1 Mafumu 7:1-51

7  Solomo anatha zaka 13+ akumanga nyumba yake, ndipo anaimanga n’kuimaliza yonse.+  Kenako anamanga nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ Nyumbayi inali mikono 100 m’litali, mikono 50 m’lifupi, ndi mikono 30 kutalika kwake. Anaimanga pamwamba pa nsanamira za mtengo wa mkungudza. Nsanamirazo zinali m’mizere yokwanira inayi. Pamwamba pa nsanamirazo+ panali mitengo ya mkungudza yodutsa chopingasa.  Nyumba imeneyi anaimanga ndi matabwa a mkungudza+ kuyambira pazitsulo zimene zinali pamwamba pa nsanamira kupita m’mwamba. Nsanamirazo zinalipo 45, ndipo pamzere uliwonse panali nsanamira* 15.  Nyumbayi inali yosanja kawiri. Nsanjika iliyonse inali ndi mzere wa mawindo. Chotero nyumba yonseyo inali ndi mizere itatu ya mawindo okhala ndi mafelemu. Mawindowo+ anayang’anizana ndi mawindo a mbali ina ya nyumbayo.  Makomo onse a nyumbayo anali ndi mafelemu okhala ndi mbali zonse zinayi zofanana.+ Mbali ya mkati ya windo loyang’anizana ndi windo lina inali ndi felemu lokhala ndi mbali zinayi zofanana. Zinali chonchi mu nsanjika zonse zitatu za nyumbayi.  Kenako anamanga Khonde la Zipilala. M’litali mwake linali mikono 50, ndipo m’lifupi mwake linali mikono 30. Kutsogolo kwa zipilalazo kunali khonde lina lokhalanso ndi zipilala ndi denga.  Anamanganso Bwalo la Mpando Wachifumu,+ kumene anali kuweruzirako milandu. Bwaloli linkatchedwanso bwalo loweruzira.+ Makoma ake anali a matabwa a mkungudza kuchokera pansi mpaka kudenga.+  Kenako Solomo anamanga nyumba yake yokhalamo kubwalo lina+ chapatali ndi nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu. Kamangidwe ka nyumbayi kanali kofanana ndi ka Bwalo la Mpando Wachifumu. Panalinso nyumba ina yofanana ndi Bwaloli imene Solomo anamangira mwana wamkazi wa Farao+ amene iye anam’kwatira.  Nyumba zonsezi, kuyambira pamaziko ake mpaka pamwamba pa khoma, ndiponso kuchokera panja pa nyumbazo mpaka kubwalo lalikulu,+ zinamangidwa ndi miyala yokwera mtengo+ yochita kuyeza, ndiponso yocheka ndi macheka a miyala, mkati ndi kunja komwe. 10  Miyala yokwera mtengo imene anamangira maziko inali ikuluikulu. Kukula kwake ina inali mikono 10, ina mikono 8. 11  Pamwamba pa miyala ya mazikoyo panalinso miyala ina yokwera mtengo yochita kuyeza ndiponso yosema. Anagwiritsiranso ntchito matabwa a mkungudza. 12  Kuzungulira bwalo lalikulu panali khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu+ kuchokera pansi, ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza pamwamba pake. Bwalo lamkati+ la nyumba+ ya Yehova ndi khonde+ la nyumbayo, zinamangidwanso mofanana. 13  Kenako Mfumu Solomo inatuma anthu kuti akatenge Hiramu+ ku Turo. 14  Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo+ odziwa kupanga zinthu ndi mkuwa.+ Hiramu anali wanzeru, womvetsa bwino zinthu,+ ndiponso wodziwa bwino kupanga zinthu zosiyanasiyana zamkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo n’kuyamba kumugwirira ntchito yake yonse. 15  Anaumba zipilala ziwiri zamkuwa.+ Kutalika kwa chipilala chilichonse kunali mikono 18, ndipo pankafunika chingwe chotalika mikono 12 kuti ayeze kuzungulira chipilala chilichonse.+ 16  Anapanga mitu iwiri youmba ndi mkuwa+ n’kuiika pamwamba pa zipilalazo. Mutu umodzi kutalika kwake kunali mikono isanu, ndipo mutu winawo kutalika kwake kunalinso mikono isanu. 17  Anapanga maukonde olukanalukana ndiponso zokongoletsera zolukanalukana ngati tcheni,+ za mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo.+ Anapanga zimenezi zokwanira 7 za mutu umodzi, ndi zinanso 7 za mutu winawo. 