1 Mbiri 18:1-17

18  Pambuyo pake, Davide anapha Afilisiti+ ndi kuwagonjetsa, ndipo anawalanda mzinda wa Gati+ ndi midzi yake yozungulira.  Kenako anagonjetsa Mowabu,+ moti Amowabuwo anakhala atumiki a Davide ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+  Davide anapha Hadadezeri+ mfumu ya Zoba+ ku Hamati,+ pamene Hadadezeriyo anali kupita kumtsinje wa Firate+ kukakhazikitsa ulamuliro wake kumeneko.  Ndipo Davide analanda magaleta 1,000, anagwira amuna 7,000 okwera pamahatchi* ndi amuna 20,000 oyenda pansi.+ Kenako Davide anapundula*+ mahatchi onse a magaleta+ kusiyapo mahatchi a magaleta okwana 100.  Pamene Asiriya a ku Damasiko anabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba,+ Davide anapha amuna 22,000 a ku Siriya.  Ndiyeno Davide anamanga midzi ya asilikali m’dera la Asiriya a ku Damasiko,+ ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho kwa iye.+ Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+  Davide anatenga zishango zozungulira+ zagolide zimene zinali ndi atumiki a Hadadezeri ndipo anabwera nazo ku Yerusalemu.+  Komanso Davide anatenga mkuwa wambirimbiri ku Tibati+ ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezeri. Solomo anagwiritsa ntchito mkuwa umenewu kupangira thanki lamkuwa,+ zipilala+ ndi ziwiya zamkuwa.+  Tsopano Tou, mfumu ya Hamati,+ atamva kuti Davide wapha gulu lonse lankhondo la Hadadezeri+ mfumu ya Zoba, 10  nthawi yomweyo anatumiza mwana wake Hadoramu+ kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake ndi kumuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri ndi kumugonjetsa (pakuti Hadadezeri ndi Tou anali kumenyana kawirikawiri). Popita kwa Davide, Hadoramu anatenga zinthu zosiyanasiyana zagolide, zasiliva,+ ndi zamkuwa. 11  Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira+ Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide amene inalanda ku mitundu yonse,+ kuchokera ku Edomu, ku Mowabu,+ kwa ana a Amoni,+ Afilisiti,+ ndi Aamaleki.+ 12  Nayenso Abisai+ mwana wa Zeruya,+ anapha Aedomu 18,000 m’chigwa cha Mchere.+ 13  Choncho anakhazikitsa midzi ya asilikali mu Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala akapolo a Davide.+ Yehova anali kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+ 14  Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli yense+ ndipo nthawi zonse anali kupereka zigamulo ndi kuchita chilungamo kwa anthu ake onse.+ 15  Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa gulu lankhondo,+ ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 16  Zadoki+ mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara anali ansembe, pamene Savisa+ anali mlembi. 17  Benaya+ mwana wa Yehoyada+ anali mtsogoleri wa Akereti+ ndi Apeleti,+ ndipo ana aamuna a Davide ndiwo anali ndi udindo waukulu kwambiri pamaso pa mfumu.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Anali kuwapundula mwa kudula mtsempha wa kuseri kwa mwendo wam’mbuyo.