1 Mbiri 20:1-8

20  Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Yowabu anatsogolera gulu lankhondo+ n’kukawononga dziko la ana a Amoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu. Tsopano Yowabu uja anapha anthu+ ku Raba n’kuwononga mzindawo.  Koma Davide anatenga chisoti chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu,+ ndipo golide wa chisoticho anali wolemera talente* limodzi. Chisoticho chinalinso ndi miyala yamtengo wapatali. Kenako anthu anaveka Davide chisoticho. Zinthu zimene anafunkha mumzindawo zinali zochuluka kwambiri.+  Anthu amene anali mumzindawo Davide anawatulutsa, ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito+ yocheka miyala, kusula zitsulo zakuthwa, ndiponso kusula nkhwangwa.+ Zimenezi n’zimene Davide anachitira mizinda yonse ya ana a Amoni. Pamapeto pake, Davide pamodzi ndi anthu onse anabwerera ku Yerusalemu.  Ndiyeno nkhondo imeneyi itatha, panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti+ ku Gezeri.+ Pa nthawi imeneyo Sibekai+ Mhusati anapha Sipa, amene anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai,+ moti Afilisiti anagonjetsedwa.  Kenako panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti, ndipo Elihanani+ mwana wa Yairi anapha Lami m’bale wake wa Goliyati+ Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu.+  Panabukanso nkhondo ina ku Gati,+ pa nthawi imene kunali munthu wa msinkhu waukulu modabwitsa.+ Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24 zonse pamodzi.+ Ameneyunso anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+  Iye anali kutonza ndi kuderera+ Isiraeli, ndipo pamapeto pake Yonatani mwana wa Simeya,+ m’bale wake wa Davide, anamupha.  Anthu amenewa anali mbadwa za Arefai+ ku Gati.+ Iwo anaphedwa+ ndi dzanja la Davide ndi la atumiki ake.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.