1 Mbiri 16:1-43

16  Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+  Davide atamaliza kupereka nsembe yopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano,+ anadalitsa+ anthu m’dzina la Yehova.+  Kuwonjezera apo, Aisiraeli onse, mwamuna komanso mkazi, aliyense wa iwo anapatsidwa+ keke yozungulira, zipatso za kanjedza zouma zoumba pamodzi ndi mphesa zouma zoumba pamodzi.  Ndiyeno Davide anaika Alevi+ ena kukhala otumikira+ pa likasa la Yehova kuti azikumbutsa+ anthu, kuyamika,+ ndi kutamanda+ Yehova Mulungu wa Isiraeli.  Mtsogoleri wawo anali Asafu,+ wachiwiri wake anali Zekariya. Panalinso Yeyeli, Semiramoti, Yehiela, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obedi-edomu, ndi Yeyeli.+ Onsewa anali ndi zoimbira za zingwe ndi azeze,+ ndipo Asafu+ anali kuimba zinganga mokweza.+  Benaya ndi Yahazieli, omwe anali ansembe, ankaimba malipenga+ nthawi zonse patsogolo pa likasa la pangano la Mulungu woona.  Pa tsiku limeneli m’pamene Davide anathandiza+ nawo kuyamika+ Yehova kudzera mwa Asafu+ ndi abale ake kwanthawi yoyamba, ndi nyimbo yakuti:   “Yamikani Yehova,+ anthu inu. Itanani pa dzina lake.+Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake!+   Muimbireni,+ muimbireni nyimbo zomutamanda!+Sinkhasinkhani ntchito zake zonse zodabwitsa.+ 10  Nyadirani dzina+ lake loyera.+Mtima wa anthu ofunafuna Yehova usangalale.+ 11  Funafunani Yehova ndiponso mphamvu zake,+Funafunani nkhope yake+ nthawi zonse. 12  Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,+ 13  Inu mbadwa za Isiraeli mtumiki wake,+Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.+ 14  Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+ Zigamulo zake zili padziko lonse lapansi.+ 15  Kumbukirani pangano lake mpaka kalekale,+Kumbukirani lonjezo limene anapereka, ku mibadwo 1,000,+ 16  Kumbukirani pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki.+ 17  Pangano limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,+Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,+ 18  Pamene anati: ‘Ndidzakupatsa dziko la Kanani,+Kuti likhale gawo la cholowa chako.’+ 19  Pamene ananena zimenezi n’kuti inu muli ochepa,+N’kuti muli ochepa kwambiri, komanso muli alendo m’dzikolo.+ 20  Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,+Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina.+ 21  Mulungu sanalole aliyense kuwachitira zachinyengo,+Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+ 22  Iye anati: ‘Anthu inu musakhudze odzozedwa anga,Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’+ 23  Imbirani Yehova, inu nonse okhala padziko lapansi!+Tsiku ndi tsiku lengezani chipulumutso chimene amapereka!+ 24  Fotokozani za ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,Ndiponso za ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu. 25  Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+Ndipo ndi woyenera kuopedwa kuposa milungu ina yonse.+ 26  Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake.+Koma Yehova, ndiye anapanga kumwamba.+ 27  Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake,+Pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.+ 28  Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu,M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+ 29  M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake,+Tengani mphatso n’kubwera nayo pamaso pake.+Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+ 30  Njenjemerani ndi mantha* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi!Ndiponso dziko lapansi ndi lokhazikika,Silidzagwedezeka ku nthawi zonse.+ 31  Kumwamba kukondwere, ndipo dziko lapansi lisangalale,+Ndipo anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’+ 32  Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,+Mtunda ukondwere ndi zonse zimene zili kumeneko.+ 33  Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera chifukwa cha Yehova,+Pakuti iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+ 34  Yamikani Yehova anthu inu, chifukwa iye ndi wabwino,+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 35  Nenani kuti: ‘Tipulumutseni, inu Mulungu wachipulumutso chathu,+Tisonkhanitseni pamodzi ndi kutilanditsa kwa anthu a mitundu ina,+Kuti titamande dzina lanu loyera,+ ndiponso kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+ 36  Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli kuyambira kalekale mpaka kalekale.’”+Ndiyeno anthu onse ananena kuti, “Ame!”* n’kutamanda Yehova.+ 37  Kenako Davide anasiya Asafu+ ndi abale ake kumeneko pamaso pa likasa la Yehova, kuti azitumikira+ pamaso pa Likasalo nthawi zonse, malinga ndi zofunikira pa tsiku lililonse.+ 38  Anasiyanso Obedi-edomu ndi abale ake okwanira 68, ndiponso Obedi-edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa kukhala alonda a pachipata. 39  Anasiyanso Zadoki+ wansembe ndi abale ake ansembe kuchihema cha Yehova chimene chinali pamalo okwezeka a ku Gibeoni,+ 40  kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova nthawi zonse paguwa lansembe zopsereza, m’mawa ndi madzulo, malinga ndi zonse zolembedwa m’chilamulo cha Yehova chimene analamula Aisiraeli.+ 41  Iwowa anali limodzi ndi Hemani+ ndi Yedutuni ndiponso amuna onse amene anasankhidwa+ mwa kutchulidwa mayina kuti aziyamika Yehova,+ chifukwa “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+ 42  Anasiya Hemani+ ndi Yedutuni+ limodzi ndi amuna aja kuti aziimba malipenga,+ zinganga ndi zipangizo zina zoimbira nyimbo ya Mulungu woona, ndipo ana+ a Yedutuni anali alonda a pachipata. 43  Pambuyo pake anthu onse ananyamuka, ndipo aliyense anapita kunyumba kwake.+ Nayenso Davide anapita kunyumba kwake n’kukadalitsa banja lake.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “imvani kupweteka kwambiri.”
Mawuwa amatanthauza kuti, “zikhale momwemo.”