18  Kenako anapanga mizere iwiri ya makangaza* n’kuwazunguliza pamaukonde awiri aja, n’kuveka mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo. Anachita zimenezi pamitu+ yonse iwiri. 19  Mitu imene inali pamwamba pa zipilala, pafupi ndi khonde, anaipanga ngati maluwa+ ndipo kutalika kwake inali mikono inayi. 20  Mitu iwiriyo inali pamwamba pa zipilala, komanso inali pamwamba pa mimba imene inagundana ndi maukonde. Kuzungulira mutu uliwonse, panali makangaza 200+ amene anali m’mizere. 21  Ndiyeno Hiramu anaika zipilala+ zija pakhonde+ la kachisi. Chipilala chimodzi anachiika mbali ya kudzanja lamanja n’kuchitcha Yakini. Chipilala china anachiika mbali ya kumanzere n’kuchitcha Boazi. 22  Pamwamba pa chipilala chilichonse panali pooneka ngati duwa. M’kupita kwa nthawi, ntchito yoika zipilalazo inatha. 23  Kenako iye anapanga thanki yamkuwa.*+ Pakamwa pa thankiyo panali papakulu mikono 10 kuyeza modutsa pakati pake, ndipo panali pozungulira. Thankiyo inali yaitali mikono isanu kuchokera pansi kufika pamwamba. Pankafunika chingwe chotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulira thankiyo.+ 24  Kuzungulira m’khosi mwake monse munali zokongoletsera+ zooneka ngati zipanda.+ Zinalipo 10 pa mkono uliwonse kuzungulira thanki yonseyo.+ Zokongoletsa zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri, ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo. 25  Thankiyo anaikhazika pang’ombe zamphongo 12.+ Ng’ombe zitatu zinayang’ana kumpoto, zitatu zinayang’ana kumadzulo, zitatu zinayang’ana kum’mwera, ndipo zitatu zinayang’ana kum’mawa. Thankiyo inali pamwamba pa ng’ombezo ndipo mbuyo zonse za ng’ombezo zinaloza pakati.+ 26  Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi.+ Mlomo wake unali ngati wa mphika wakukamwa ngati duwa.+ M’thankiyo munkalowa+ madzi okwana mitsuko* 2,000.+ 27  Kenako anapanga zotengera 10+ zamkuwa zokhala ndi mawilo. Chotengera chilichonse chinali mikono inayi m’litali, mikono inayi m’lifupi, ndi mikono itatu kutalika kwake kuchokera pansi kukafika pamwamba. 28  Zotengerazo zinapangidwa motere: Zinali ndi malata m’mbali mwake, ndipo malatawo anali pakati pa zitsulo zopingasana. 29  Pamalata amene anali pakati pa zitsulo zopingasana anajambulapo mikango,+ ng’ombe zamphongo,+ ndi akerubi.+ Pazitsulo zopingasana anajambulaponso zimenezo mochita kugoba. Pamwamba ndi pansi pa mikango ndi ng’ombe zamphongozo, anajambulapo mochita kugoba nkhata zamaluwa+ zopendeketsa. 30  Chotengera chilichonse chinali ndi mawilo anayi amkuwa ndi mitanda yamkuwa yolumikiza wilo ndi wilo linzake. M’makona ake anayi munali zogwiriziza mawilo, ndipo zogwirizizazo zinkafika pansi pa beseni. Zogwirizizazo anazipangira kumodzi ndi nkhata zamaluwa zochokera pa chogwiriziza chilichonse. 31  Pakamwa pake, kuyambira mkati n’kukwera m’mwamba kuchokera pa zogwiriziza, inali mikono [?].* Kamwa lake linali lozungulira lopangidwa kuti azikhazikapo beseni. Kutalika kwa kamwalo kunali mkono umodzi ndi hafu. Pakamwapo anajambulapo zinthu zokongoletsera. Zinthuzo anazijambula mochita kugoba. Malata a m’mbali mwake anali a mbali zinayi zofanana, osati ozungulira. 32  Pansi pa malata a m’mbaliwo panali mawilo anayi. Zogwiriziza za mawilowo zinali m’makona a chotengeracho. Wilo lililonse linali mkono umodzi ndi hafu kutalika kwake. 33  Mawilowo anawapanga ngati mawilo a galeta.+ Zogwiriziza zake, zingelengele zake, masipokosi ake, ndi mahabu ake, zonse zinali zoumba ndi mkuwa. 34  Panali zogwiriziza zinayi, chimodzi pa kona iliyonse ya chotengera. Chotengera chilichonse chinali ndi makona anayi. Zogwiriziza zake anaziumbira kumodzi ndi chotengeracho. 