1 Mbiri 13:1-14

13  Tsopano Davide anakambirana ndi mkulu aliyense wa anthu 1,000, wa anthu 100 ndiponso mtsogoleri aliyense.+  Iye anauza mpingo wonse wa Isiraeli kuti: “Ngati mukuona kuti ndi bwino ndiponso ngati zili zovomerezeka kwa Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kupita kwa abale athu ena m’madera onse a Isiraeli.+ Uthengawu upitenso kwa ansembe,+ ndi kwa Alevi,+ m’mizinda yawo+ yonse yokhala ndi malo odyetserako ziweto, kuti abwere kuno.  Kenako tikatenge likasa+ la Mulungu wathu n’kubwera nalo mpaka kwathu kuno.” Anatero chifukwa chakuti m’masiku a Sauli likasalo sanali kulisamala.+  Choncho mpingo wonse unagwirizana nazo, chifukwa anthu onse anaona kuti ndi bwino kutero.+  Chotero, Davide anasonkhanitsa+ Aisiraeli onse kuchokera kumtsinje wa Iguputo+ mpaka kukafika polowera ku Hamati,+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu.+  Atatero, Davide ndi Aisiraeli onse ananyamuka kupita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali m’dera la Yuda. Anapita kumeneko kukatenga likasa la Mulungu woona, Yehova, wokhala pa akerubi.+ Palikasa limeneli, amaitanirapo dzina lake.  Koma iwo ananyamulira likasa la Mulungu woonalo pangolo yatsopano+ kuchokera kunyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo+ anali kutsogolera ngoloyo.  Ndipo Davide ndi Aisiraeli onse anali kusangalala kwadzaoneni+ pamaso pa Mulungu woona. Anali kuimba nyimbo+ ndi azeze,+ zoimbira za zingwe,+ maseche,+ zinganga ndi malipenga.+  Kenako anafika kumalo opunthira mbewu a Kidoni,+ ndipo Uza anatambasulira dzanja lake pa Likasa+ n’kuligwira, chifukwa ng’ombe zinatsala pang’ono kuligwetsa. 10  Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, ndipo anamupha chifukwa anatambasula dzanja lake n’kugwira Likasa,+ moti Uza anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.+ 11  Zitatero, Davide anakwiya+ chifukwa mkwiyo wa Yehova unaphulikira Uza modzidzimutsa. Chotero malo amenewo amatchedwa dzina lakuti Perezi-uza* kufikira lero. 12  Tsiku limenelo, Davide anachita mantha kwambiri chifukwa cha Mulungu woona,+ ndipo anati: “Kodi ndibweretsa bwanji likasa la Mulungu woona kumene ine ndikukhala?”+ 13  Pamenepo Davide sanatenge Likasa kupita nalo kumene anali kukhala ku Mzinda wa Davide. M’malomwake, analipatutsira kunyumba ya Obedi-edomu+ Mgiti.+ 14  Likasa la Mulungu woona linakhalabe ndi banja la Obedi-edomu kunyumba kwake+ kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anapitiriza kudalitsa+ banja la Obedi-edomu, ndi zinthu zake zonse.

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Mkwiyo Woyakira Uza.”