1 Mafumu 8:1-66

8  Pa nthawi imeneyo Solomo+ anauza akulu,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a makolo+ a ana a Isiraeli, kuti asonkhane+ kwa Mfumu Solomo ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa la pangano+ la Yehova ku Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+  Choncho anthu onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa Mfumu Solomo pachikondwerero+ cha m’mwezi wa Etanimu, womwe ndi mwezi wa 7.+  Akulu onse a Isiraeli anabwera, ndipo ansembe anayamba kunyamula+ Likasa.+  Ansembe ndi Alevi+ ananyamula+ likasa la Yehova, chihema+ chokumanako,+ ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali m’chihemacho.  Mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Isiraeli, onse amene anabwera atawaitana, anafika pamaso pa Likasa n’kuyamba kupereka nsembe+ zambiri za nkhosa ndi ng’ombe, zomwe sanathe kuziwerenga chifukwa chochuluka.+  Kenako ansembe anabweretsa likasa+ la pangano la Yehova kumalo ake,+ kuchipinda chamkati cha nyumbayo, Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+  Akerubiwo anatambasulira mapiko awo pamwamba pa malo okhala Likasa, moti akerubiwo anatchinga pamwamba pa Likasa ndi mitengo yake yonyamulira.+  Koma mitengo yonyamulirayo+ inali yaitali, moti nsonga zake zinkaoneka kuchokera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinali kuoneka kunja. Mitengo yonyamulirayo ikadali pomwepo mpaka lero.+  Mu Likasalo munalibe chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo+ ku Horebe. Anaiikamo nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi ana a Isiraeli, pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+ 10  Tsopano ansembe atatuluka m’malo oyera, mtambo+ unadzaza nyumba ya Yehova. 11  Chifukwa cha mtambowo, ansembewo+ analephera kupitiriza kutumikira,+ popeza ulemerero+ wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehovayo.+ 12  Pa nthawi imeneyo Solomo anati: “Yehova anati adzakhala mu mdima wandiweyani.+ 13  Ine ndakwanitsa kukumangirani nyumba yomwe ndi malo anu okhalamo okwezeka,+ malo okhazikika+ oti mukhalemo mpaka kalekale.”+ 14  Kenako mfumu inatembenuka n’kuyang’ana anthuwo. Ndiyeno inayamba kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli. Pamenepo n’kuti mpingo wonse wa Isiraeli utaimirira. 15  Mfumuyo inapitiriza kuti: “Adalitsike Yehova+ Mulungu wa Isiraeli, amene analankhula ndi pakamwa pake kwa Davide+ bambo anga, ndipo ndi dzanja lake wakwaniritsa zimene ananena,+ zakuti, 16  ‘Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisiraeli m’dziko la Iguputo, sindinasankhe+ mzinda m’mafuko onse a Isiraeli woti iwo amangeko nyumba+ ya dzina langa+ kuti likhale kumeneko. Koma ndidzasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+ 17  Ndipo bambo anga Davide, anafuna mumtima mwawo kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 18  Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Popeza unafuna mumtima mwako kumanga nyumba ya dzina langa, unachita bwino chifukwa unafuna mumtima mwako kuchita zimenezi.+ 19  Koma iweyo sumanga nyumbayi, m’malomwake mwana wako wamwamuna wotuluka m’chiuno mwako ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 20  Yehova anakwaniritsa mawu amene ananena,+ kuti ineyo ndilowe m’malo mwa Davide bambo anga n’kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli,+ monga momwe Yehova ananenera, ndiponso kuti ndimange nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 21  Komanso kuti m’nyumbamo ndisankhemo malo oika Likasa, lomwe muli pangano+ la Yehova limene anapangana ndi makolo athu pamene anali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo.” 22  Tsopano Solomo anaimirira kutsogolo kwa guwa lansembe+ la Yehova pamaso pa mpingo wonse wa Isiraeli. Kenako anatambasula manja ake n’kuwakweza kumwamba.+ 23  Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu+ amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse,+ inu mumawasungira pangano ndi kukoma mtima kosatha.+ 24  Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga. Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 25  Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga, pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako asamale mayendedwe awo mwa kuyenda pamaso panga monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’ 26  Tsopano inu Mulungu wa Isiraeli, lonjezo lanu+ limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga, likwaniritsidwe chonde. 