35  Pamwamba pa chotengeracho panali chokhazikapo beseni. Chokhazikapo besenicho chinali chozungulira, ndipo kutalika kwake kunali hafu ya mkono kuchokera pansi kufika pamwamba. Chokhazikapo besenicho anachipangira kumodzi ndi chotengeracho ndiponso ndi malata ake a m’mbali. 36  Komanso pamalata a m’mbali mwa chokhazikapo besenicho, ndi pazitsulo zimene zinali pakati pa malatawo, anajambulapo mochita kugoba+ akerubi, mikango, ndi mitengo yakanjedza malinga ndi kukula kwa malo ake. Anajambulanso mochita kugoba nkhata zamaluwa kuzungulira chokhazikapo besenicho.+ 37  Mmenemu ndi mmene zotengera 10+ zimenezo anazipangira. Zinali zoumbidwa chimodzimodzi,+ kukula kwake chimodzimodzi, ndiponso zooneka chimodzimodzi. 38  Kenako anapanga mabeseni 10+ amkuwa. Beseni lililonse linali lokwana mitsuko* 40, ndipo linali mikono inayi kukula kwake. Pachotengera chilichonse mwa zotengera 10 zija panali beseni limodzi. 39  Anaika zotengera zisanu mbali ya kudzanja lamanja kwa nyumbayo ndi zotengera zina zisanu mbali ya kumanzere kwa nyumbayo.+ Thanki ija anaiika mbali ya kudzanja lamanja kwa nyumbayo, kum’mawa chakum’mwera kwake.+ 40  M’kupita kwa nthawi Hiramu+ anapanga mabeseni,+ mafosholo+ ndi mbale zolowa.+ Kenako iye anamaliza+ ntchito yonse imene anali kugwirira Mfumu Solomo, yokhudza nyumba ya Yehova. 41  Anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa+ imene anaiika pamwamba pa zipilala ziwirizo, ndi maukonde awiri+ okutira mitu iwiri yozungulira imene inali pamwamba pa zipilalazo. 42  Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja, mizere iwiri ya makangaza pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija. 43  Anapanganso zotengera 10,+ mabeseni 10+ oika pazotengerazo, 44  thanki imodzi,+ ng’ombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo,+ 45  ndowa, mafosholo, mbale zolowa, ndi ziwiya zina zonse.+ Hiramu anapanga zinthu zimenezi ndi mkuwa wonyezimira. Anapangira Mfumu Solomo kuti aziike m’nyumba ya Yehova. 46  Mfumuyo inaumbira zinthu zimenezi m’chikombole chadongo, m’Chigawo* cha Yorodano,+ pakati pa Sukoti+ ndi Zeretani.+ 47  Solomo sanayeze ziwiya zonse+ chifukwa zinali zochuluka kwambiri.+ Mkuwawo sunadziwike kulemera kwake.+ 48  M’kupita kwa nthawi, Solomo anapanga ziwiya zonse za panyumba ya Yehova, za paguwa lansembe+ lagolide, ndi za patebulo+ limene ankaikapo mkate wachionetsero. 49  Anapanganso zoikapo nyale+ zagolide woyenga bwino,+ n’kukaziika pafupi ndi chipinda chamkati, zisanu mbali ya kudzanja lamanja, zisanu mbali ya kumanzere. Ndiponso anapanga maluwa+ agolide, nyale+ zagolide, zopanira+ zagolide zozimitsira nyale, 50  mabeseni, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa,+ makapu,+ ndi zopalira moto.+ Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso molowa miyendo ya zitseko+ za chipinda chamkati, kutanthauza Chipinda Choyera Koposa, ndiponso molowa miyendo ya zitseko+ za nyumbayo.+ Zonsezi zinali zagolide. 51  Pa mapeto pake, Mfumu Solomo inamaliza+ ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene inayenera kugwira. Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zonse zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Anatenga siliva, golide, ndi ziwiya zina n’kukaziika mosungira chuma cha panyumba ya Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena “zipinda” kapenanso “mitengo yapamwamba pa nsanamira.” M’Chiheberi anangoti “15.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Mawu ake enieni, “nyanja yosungunula.”
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
M’Malemba achiheberi mulibe nambala yake.
Onani Zakumapeto 12.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.