1 Mbiri 2:1-55

2  Awa ndiwo anali ana a Isiraeli:+ Rubeni,+ Simiyoni,+ Levi,+ Yuda,+ Isakara,+ Zebuloni,+  Dani,+ Yosefe,+ Benjamini,+ Nafitali,+ Gadi,+ ndi Aseri.+  Ana a Yuda anali Ere,+ Onani,+ ndi Shela.+ Mwana wamkazi wa Sua Mkanani ndiye anam’berekera ana atatuwa. Ere mwana woyamba wa Yuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo iye anamupha.+  Tamara+ mpongozi wake ndiye anam’berekera Perezi+ ndi Zera. Ana onse a Yuda anali asanu.  Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.+  Ana a Zera+ anali Zimiri, Etani, Hemani, Kalikoli, ndi Dara.+ Onse pamodzi analipo asanu.  Mwana wa Karami+ anali Akari,* amene anachititsa Isiraeli kunyanyalidwa.+ Iye anachita zinthu zosakhulupirika zokhudzana ndi chinthu choyenera kuwonongedwa.+  Mwana wa Etani+ anali Azariya.  Ana amene Hezironi+ anabereka anali Yerameeli,+ Ramu,+ ndi Kelubai. 10  Ramu anabereka Aminadabu, Aminadabu+ anabereka Naasoni+ mtsogoleri wa ana a Yuda. 11  Naasoni anabereka Salima,+ Salima anabereka Boazi,+ 12  Boazi anabereka Obedi,+ Obedi anabereka Jese,+ 13  Jese anabereka mwana wake woyamba Eliyabu,+ wachiwiri Abinadabu,+ wachitatu Simeya,+ 14  wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, 15  wa 6 Ozemu, ndipo wa 7 anali Davide.+ 16  Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli,+ ndipo Zeruya anali ndi ana atatu: Abisai,+ Yowabu,+ ndi Asaheli.+ 17  Abigayeli anabereka Amasa,+ ndipo bambo ake a Amasa anali Yeteri+ Mwisimaeli. 18  Kalebe mwana wa Hezironi+ anabereka ana kudzera mwa Azuba mkazi wake ndiponso kudzera mwa Yerioti. Ana akewo anali: Yeseri, Sobabu, ndi Aridoni. 19  Patapita nthawi, Azuba anamwalira. Chotero Kalebe anakwatira Efurata,+ yemwe m’kupita kwa nthawi anam’berekera Hura.+ 20  Hura anabereka Uri.+ Uri anabereka Bezaleli.+ 21  Kenako Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri,+ bambo wa Giliyadi.+ Hezironi anakwatira ali ndi zaka 60, koma mkaziyo anam’berekera Segubu. 22  Segubu anabereka Yairi,+ amene anadzakhala ndi mizinda 23+ m’dziko la Giliyadi. 23  Kenako Gesuri+ ndi Siriya+ analanda Havoti-yairi.+ Analandanso Kenati+ ndi midzi yake yozungulira, mizinda 60. Onsewa anali ana a Makiri, bambo wa Giliyadi. 24  Hezironi+ atamwalira ku Kalebe-efurata, Abiya mkazi wake anam’berekera Ashari bambo wa Tekowa.+ 25  Ana a Yerameeli+ mwana woyamba wa Hezironi anali Ramu+ woyamba kubadwa, ndi Buna, Oreni, Ozemu, ndi Ahiya. 26  Yerameeli anakwatira mkazi wina dzina lake Atara. Iye anali mayi ake a Onamu. 27  Ana a Ramu+ mwana woyamba wa Yerameeli anali Maazi, Yamini, ndi Ekeri. 28  Ana a Onamu+ anali Samai ndi Yada. Ana a Samai anali Nadabu ndi Abisuri. 29  Mkazi wa Abisuri dzina lake linali Abihaili, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’berekera Abani ndi Molidi. 30  Ana a Nadabu+ anali Seledi ndi Apaimu, koma Seledi anamwalira wopanda mwana. 31  Mwana wa Apaimu anali Isi, mwana wa Isi anali Sesani,+ mwana wa Sesani anali Alai. 32  Ana a Yada m’bale wake wa Samai anali Yeteri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda mwana. 33  Ana a Yonatani anali Pelete ndi Zaza. Awa ndiwo anali ana a Yerameeli. 34  Sesani+ analibe ana aamuna, koma anali ndi ana aakazi. Iye anali ndi wantchito wachiiguputo+ dzina lake Yaha. 35  Choncho Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yaha kuti akhale mkazi wake, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’berekera Atai. 36  Atai anabereka Natani, Natani anabereka Zabadi,+ 37  Zabadi anabereka Efilali, Efilali anabereka Obedi, 38  Obedi anabereka Yehu, Yehu anabereka Azariya, 39  Azariya anabereka Helezi, Helezi anabereka Eleasa, 40  Eleasa anabereka Sisimai, Sisimai anabereka Salumu, 41  Salumu anabereka Yekamiya, ndipo Yekamiya anabereka Elisama. 42  Ana a Kalebe+ m’bale wake wa Yerameeli anali Mesa mwana wake woyamba, yemwe anali bambo wa Zifi, ndi ana a Maresha bambo wa Heburoni. 43  Ana a Heburoni anali Kora, Tapuwa, Rekemu, ndi Sema. 44  Sema anabereka Rahamu bambo wa Yorikeamu. Rekemu anabereka Samai. 45  Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali bambo wa Beti-zuri.+ 46  Efa mdzakazi wa Kalebe anabereka Harana, Moza, ndi Gazezi. Harana anabereka Gazezi. 47  Ana a Yahadai anali Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efa, ndi Safa. 48  Maaka mdzakazi wa Kalebe anabereka Seberi ndi Tirana. 49  M’kupita kwa nthawi anabereka Safa bambo wa Madimana.+ Anaberekanso Seva bambo wa Makibena ndi Gibeya.+ Mwana wamkazi wa Kalebe+ anali Akisa.+ 50  Awa ndiwo anali ana a Kalebe. Tsopano awa ndiwo ana a Hura+ mwana woyamba wa Efurata:+ Sobala+ bambo wa Kiriyati-yearimu,+ 51  Salima bambo wa Betelehemu,+ ndi Harefi bambo wa Beti-gaderi. 52  Sobala+ bambo wa Kiriyati-yearimu anabereka ana awa: Haroye, ndi hafu ya anthu otchedwa Amenuhoti. 53  Mabanja a Kiriyati-yearimu anali Aitiri,+ Aputi, Asumati, ndi Amisirai. Azorati+ ndi Aesitaoli+ anachokera ku mabanja amenewa. 54  Ana a Salima anali anthu okhala ku Betelehemu,+ ku Netofa,+ ndi ku Atiroti-beti-yowabu. Hafu ya anthu okhala ku Manahati ndi anthu okhala ku Zora, analinso ana a Salima. 55  Mabanja a alembi amene anali kukhala ku Yabezi+ anali Atirati, Asimeati, ndi Asukati. Amenewa anali Akeni+ amene anachokera kwa Hamati bambo wa nyumba ya Rekabu.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Akari” limatanthauza “Mavuto, Wovutitsa.” Pa Yoswa 7:1, 18, akutchedwa “Akani.”