27  “Koma kodi Mulungu angakhaledi padziko lapansi?+ Taonani! Kumwamba,+ ngakhale kumwambamwamba,+ simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba+ imene ndamangayi? 28  Mutembenukire ku pemphero+ la mtumiki wanu ndi pempho lake lopempha chifundo,+ inu Yehova Mulungu wanga. Mverani kulira kwanga kochonderera ndi pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero.+ 29  Maso anu akhale akuyang’ana+ nyumba ino usiku ndi usana. Akhale akuyang’ana malo amene munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala kumeneko,’+ kuti mumvere pemphero limene mtumiki wanu akupemphera atayang’ana kumalo ano.+ 30  Mumve pemphero lopempha chifundo+ la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisiraeli, limene angapemphere atayang’ana malo ano. Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+ 31  “Munthu akachimwira mnzake,+ wochimwiridwayo n’kulumbiritsa*+ wochimwayo pofuna kutsimikiza kuti sanachimwedi, ndiyeno wochimwayo akabwera patsogolo pa guwa lansembe m’nyumba ino chifukwa cha zimene analumbira, 32  inu mumve muli kumwamba ndipo muchitepo kanthu mwa kusonyeza amene ali wolakwa pom’bwezera mogwirizana ndi njira yake,+ ndi kusonyeza amene ali wolungama+ pom’patsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo chake.+ 33  “Anthu anu Aisiraeli akagonja kwa adani+ awo chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno akabwerera kwa inu+ n’kutamanda dzina lanu+ ndi kupemphera+ ndiponso kupempha kwa inu kuti muwachitire chifundo m’nyumba ino,+ 34  inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la anthu anu Aisiraeli,+ ndi kuwabwezeretsa+ kudziko limene munapatsa makolo awo.+ 35  “Kumwamba kukatsekeka, mvula n’kumakanika kugwa+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno iwo n’kupemphera atayang’ana malo ano,+ ndi kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya tchimo lawo chifukwa choti mwakhala mukuwasautsa,+ 36  inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisiraeli, popeza mumawaphunzitsa+ njira yabwino yoti ayendemo.+ Mubweretse mvula+ padziko lanu, limene mwapatsa anthu anu monga cholowa. 37  “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu, matenda ambewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo, ndiponso kukagwa mliri wamtundu uliwonse, nthenda yamtundu uliwonse, 38  ndiyeno anthuwo akapereka pemphero lililonse,+ pempho lililonse lopempha chifundo+ limene munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli angapemphe,+ chifukwa aliyense wa iwo akudziwa ululu wa mumtima mwake,+ ndipo iwo akatambasula manja awo kuwalozetsa kunyumba ino,+ 39  inuyo mumve muli kumwamba,+ malo anu okhala okhazikika+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu.+ Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inuyo nokha mumadziwa bwino mtima wa ana onse a anthu).+ 40  Muchite zimenezi n’cholinga choti iwo akuopeni,+ masiku onse amene angakhale ndi moyo padziko limene munapatsa makolo athu.+ 41  “Komanso mlendo+ amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli, amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu+ 42  (popeza adzamva za dzina lanu lalikulu,+ za dzanja lanu lamphamvu+ ndi mkono wanu wotambasuka), ndipo wabwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino,+ 43  inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani.+ Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu,+ kuti akuopeni mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.+ 44  “Anthu anu akapita kunkhondo+ kukamenyana ndi adani awo kumene inuyo mwawatumiza,+ ndipo akapemphera+ kwa Yehova atayang’ana kumzinda umene mwasankha+ ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 45  inuyo mumve muli kumwamba pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo, ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.