1 Mbiri 11:1-47

11  Patapita nthawi, Aisiraeli+ onse anasonkhana kwa Davide ku Heburoni+ ndi kumuuza kuti: “Ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.+  Kuyambira kale, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inuyo munali kutsogolera Isiraeli polowa ndi potuluka.+ Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuuzani kuti, ‘Udzaweta+ anthu anga Aisiraeli, ndipo udzakhala mtsogoleri+ wa anthu anga Aisiraeli.’”  Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Davide anachita nawo pangano ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli, mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene analankhula kudzera mwa Samueli.+  Pambuyo pake Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Yerusalemu,+ kapena kuti ku Yebusi,+ dziko limene kunali kukhala Ayebusi.+  Anthu okhala ku Yebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno.”+ Ngakhale zinali choncho, Davide analanda Ziyoni,+ malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, umene ndi Mzinda wa Davide.+  Chotero Davide anati: “Aliyense amene ayambirire kuukira+ Ayebusi akhala mtsogoleri ndiponso kalonga.” Pamenepo Yowabu+ mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, choncho anakhala mtsogoleri.  Ndiyeno Davide anayamba kukhala m’malo ovuta kufikako.+ N’chifukwa chake mzindawo anautcha kuti Mzinda wa Davide.+  Kenako Davide anayamba kumanga mzinda pamalo onsewo, kuyambira ku Chimulu cha Dothi* mpaka kumadera ozungulira, koma Yowabu ndiye anadzamanganso+ mzinda wonsewo.  Chotero ulamuliro wa Davide unakulirakulira,+ chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.+ 10  Tsopano otsatirawa ndiwo atsogoleri a amuna amphamvu+ a Davide omwe anali kulimbikitsa nawo ufumu wake mwamphamvu pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu malinga ndi mawu a Yehova+ okhudza Isiraeli. 11  Uwu ndiwo mndandanda wa amuna amphamvu a Davide: Yasobeamu+ mwana wa Mhakimoni, yemwe anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 300 ulendo umodzi.+ 12  Wotsatira wake anali Eleazara+ mwana wa Dodo, Muahohi.+ Iye anali mmodzi wa amuna atatu amphamvuwo.+ 13  Iye ndiye anali limodzi ndi Davide ku Pasi-damimu+ kumene Afilisiti anasonkhana kuti achite nawo nkhondo. Kumeneko kunali munda wodzaza ndi balere, ndipo anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo.+ 14  Koma iye anaima pakati pa mundawo n’kuulanditsa. Anapha Afilisiti moti Yehova anapereka chipulumutso+ chachikulu.+ 15  Kenako, atatu mwa atsogoleri 30+ anapita kwa Davide kuthanthwe, kuphanga la Adulamu.+ Pa nthawiyi gulu lankhondo la Afilisiti linali litamanga msasa m’chigwa cha Arefai.+ 16  Pamenepo n’kuti Davide ali m’malo ovuta kufikako,+ ndiponso n’kuti mudzi wa asilikali a Afilisiti+ uli ku Betelehemu. 17  Patapita nthawi, Davide anafotokoza zimene anali kulakalaka, kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa+ madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu+ chimene chili pachipata!” 18  Pamenepo amuna atatu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+ 19  Iye anati: “Sindingachite zimenezo chifukwa ndimalemekeza Mulungu wanga. Kodi ndimwe magazi+ a anthuwa omwe anaika moyo wawo pachiswe? Iwowa akanataya moyo wawo pokatunga madziwa.” Chotero iye anakana kumwa madziwo.+ Izi n’zimene amuna atatu amphamvu aja anachita. 20  Abisai+ m’bale wake wa Yowabu+ anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye ananyamula mkondo n’kupha anthu 300 ulendo umodzi, ndipo anali wotchuka ngati amuna atatu aja. 21  Pa amuna atatuwo, iye anali wolemekezeka kwambiri kuposa awiri enawo, ndipo anakhala mtsogoleri wawo. Koma sanafanane+ ndi amuna atatu oyambirira aja. 22  Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa. 23  Benaya ndiye anaphanso Mwiguputo wa msinkhu waukulu modabwitsa, yemwe anali chiphona chachitali mikono* isanu.+ Mwiguputoyo anali ndi mkondo+ m’manja mwake, waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu, koma Benaya anapitabe kukakumana naye atanyamula ndodo, n’kulanda mkondowo ndipo anamupha ndi mkondo wake womwewo.+ 24  Izi n’zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita, ndipo dzina lake linali pakati pa amuna atatu amphamvu. 25  Ngakhale kuti anali wolemekezeka kuposa amuna 30 aja, iye sanafikepo pa amuna atatu oyamba aja.+ Komabe Davide anamuika kukhala mtsogoleri wa asilikali omulondera.+ 26  Amuna amphamvu a magulu ankhondo anali Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu, Elihanani+ mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, 27  Samoti+ Mharori, Helezi Mpeloni,+ 28  Ira+ mwana wa Ikesi Mtekowa, Abi-ezeri Muanatoti,+ 29  Sibekai+ Mhusati, Ilai Muahohi,+ 30  Maharai+ Mnetofa,+ Heledi+ mwana wa Bana Mnetofa, 31  Ifai mwana wa Ribai+ wa ku Gibeya+ wa fuko la ana a Benjamini,+ Benaya Mpiratoni,+ 32  Hurai wa kuzigwa* za Gaasi,+ Abiyeli Muaraba, 33  Azimaveti M’bahurimu,+ Eliyaba Msaaliboni, 34  ana a Hasemu Mgizoni, Yonatani+ mwana wa Sage Mharari, 35  Ahiyamu mwana wa Sakari+ Mharari, Elifali+ mwana wa Uri, 36  Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni, 37  Heziro wa ku Karimeli,+ Naarai mwana wa Ezibai, 38  Yoweli m’bale wake wa Natani,+ Mibari mwana wa Hagiri, 39  Zeleki Muamoni, Naharai M’beeroti yemwe anali wonyamula zida wa Yowabu mwana wa Zeruya, 40  Ira Muitiri, Garebi+ Muitiri, 41  Uriya+ Mhiti,+ Zabadi mwana wa Alai, 42  Adina mwana wa Siza Mrubeni yemwe anali mtsogoleri wa Arubeni okwanira 30, 43  Hanani mwana wa Maaka, Yosafati Mmitini, 44  Uzia Muasitaroti, Sama ndi Yeyeli ana a Hotamu Muaroweli, 45  Yediyaeli mwana wa Simuri, m’bale wake Yoha Mtizi, 46  Elieli Mmahavi, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima Mmowabu, 47  Elieli, Obedi, ndi Yaasiyeli Mmezobai.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.