1 Mbiri 22:1-19

22  Tsopano Davide anati: “Malo ano ndiwo nyumba+ ya Yehova Mulungu woona, ndipo guwa lansembe+ ili ndi la nsembe zopsereza za Isiraeli.”  Atatero, Davide analamula kuti asonkhanitse alendo+ okhala m’dziko la Isiraeli. Alendowo anawaika kukhala osema miyala,+ kuti azisema miyala yofanana mbali zonse,+ yomangira nyumba ya Mulungu woona.  Ndiyeno Davide anasonkhanitsa zitsulo zambirimbiri zopangira misomali ya zitseko za pazipata komanso zopangira zida zopanira zinthu. Anasonkhanitsanso mkuwa wambirimbiri wosatheka kuuyeza kulemera kwake.+  Iye anasonkhanitsanso matabwa osawerengeka a mkungudza,+ popeza Asidoni+ ndi anthu a ku Turo+ anali atabweretsera Davide matabwa ambirimbiri a mkungudza.  Kenako Davide anati: “Mwana wanga Solomo ndi wamng’ono komanso wosakhwima,+ koma nyumba yoti adzamangire Yehova idzakhala yokongola,+ yaulemerero wosaneneka+ ndiponso yotchuka ndi yotamandika kumayiko onse. Ndiyetu ndim’konzere zipangizo zoti adzagwiritsire ntchito.” Chotero Davide asanafe, anasonkhanitsa zipangizo zambirimbiri pokonzekera ntchitoyo.+  Kuwonjezera pamenepo, anaitana mwana wake Solomo kuti amuuze za ntchito yomanga nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.  Ndipo Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Ineyo, ndinafunitsitsa ndi mtima wanga wonse+ kumanga nyumba ya dzina+ la Yehova Mulungu wanga.  Koma mawu a Yehova ananditsutsa, kuti: ‘Iweyo wakhetsa magazi ambirimbiri+ ndipo wamenya nkhondo zikuluzikulu.+ Sungamange nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wakhetsa magazi ambirimbiri pamaso panga padziko lapansi.  Taona, udzabala mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wabata, ndipo ndidzam’patsa mpumulo pakati pa adani ake onse omuzungulira.+ N’chifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo,*+ ndipo m’masiku ake ndidzakhazikitsa mtendere+ ndi bata pa Isiraeli. 10  Iyeyo ndi amene adzamanga nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana+ wanga, ndipo ine ndidzakhala atate wake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu+ pa Isiraeli ndipo sudzagwedezeka mpaka kalekale.’ 11  “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendere bwino kuti umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga mmene iye analankhulira za iwe.+ 12  Yehova akupatse nzeru ndi kuzindikira.+ Akupatsenso lamulo lotsogolera Isiraeli, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.+ 13  Zinthu zidzakuyendera bwino+ ukayesetsa kutsatira malamulo+ ndi zigamulo+ zimene Yehova analamula+ Mose zokhudza Isiraeli. Khala wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+ Usaope+ kapena kuchita mantha.+ 14  Taona, pa nthawi ya masautso anga+ ndasonkhanitsa golide womangira nyumba ya Yehova wokwanira matalente* 100,000,+ ndi siliva wokwanira matalente 1,000,000. Koma n’zosatheka kuyeza kulemera kwa mkuwa+ ndi zitsulo+ chifukwa n’zochuluka kwambiri. Ndakonzanso matabwa ndi miyala, koma udzawonjezerapo zina. 15  Palinso antchito ambirimbiri, osema miyala,+ amisiri a miyala ndi a matabwa, ndiponso anthu onse odziwa ntchito zosiyanasiyana.+ 16  Golide, siliva, mkuwa, ndi zitsulo n’zosatheka kuziwerenga.+ Yamba kugwira ntchito imeneyi,+ ndipo Yehova akhale nawe.”+ 17  Zitatha izi, Davide analamula akalonga onse a Isiraeli kuti athandize mwana wake Solomo. Iye anati: 18  “Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu?+ Kodi sanakupatseni mpumulo m’dziko lonseli?+ Pakuti iye wapereka m’manja mwanga anthu a m’dzikoli, ndipo dzikoli lagonjetsedwa pamaso pa Yehova+ ndi pa anthu ake. 19  Choncho funafunani Yehova Mulungu wanu+ ndi mtima wanu ndi moyo wanu.+ Yambani kumanga nyumba yopatulika+ ya Yehova Mulungu woona.+ Kenako mukatenge likasa+ la pangano la Yehova ndi ziwiya zopatulika za Mulungu woona n’kuziika m’nyumba ya dzina+ la Yehova imene imangidweyo.”

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Wamtendere.”
Onani Zakumapeto 12.