+ 46  “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa adani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko la adani, lakutali kapena lapafupi,+ 47  ndiyeno iwo n’kuzindikira kulakwa kwawo m’dziko limene anawatengeralo+ n’kulapa,+ ndipo akapempha+ chifundo kwa inu m’dziko la adani awo amene awagwira,+ n’kunena kuti, ‘Tachimwa,+ tachita zolakwa,+ ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 48  n’kubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, m’dziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayang’ana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, kumzinda umene mwasankha ndi nyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 49  inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.+ Mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo, ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.+ 50  Mukhululukire+ anthu anu amene anakuchimwirani.+ Muwakhululukirenso chifukwa cha malamulo anu onse amene anaphwanya,+ komanso owagwirawo akamawaona azikhudzidwa mtima+ ndi kuwachitira chisoni, 51  (popeza iwo ndi anthu anu ndi cholowa chanu,+ amene munawatulutsa ku Iguputo,+ kuwachotsa m’ng’anjo yachitsulo).+ 52  Maso anu aone pempho lopempha chifundo la mtumiki wanu, ndi pempho lopempha chifundo+ la anthu anu Aisiraeli, mwa kuwamvera zopempha zawo zonse zimene angakupempheni.+ 53  Pakuti inuyo munawapatula pakati pa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi+ kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munalankhulira kudzera mwa Mose+ mtumiki wanu, pamene munali kutulutsa makolo athu ku Iguputo, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.” 54  Tsopano Solomo atangomaliza kupemphera kwa Yehova pemphero lonseli, ndi pempho lopempha chifundo, anaimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova popeza nthawi yonseyi anali chogwada,+ manja ake atawatambasulira kumwamba.+ 55  Anaimirira+ n’kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli ndi mawu okweza, akuti: 56  “Adalitsike Yehova+ amene wapatsa anthu ake Aisiraeli malo ampumulo, monga mwa zonse zimene analonjeza.+ Palibe mawu ndi amodzi omwe+ amene sanakwaniritsidwe pa malonjezo ake onse abwino amene analonjeza kudzera mwa Mose mtumiki wake.+ 57  Yehova Mulungu wathu akhale nafe+ monga mmene anakhalira ndi makolo athu.+ Asatisiye kapena kutitaya.+ 58  Alozetse mtima wathu+ kwa iye kuti tiyende m’njira zake zonse+ ndi kusunga malamulo ake,+ malangizo ake,+ ndi zigamulo zake,+ zimene analamula makolo athu. 59  Mawu angawa amene ndanena popempha chifundo pamaso pa Yehova, azikumbukiridwa+ ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti aonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa mtumiki wake ndi anthu ake Aisiraeli, monga momwe kungafunikire tsiku+ ndi tsiku. 60  Atero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe+ kuti Yehova ndi Mulungu woona.+ Palibenso wina.+ 61  Mutumikire Yehova Mulungu wathu ndi mtima wathunthu+ mwa kuyenda motsatira malangizo ake ndi kusunga malamulo ake, monga mmene mukuchitira lero.” 62  Mfumuyo ndi Aisiraeli onse amene anali nayo anayamba kupereka nsembe yaikulu pamaso pa Yehova.+ 63  Solomo anapereka nsembe zachiyanjano+ zimene anayenera kupereka kwa Yehova. Anapereka ng’ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000+ kuti mfumuyo ndi ana onse a Isiraeli atsegulire+ nyumba ya Yehova. 64  Tsiku limenelo, pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova+ panayenera kupatulidwa ndi mfumu, chifukwa inafunika kuperekerapo nsembe yopsereza, nsembe yambewu, ndi mafuta a nsembe zachiyanjano. Inatero popeza guwa lansembe lamkuwa+ limene lili pamaso pa Yehova linachepa, ndipo nsembe yopsereza, nsembe yambewu, ndi mafuta+ a nsembe zachiyanjano sizikanakwanapo. 65  Pa nthawi imeneyo Solomo anachita chikondwerero+ pamodzi ndi Aisiraeli onse. Unali mpingo waukulu+ wa anthu amene anachokera kumadera osiyanasiyana, kuyambira polowera ku Hamati+ n’kutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ Anachita chikondwererochi pamaso pa Yehova Mulungu wathu masiku 7, ndi masiku enanso 7.+ Onse pamodzi masiku 14. 66  Pa tsiku la 8 Solomo anauza anthuwo kuti azipita,+ ndipo anthuwo anadalitsa mfumuyo n’kuyamba kupita kwawo. Anapita akusangalala,+ chimwemwe chitadzaza mumtima,+ chifukwa cha zabwino zonse+ zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake ndi anthu ake Aisiraeli.

Mawu a M'munsi

Palembali mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “n’kulumbiritsa” akunena za lumbiro limene munthu ankatha kulandira nalo chilango ngati analumbira zonama.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.