lanu loyera, zachokera m’dzanja lanu ndipo zonse ndi zanu.+ 17  Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti inu ndinu wosanthula mitima,+ ndiponso kuti mumakonda chilungamo.+ Ineyo kumbali yanga, ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu ndi mtima wowongoka. Ndasangalala kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwaufulu kwa inu. 18  Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli makolo athu,+ thandizani anthu awa kuti apitirizebe kukhala ndi mtima wodzipereka woterewu,+ ndiponso kuti akutumikireni ndi mtima wawo wonse.+ 19  Mupatse Solomo mwana wanga mtima wathunthu+ kuti asunge malamulo anu,+ maumboni* anu,+ ndi kuti achite zonse. Ndiponso kuti amange chinyumba chachikulu+ chimene ndakonzeratu zipangizo zake.”+ 20  Kenako Davide anauza mpingo wonse kuti:+ “Tsopano tamandani+ Yehova Mulungu wanu!” Choncho mpingo wonse unayamba kutamanda Yehova Mulungu wa makolo awo, ndipo anagwada+ n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ kwa Yehova ndi kwa mfumu. 21  Anthuwo anayamba kupereka nsembe+ kwa Yehova, ndipo anali kupereka nsembe zopsereza+ kwa Yehova mpaka tsiku lotsatira. Anapereka ng’ombe zamphongo zazing’ono 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ana a nkhosa amphongo 1,000, ndi nsembe zake zachakumwa.+ Iwo anapereka nsembe zambirimbiri za Isiraeli yense.+ 22  Pa tsiku limenelo, iwo anadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Yehova.+ Kachiwirinso, analonga Solomo mwana wa Davide kukhala mfumu,+ ndi kum’dzoza pamaso pa Yehova kukhala mtsogoleri.+ Anadzozanso Zadoki+ kukhala wansembe. 23  Chotero, Solomo anayamba kukhala pampando wachifumu wa Yehova+ monga mfumu m’malo mwa Davide bambo wake, ndipo ankalamulira bwino.+ Aisiraeli onse anali kumumvera. 24  Akalonga onse+ ndi amuna amphamvu,+ ndiponso ana onse a Mfumu Davide,+ anali kugonjera Solomo mfumu. 25  Yehova anapitiriza kukweza Solomo+ pamaso pa Aisiraeli onse, ndi kum’patsa ulemu waukulu wachifumu kuposa mfumu ina iliyonse imene inalamulira Isiraeli iye asanakhale mfumu.+ 26  Kunena za Davide mwana wa Jese, iye analamulira Isiraeli yense.+ 27  Masiku onse amene iye analamulira Isiraeli anakwana zaka 40.+ Ku Heburoni analamulira zaka 7,+ ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.+ 28  Pamapeto pake, iye anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali,+ wokhutira ndi masiku, chuma+ ndi ulemerero.+ Kenako Solomo mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 29  Nkhani zokhudza Davide mfumu, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa pakati pa mawu a Samueli wamasomphenya,*+ Natani+ mneneri, ndiponso pakati pa mawu a Gadi+ wamasomphenya. 30  Nkhanizo zinalembedwa pamodzi ndi nkhani zonse zokhudza ufumu wake, zochita zake zamphamvu, ndi zinthu+ zimene zinachitika kwa iye, kwa Isiraeli, ndi kwa maufumu onse a m’mayiko osiyanasiyana.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
“Dariki” ndi ndalama yagolide yachiperisiya. Onani Zakumapeto 12.
Kapena kuti “zikumbutso.”
Zikuoneka kuti wamasomphenya anali munthu amene Mulungu ankamuchititsa kuti azitha kudziwa chifuniro cha Mulunguyo.