1 Mbiri 25:1-31

25  Ndipo Davide ndi atsogoleri+ a magulu a anthu otumikira,+ anapatula ena mwa ana a Asafu, a Hemani,+ ndi a Yedutuni,+ kuti azitumikira. Amuna atatuwa anali kulosera ndi azeze,+ zoimbira za zingwe,+ ndi zinganga.+ Mwa ana awo anatengamo amuna ena n’kuwaika pa udindo kuti azitumikira.  Pa ana a Asafu, anatengapo Zakuri, Yosefe,+ Netaniya, ndi Asarela.+ Ana ake amenewa anali kuyang’aniridwa ndi Asafuyo,+ amenenso anali mneneri wa mfumu.  Kwa Yedutuni,+ anatengako ana ake awa: Gedaliya,+ Zeri,+ Yesaiya,+ Simeyi, Hasabiya, ndi Matitiya,+ ana 6. Iwowa anali kuyang’aniridwa ndi Yedutuni bambo wawo, amene anali kulosera ndi zeze poyamika ndi potamanda Yehova.+  Kwa Hemani,+ anatengako ana ake awa: Bukiya,+ Mataniya,+ Uziyeli,+ Sebueli, Yerimoti, Hananiya,+ Haneni, Eliyata,+ Gidaliti,+ Romamiti-ezeri,+ Yosebekasa,+ Maloti,+ Hotiri,+ ndi Mahazioti.  Onsewa anali ana a Hemani, wamasomphenya+ wa mfumu pa zinthu za Mulungu woona komanso wokweza nyanga* yake pofuna kutamanda Mulungu. Choncho Mulungu woona anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.+  Ana onsewa anali kuyang’aniridwa ndi bambo awo poimba nyimbo m’nyumba ya Yehova. Ankaimba nyimbozo ndi zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze,+ pochita utumiki wa panyumba ya Mulungu woona. Koma Asafu, Yedutuni, ndi Hemani anali kuyang’aniridwa ndi mfumu.+  Chiwerengero chawo, pamodzi ndi abale awo ophunzitsidwa kuimbira Yehova,+ onse akatswiri,+ chinakwana 288.  Kenako anachita maere+ powagawira ntchito yoti azichita. Pochita maerewo, onse anali chimodzimodzi. Sanali kuyang’ana kuti uyu ndi wamng’ono kapena wamkulu,+ katswiri+ kapena wophunzira kumene.  Zotsatira za maerewo zinali motere: Maere oyamba anagwera Yosefe+ mwana wa Asafu, achiwiri anagwera Gedaliya+ (iye ndi abale ake ndi ana ake analipo 12), 10  achitatu anagwera Zakuri,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 11  achinayi anagwera Iziri,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 12  achisanu anagwera Netaniya,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 13  a 6 anagwera Bukiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 14  a 7 anagwera Yesarela,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 15  a 8 anagwera Yesaiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 16  a 9 anagwera Mataniya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 17  a 10 anagwera Simeyi, ana ake ndi abale ake analipo 12, 18  a 11 anagwera Azareli,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 19  a 12 anagwera Hasabiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 20  a 13 anagwera Subaeli,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 21  a 14 anagwera Matitiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 22  a 15 anagwera Yeremoti, ana ake ndi abale ake analipo 12, 23  a 16 anagwera Hananiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 24  a 17 anagwera Yosebekasa, ana ake ndi abale ake analipo 12, 25  a 18 anagwera Haneni, ana ake ndi abale ake analipo 12, 26  a 19 anagwera Maloti, ana ake ndi abale ake analipo 12, 27  a 20 anagwera Eliyata, ana ake ndi abale ake analipo 12, 28  a 21 anagwera Hotiri, ana ake ndi abale ake analipo 12, 29  a 22 anagwera Gidaliti, ana ake ndi abale ake analipo 12, 30  a 23 anagwera Mahazioti,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 31  ndipo maere a 24 anagwera Romamiti-ezeri,+ ana ake ndi abale ake analipo 12.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.