1 Mafumu 5:1-18

5  Hiramu+ mfumu ya ku Turo+ inatumiza atumiki+ ake kwa Solomo, pakuti inamva kuti iyeyo ndi amene anadzozedwa kulowa ufumu m’malo mwa bambo ake, popeza Hiramuyo ankamukonda Davide masiku ake onse.+  Kenako Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu, kuti:+  “Inuyo mukudziwa bwino kuti Davide bambo anga sanathe kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo+ zimene adani ake ankamenyana naye m’madera onse omuzungulira, mpaka pamene Yehova anaika adani akewo pansi pa mapazi ake.  Tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mpumulo pakati pa adani anga onse ondizungulira.+ Palibe amene akulimbana nane, ndipo palibe choipa chilichonse chimene chikuchitika.+  Panopa ndikuganiza zomanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga,+ monga momwe Yehova analonjezera Davide bambo anga kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamuike pampando wako wachifumu m’malo mwa iweyo, ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+  Tsopano lamulani kuti anthu andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga adzakhala limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzakupatsani malipiro a antchito anu malingana ndi zonse zomwe munganene. Inuyo mukudziwa bwino kuti pakati pathu palibenso anthu odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+  Hiramu+ atangomva mawu a Solomo, anasangalala kwambiri ndipo ananena kuti: “Yehova atamandike+ lero, popeza wapereka kwa Davide mwana wanzeru+ woti alamulire anthu ochulukawa.”+  Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo, kuti: “Ndamva uthenga wanu. Ineyo ndichita zonse zimene mukufuna pa nkhani ya mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza.+  Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni+ n’kutsikira nayo kunyanja, ndipo ineyo kumbali yanga ndidzaimanga pamodzi ngati phaka n’kuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze.+ Kenako ndidzauza anthu kuti aimasule, ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Ndipo inu mudzachita zofuna zanga pondipatsa chakudya cha banja langa.”+ 10  Choncho Hiramu anapereka kwa Solomo mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza, monga momwe Solomo anafunira. 11  Ndipo Solomo anapereka kwa Hiramu tirigu wokwana miyezo 20,000 ya kori,*+ kuti chikhale chakudya cha banja lake, ndiponso mafuta oyenga bwino kwambiri+ okwana miyezo 20 ya kori. Izi n’zimene Solomo ankapereka kwa Hiramu chaka ndi chaka.+ 12  Ndiyeno Yehova anapatsa Solomo nzeru monga mmene anam’lonjezera.+ Pakati pa Hiramu ndi Solomo panali mtendere, ndipo awiriwa anachita pangano. 13  Anthu amene Mfumu Solomo inawalemba ntchito yokakamiza anachokera ku Isiraeli konse, ndipo anthu olembedwa ntchito yokakamizawo+ anakwana amuna 30,000. 14  Inkawatumiza ku Lebanoni m’magulu a anthu 10,000 pamwezi. Kwa mwezi umodzi anthuwo ankakhala ku Lebanoni, ndipo kwa miyezi iwiri ankakhala kwawo.+ Adoniramu+ ndiye anali woyang’anira anthu olembedwa ntchito yokakamizawo.+ 15  Solomo anali ndi anthu+ 70,000 onyamula katundu,+ ndi ena 80,000 osema miyala+ kumapiri.+ 16  Kuwonjezera pa amenewa, panalinso akapitawo a nduna za Solomo+ oyang’anira ntchitoyo. Analipo akapitawo 3,300+ oyang’anira anthu amene anali kugwira ntchitoyo. 17  Ndiyeno mfumuyo inalamula kuti aseme miyala ikuluikulu yokwera mtengo,+ kuti akamange maziko+ a nyumbayo ndi miyala yosema.+ 18  Choncho amisiri omanga a Solomo ndi amisiri omanga a Hiramu ndiponso Agebala+ anasema miyalayo, ndipo anapitiriza kudula mitengo ndi kusema miyala pokonzekera kumanga nyumbayo.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Mf 4:22.