1 Mafumu 6:1-38

6  Tsopano Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova.+ Anayamba kuchita zimenezi m’chaka cha 480 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo,+ m’mwezi wachiwiri+ wa Zivi.+ Ichi chinali chaka chachinayi+ cha ulamuliro wake monga mfumu ya Isiraeli.  Nyumba imene Mfumu Solomo inamangira+ Yehova, m’litali mwake inali mikono* 60,+ m’lifupi mwake inali mikono 20, ndipo kutalika kwake inali mikono 30.+  Khonde+ la kutsogolo kwa chipinda chachikulu* cha nyumbayo linali mikono 20 m’litali, kufanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Khondelo linali kutsogolo kwa nyumbayo, ndipo linali mikono 10 m’lifupi mwake.  Nyumbayo anaiika mawindo. Mawindo ake anali aakulu mkati, aang’ono kunja.+  Komanso, anamanga zipinda kuzungulira khoma lonse la nyumbayo, kuzungulira makoma onse akunja a chipinda chachikulu ndi chipinda chamkati.+ Anamanga zipinda zam’mbali+ zosanjikizana kuzungulira nyumba yonseyo.  Chipinda cham’mbali chapansi chinali mikono isanu m’lifupi mwake. Chipinda cham’mbali chapakati chinali mikono 6 m’lifupi mwake, ndipo chipinda cham’mbali chachitatu chinali mikono 7 m’lifupi mwake. Makoma onse akunja a nyumbayo anangowagoba+ n’cholinga choti asawaboole.+  Nyumbayo anaimanga ndi miyala yosema+ kale, ndipo kulira kwa nyundo, nkhwangwa, kapena zida zilizonse zachitsulo sikunamveke m’nyumbayo+ pamene anali kuimanga.  Khomo lolowera+ kuchipinda cham’mbali chapansi linali kumanja kwa nyumbayo, ndipo ankakwera masitepe oyenda chokhotakhota kukafika kuchipinda chapakati. Kuchokera kuchipinda chimenechi, ankakwera n’kukafika kuchipinda chachitatu.  Anapitiriza kumanga nyumbayo kuti aimalize,+ ndipo mkati mwa nyumbayo anamangamo ndi matabwa ndi mitanda ya mitengo ya mkungudza.+ 10  Anamanga zipinda zam’mbali+ zosanjikizana kuzungulira nyumba yonseyo. Chipinda chilichonse chinali chotalika mikono isanu. Zipindazo anazilumikiza kunyumbayo ndi matabwa+ a mkungudza. 11  Pa nthawiyo, Yehova anauza Solomo+ kuti:+ 12  “Kunena za nyumba ukumangayi, ukayenda motsatira malamulo+ anga ndi kusunga zigamulo+ zanga zonse ndi kuzitsatira,+ inenso ndidzakwaniritsadi mawu anga okhudza iweyo amene ndinalankhula kwa bambo ako Davide.+ 13  Ndidzakhaladi pakati pa ana a Isiraeli,+ ndipo sindidzasiya anthu anga, Aisiraeli.”+ 14  Solomo anapitiriza kumanga nyumbayo kuti aimalize.+ 15  Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga* anakutamo ndi matabwa. Kenako anakuta pansi pa nyumbayo ndi matabwa akuluakulu a mitengo yofanana ndi mkungudza.+ 16  Komanso, anagawa chigawo cha mikono 20 kumbuyo kwa nyumbayo ndi matabwa a mkungudza, kuchokera pansi mpaka kudenga. Nyumbayo anaimangira chipinda chamkati,+ chotchedwa Malo Oyera Koposa.+ 17  Chipinda chachikulu kutsogolo+ kwa nyumbayo+ chinali mikono 40. 18  Pamatabwa a mkungudza a mkati mwa nyumbayo anajambulapo mochita kugoba zokongoletsera zooneka ngati zipanda+ ndi nkhata zamaluwa.+ Mkati monse munali matabwa a mkungudza ndipo simunkaoneka mwala uliwonse. 19  Iye anakonza mkati mwa chipinda chamkati+ cha nyumbayo kuti aikemo likasa+ la pangano+ la Yehova. 