1 Mafumu 4:1-34

4  Mfumu Solomo inapitiriza kulamulira Isiraeli yense.+  Ndipo awa ndiwo akalonga+ amene inali nawo: Wansembe Azariya mwana wa Zadoki,+  Elihorefi ndi Ahiya, ana a Sisa, omwe anali alembi,+ ndi wolemba zochitika dzina lake Yehosafati,+ mwana wa Ahiludi.  Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mkulu wa asilikali,+ ndipo Zadoki ndi Abiyatara+ anali ansembe.  Azariya mwana wa Natani+ anali mkulu wa nduna, ndipo Zabudu mwana wa Natani anali wansembe, bwenzi+ la mfumu.  Ahisara anali woyang’anira banja lachifumu, ndipo Adoniramu,+ mwana wa Abada, anali woyang’anira anthu olembedwa ntchito yokakamiza.+  Solomo anali ndi nduna 12 mu Isiraeli yense, zomwe zinkabweretsa chakudya kwa mfumu ndi banja lake lachifumu. Nduna iliyonse inali ndi udindo wobweretsa chakudya kwa mwezi umodzi pachaka.+  Mayina a ndunazo anali awa: Mwana wa Hura, kudera lamapiri la Efuraimu,+  mwana wa Dekeri, amene ankayang’anira ku Makazi, ku Saalibimu,+ ku Beti-semesi,+ ndi ku Eloni-beti-hanani, 10  mwana wa Hesedi, ku Aruboti (dera lake linali Soko ndi dera lonse la Heferi),+ 11  mwana wa Abinadabu, kumapiri onse a Dori+ (Tafati mwana wa Solomo anadzakhala mkazi wake), 12  Baana mwana wa Ahiludi, ku Taanaki+ ndi ku Megido+ ndi ku Beti-seani+ konse, pafupi ndi Zeretani+ kumunsi kwa Yezereeli,+ kuchokera ku Beti-seani kukafika ku Abele-mehola+ mpaka kuchigawo cha Yokimeamu,+ 13  mwana wa Geberi ku Ramoti-giliyadi+ (dera lake linali midzi ing’onoing’ono ya Yairi+ mwana wa Manase, yomwe ili ku Giliyadi.+ Analinso ndi chigawo cha Arigobi,+ chomwe chili ku Basana.+ Kunali mizinda ikuluikulu 60 yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso mipiringidzo yamkuwa), 14  Ahinadabu mwana wa Ido, ku Mahanaimu,+ 15  Ahimazi ku Nafitali+ (nayenso anakwatira mwana wa Solomo, Basemati),+ 16  Baana mwana wa Husai, ku Aseri+ ndi ku Bealoti, 17  Yehosafati mwana wa Paruwa, ku Isakara,+ 18  Simeyi+ mwana wa Ela, ku Benjamini,+ 19  Geberi mwana wa Uri, ku Giliyadi,+ m’dera la Sihoni+ mfumu ya Aamori,+ ndi la Ogi+ mfumu ya Basana.+ Panalinso nduna imodzi yoyang’anira nduna zonse m’dzikomo. 20  Ayuda ndi Aisiraeli anachuluka kwambiri.+ Kuchuluka kwake anali ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja, ndipo anali kudya, kumwa, ndi kusangalala.+ 21  Solomo anakhala wolamulira wa maufumu onse kuyambira ku Mtsinje*+ mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo. Maufumu amenewa anali kubweretsa mphatso kwa Solomo ndi kum’tumikira masiku onse a moyo wake.+ 22  Chakudya cha kunyumba yachifumu ya Solomo tsiku lililonse chinkakhala ufa wosalala wokwana miyezo 30 ya kori,*+ ufa wamba wokwana miyezo 60 ya kori, 23  ng’ombe 10 zodyetsera m’khola, ng’ombe 20 zodyetsera kutchire, nkhosa 100, ndiponso mbawala zamphongo,+ insa,+ ngondo, ndi mbalame zoweta zonona. 24  Iye ankalamulira chilichonse kumbali yakuno ya Mtsinje,+ kuchokera ku Tifisa mpaka ku Gaza.+ Ankalamulira mafumu onse a mbali yakuno ya Mtsinje,+ ndipo m’zigawo zake zonse munali mtendere.+ 25  Ayuda+ ndi Aisiraeli anapitiriza kukhala mwabata.+ Aliyense anali pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+ kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba,+ masiku onse a Solomo. 26  Solomo anali ndi makola 40,000 a mahatchi+ okoka magaleta ake,+ ndi amuna 12,000 okwera pamahatchi. 27  Nduna+ zinkabweretsa chakudya cha Mfumu Solomo ndi cha aliyense wodyera limodzi ndi mfumuyo. Nduna iliyonse inkabweretsa chakudya kwa mwezi umodzi, ndipo inkaonetsetsa kuti pasakhale choperewera. 28  Ankabweretsanso balere ndi chakudya cha mahatchi okoka magaleta ndiponso cha mahatchi ena.+ Ankachipititsa kulikonse komwe chikufunika, aliyense malinga ndi udindo wake.+ 29  Mulungu anapitiriza kupatsa Solomo nzeru zopanda malire ndi luso lomvetsa zinthu losaneneka.+ Anam’patsanso mtima wozindikira zinthu mwakuya.+ 30  Nzeru za Solomo zinaposa+ nzeru za anthu onse a Kum’mawa+ ndi nzeru zonse za ku Iguputo.+ 31  Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense. Anali wanzeru kuposa Etani+ mwana wa Zera, Hemani,+ Kalikoli,+ ndi Darida ana a Maholi. Ndipo anatchuka m’mitundu yonse yozungulira.+ 32  Ankalankhula miyambi 3,000+ ndipo nyimbo zake+ zinakwana 1,005. 33  Ankafotokoza za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni+ mpaka kamtengo ka hisope+ kamene kamamera pakhoma.* Ankafotokozanso za zinyama,+ zolengedwa zouluka,+ nsomba,+ ndiponso za zokwawa.+ 34  Ndipo anthu ankabwera kuchokera ku mitundu yonse kudzamva nzeru za Solomo,+ ngakhalenso kuchokera kwa mafumu onse a padziko lapansi amene anamva za nzeru zake.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Eze 45:14.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”