1 Mbiri 10:1-14

10  Tsopano Afilisiti+ anayamba kumenyana ndi Aisiraeli ndipo amuna a Isiraeli anali kuthawa pamaso pa Afilisitiwo, moti anali kuphedwa m’phiri la Giliboa.+  Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani,+ Abinadabu+ ndi Malikisuwa,+ ana a Sauli.+  Nkhondo inamukulira kwambiri Sauli, moti pamapeto pake oponya mivi ndi uta anamupeza n’kumuvulaza.+  Kenako Sauli anauza womunyamulira zida+ kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundizunza.”+ Koma womunyamulira zida uja sanafune+ kuchita zimenezo, chifukwa anali kuchita mantha kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake n’kuligwera.+  Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa, nayenso anagwera palupanga n’kufa.+  Chotero Sauli ndi ana ake atatu anafa,+ ndipo anthu onse a m’nyumba yake anafera limodzi.  Amuna onse a Isiraeli amene anali m’chigwa ataona kuti asilikaliwo athawa, komanso kuti Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuchoka m’mizinda yawo ndi kuthawa.+ Kenako Afilisiti anabwera n’kuyamba kukhala m’mizindayo.  Ndiyeno tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzavula zovala+ anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa paphiri la Giliboa.+  Iwo anam’vula Sauli n’kumudula mutu,+ ndi kumuvula zida zake. Kenako anatumiza uthenga+ m’dziko lonse la Afilisiti, kwa mafano awo+ ndi kwa anthu awo. 10  Pamapeto pake, anakaika zida zakezo m’nyumba ya mulungu wawo,+ ndipo mutu wake anakaumangirira kunyumba ya Dagoni.+ 11  Anthu onse a ku Yabesi+ ku Giliyadi anamva zonse zimene Afilisiti anamuchita Sauli.+ 12  Chotero amuna onse olimba mtima ananyamuka n’kukanyamula mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake n’kupita nayo ku Yabesi. Atatero anakafotsera mafupa awo pansi pa mtengo waukulu+ ku Yabesiko.+ Kenako anasala kudya+ masiku 7. 13  Choncho Sauli anafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake popeza anachita zosakhulupirika+ kwa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu.+ 14  Sauli sanafunse kwa Yehova,+ chotero iye anamupha n’kupereka ufumuwo kwa Davide mwana wa Jese.+

Mawu a M'munsi

Ena amati, “kugwaza.”