20  Chipinda chamkati chinali mikono 20 m’litali, mikono 20 m’lifupi+ ndi mikono 20 kutalika kwake. Chipindacho anachikuta ndi golide woyenga bwino,+ komanso anakuta guwa lansembe+ ndi matabwa a mkungudza. 21  Solomo anakuta+ mkati mwa nyumba yonseyo ndi golide woyenga bwino.+ Anatenga matcheni+ agolide ndi kuwadutsitsa kutsogolo kwa chipinda chamkati,+ n’kukuta chipindacho ndi golide. 22  Nyumba yonseyo anaikuta ndi golide+ mpaka kuimaliza, ndipo guwa lansembe lonse,+ lomwe linali kufupi ndi chipinda chamkati, analikuta ndi golide.+ 23  Komanso, m’chipinda chamkati anapangamo akerubi+ awiri kuchokera ku mtengo wamafuta.* Kerubi aliyense anali mikono 10 kutalika kwake.+ 24  Phiko limodzi la kerubi linali lalitali mikono isanu, ndipo phiko linalo linali lalitali mikono isanunso. Kuchokera kunsonga ya phiko lake limodzi kufika kunsonga ya phiko lake lina, kutalika kwake kunali kukwana mikono 10.+ 25  Kerubi wachiwiri anali wotalika mikono 10. Akerubi awiriwo anali ofanana kukula kwawo ndiponso kapangidwe kawo. 26  Kerubi mmodzi anali mikono 10 kutalika kwake, ndipo winayonso anali chimodzimodzi. 27  Kenako anaika akerubiwo m’chipinda chamkati, ndipo mapiko awo anali otambasula.+ Nsonga ya phiko la kerubi mmodzi inagunda khoma ndipo nsonga ya phiko la kerubi winayo inagundanso khoma lina. Mapiko awo anafika pakati pa nyumbayo, ndipo anagundana.+ 28  Kenako Solomo anakuta akerubiwo ndi golide.+ 29  Pamakoma onse a nyumbayo, m’zipinda zonse ziwiri, chamkati ndi chakunja, anajambulapo akerubi,+ mitengo ya kanjedza,+ ndi maluwa.+ Anajambula zinthu zimenezi mochita kugoba. 30  Pansi+ pa nyumbayo, m’zipinda zonse ziwiri, chamkati ndi chakunja, anakutapo ndi golide. 31  Pakhomo la chipinda chamkati anaikapo zitseko+ za mtengo wamafuta,+ zipilala za m’mbali, ndi mafelemu. Zimenezi zinali mbali yachisanu. 32  Zitseko ziwirizo zinali za matabwa a mtengo wa mafuta. Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza, ndi maluwa, ndipo anazikuta ndi golide. Kenako akerubi ndi mitengo ya kanjedza yolemba mochita kugoba ya pazitsekozo, anazikuta ndi golide. 33  Anapanganso zomwezo pakhomo la chipinda chachikulu, pamafelemu ake a mtengo wamafuta omwe anali ofanana mbali zonse kutalika kwake. 34  Zitseko ziwirizo zinali za matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza.+ Zitseko ziwiri za khomo limodzi zinkayenda pamiyendo yake, ndipo zitseko ziwiri za khomo linalo zinkayendanso pamiyendo yake.+ 35  Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza, ndi maluwa ndipo anakuta zojambulazo ndi golide.+ 36  Kenako anamanga khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu+ kuzungulira bwalo lamkati,+ ndipo anawonjezeranso mzere umodzi wa matabwa a mkungudza. 37  M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomo, m’mwezi wa Zivi,+ anamanga maziko+ a nyumba ya Yehova. 38  Ndipo m’chaka cha 11, m’mwezi wa Buli,* womwe ndi mwezi wa 8, anamaliza+ kumanga zinthu zonse panyumbayo motsatira mapulani ake onse.+ Motero, Solomo anatha zaka 7 akumanga nyumbayo.

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Mawu ake enieni, “kachisi,” mwina kutanthauza Malo Oyera.
Kapena kuti “kutsindwi.”
Mwina umenewu unali mtengo wa mtundu wa paini.
Onani Zakumapeto 13.