1 Mafumu 9:1-28
9 Solomo atangomaliza kumanga nyumba+ ya Yehova ndi nyumba ya mfumu+ ndiponso chinthu chilichonse chimene anafuna kupanga,+
2 Yehova anaonekera kwa iye kachiwiri, mofanana ndi momwe anamuonekera ku Gibeoni.+
3 Ndipo Yehova anamuuza kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndi pempho lako lopempha chifundo kwa ine. Ndayeretsa+ nyumba imene wamangayi mwa kuikapo dzina langa+ mpaka kalekale, ndipo maso anga+ ndi mtima wanga adzakhala pamenepo nthawi zonse.+
4 Iweyo ukayenda+ pamaso panga monga momwe Davide+ bambo ako anayendera, yemwe anali ndi mtima wosagawanika+ ndipo anayenda mowongoka,+ ukachita mogwirizana ndi zonse zimene ndinakulamula,+ komanso ukasunga malangizo anga+ ndi zigamulo zanga,+
5 inenso ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu ufumu wa Isiraeli mpaka kalekale, monga momwe ndinalonjezera Davide bambo ako kuti, ‘Munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+
6 Koma inuyo ndi ana anu mukadzabwerera n’kusiya kunditsatira,+ osasunga malamulo anga amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina+ ndi kuigwadira,
7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.
8 Nyumba iyi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi nayo adzayang’ana modabwa+ ndi kuimba mluzu n’kunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anachita zimenezi padzikoli ndi panyumbayi?’+
9 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake, anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira. N’chifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+
10 Ndiyeno pamapeto pa zaka 20 zimene Solomo anamanga nyumba ziwirizo, nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu,+
11 Mfumu Solomo anapatsa Hiramu mizinda 20 m’dera la Galileya.+ (Hiramu+ mfumu ya Turo anathandiza Solomo+ ndi matabwa a mkungudza, matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza, ndi golide yense amene anafuna.)+
12 Choncho Hiramu anachoka ku Turo kupita kukaona mizinda imene Solomo anamupatsa, koma sinamusangalatse ataiona.+
13 Ndipo anati: “Kodi mizinda wandipatsayi ndi yamtundu wanji m’bale wanga?” Chotero mizindayo inatchedwa Dziko la Kabulu* mpaka lero.
14 Pa nthawi imeneyo, Hiramu anatumiza kwa mfumuyo golide wokwana matalente* 120.+
15 Mfumu Solomo inaitana anthu ogwira ntchito yokakamiza+ kuti adzamange nyumba ya Yehova,+ nyumba yake, Chimulu cha Dothi,*+ khoma+ lozungulira Yerusalemu, ndiponso mizinda ya Hazori,+ Megido,+ ndi Gezeri.+
16 (M’mbuyomo, Farao mfumu ya Iguputo inabwera n’kulanda mzinda wa Gezeri n’kuutentha ndi moto. Akanani+ okhala mumzindawo inawapha. Kenako inaupereka kwa mwana wake wamkazi+ monga mphatso pamene anali kukwatiwa ndi Solomo.)
17 Solomo anamanganso Gezeri, Beti-horoni Wakumunsi,+
18 Baalati,+ ndi Tamara m’chipululu cha m’dzikolo.
19 Anamanganso mizinda yake yonse yosungirako zinthu,+ mizinda yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi, ndiponso zilizonse zimene iye anakonda+ kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni, ndi m’dziko lonse limene ankalamulira.
20 Anthu onse otsala a Aamori,+ Ahiti,+ Aperezi,+ Ahivi,+ ndi Ayebusi,+ amene sanali ana a Isiraeli,+
21 ana awo amene anatsala m’dzikomo, amene ana a Isiraeli analephera kuwawononga,+ Solomo anali kuwagwiritsa ntchito yaukapolo. Anthuwa akupitiriza kugwira ntchito yotere kufikira lero.+
22 Palibe ana a Isiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo,+ chifukwa iwo anali ankhondo ake, atumiki ake, akalonga ake, asilikali othandiza pa magaleta, ndiponso atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta, ndi a amuna ake okwera pamahatchi.+
23 Panali akuluakulu oyang’anira nduna okwana 550 amene ankayang’anira ntchito ya Solomo. Iwowa anali akapitawo oyang’anira anthu ogwira ntchito.+
24 Mwana wamkazi wa Farao+ anachoka ku Mzinda wa Davide+ n’kukakhala kunyumba yake imene Solomo anam’mangira. Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+
25 Katatu+ pachaka, Solomo ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano paguwa lansembe limene anamangira Yehova.+ Ankapereka nsembe zautsi paguwa lansembe+ lomwe linali pamaso pa Yehova, ndipo anamaliza kumanga nyumbayo.+
26 Panali zombo zimene Mfumu Solomo inapanga ku Ezioni-geberi,+ pafupi ndi Eloti,+ pagombe la Nyanja Yofiira m’dziko la Edomu.+
27 M’zombomo, Hiramu ankatumizamo antchito ake+ omwe anali amalinyero odziwa za panyanja, pamodzi ndi antchito a Solomo.
28 Iwo ankapita ku Ofiri+ n’kukatenga golide wokwana matalente 420,+ n’kubwera naye kwa Mfumu Solomo.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “Dziko Lopanda Pake,” kapenanso “Dziko Lomangidwa Maunyolo.”
^ Onani Zakumapeto 12.