1 Mafumu 3:1-28

3  Kenako Solomo anachita mgwirizano wa ukwati+ ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anatenga mwana wamkazi wa Faraoyo+ n’kubwera naye ku Mzinda wa Davide,+ kuti azikhala kaye kumeneko mpaka iye atamaliza kumanga nyumba yake,+ nyumba ya Yehova,+ ndi mpanda wozungulira Yerusalemu yense.+  Anthuwo anali kupereka nsembe pamalo okwezeka,+ chifukwa anali asanamange nyumba ya dzina la Yehova mpaka masiku amenewo.+  Solomo anapitiriza kukonda+ Yehova mwa kuyenda motsatira malamulo a Davide bambo ake,+ kungoti nthawi zonse anali kupereka nsembe zopsereza pamalo okwezeka.+  Chotero mfumu inapita ku Gibeoni+ kukapereka nsembe, chifukwa kumeneko ndiye kunali malo okwezeka ofunika kwambiri.+ Kumeneko, Solomo anapereka nsembe zopsereza zokwana 1,000 paguwa lansembe.+  Ku Gibeoniko, Yehova Mulungu anaonekera+ kwa Solomo m’maloto+ usiku ndipo anati: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikupatse.”+  Solomo atamva anati: “Inu mwasonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa mtumiki wanu Davide bambo anga, popeza anayenda pamaso panu m’choonadi ndi m’chilungamo+ ndiponso anali wowongoka mtima pamaso panu. Munapitiriza kumusonyeza kukoma mtima kosatha kumeneku moti munam’patsa mwana kuti lero akhale pampando wake wachifumu.+  Tsopano Yehova Mulungu wanga, mwaika mtumiki wanune kukhala mfumu m’malo mwa Davide bambo anga. Komatu ndine mwana+ ndipo sindikudziwa zinthu zambiri.+  Mtumiki wanune ndili pakati pa anthu anu amene mwawasankha,+ anthu ochuluka zedi amene sangatheke kuwerengeka chifukwa chochuluka.+  Mupatse mtumiki wanune mtima womvera kuti ndiweruze+ anthu anu, ndi kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa,+ pakuti ndani angathe kuweruza+ anthu anu ovutawa?”+ 10  Zimene anapempha Solomozi zinamusangalatsa Yehova.+ 11  Ndiyeno Mulungu anamuuza kuti: “Popeza wapempha zimenezi ndipo sunapemphe masiku ambiri, chuma,+ kapena moyo wa adani ako, koma wapempha kuti ukhale womvetsa zinthu kuti uzitha kuweruza milandu,+ 12  taona, ndichita mogwirizanadi ndi mawu ako.+ Ndithu ndikupatsa mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu+ moti ndi kale lonse sipanakhalepo munthu ngati iwe, ndipo pambuyo pako sipadzakhalanso wina ngati iwe.+ 13  Ndikupatsanso zomwe sunapemphe,+ chuma+ ndi ulemerero, moti sikudzakhalanso mfumu ngati iwe masiku ako onse.+ 14  Ndipo ukayenda m’njira zanga mwa kusunga malangizo ndi malamulo anga+ monga momwe Davide bambo ako anayendera,+ ndidzatalikitsanso masiku ako.”+ 15  Solomo atagalamuka,+ anazindikira kuti waona masomphenya. Kenako anapita ku Yerusalemu n’kukaimirira pamaso pa likasa+ la pangano la Yehova. Ndiyeno anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano+ n’kukonzera phwando+ atumiki ake onse.+ 16  Kenako akazi awiri omwe anali mahule+ anapita kwa mfumu n’kuima pamaso pake.+ 17  Mmodzi wa akaziwo anati: “Pepani mbuyanga,+ ine ndi mayi uyu tikukhala m’nyumba imodzi. Ineyo ndinabereka mwana wamwamuna pafupi naye m’nyumbamo. 18  Patapita masiku atatu kuchokera tsiku limene ine ndinabereka mwana, mayi uyu nayenso anabereka mwana wamwamuna. Ndipo tinali limodzi. M’nyumbamo munalibe munthu wina aliyense kupatulapo awirife. 19  Kenako mwana wa mayiyu anafa usiku chifukwa anam’tsamira. 20  Choncho kapolo wanune ndili m’tulo, mayiyu anadzuka pakati pa usiku n’kutenga mwana wanga amene anali pambali panga, n’kumuika pachifuwa pake. Ndiyeno anatenga mwana wake wakufayo n’kumuika pachifuwa panga. 21  Nditadzuka kuti ndiyamwitse+ mwana wanga, ndinapeza kuti anali wakufa. Choncho ndinamuyang’anitsitsa kwambiri m’mawa n’kuona kuti si mwana wanga amene ndinabereka.” 22  Koma mayi wina uja anati: “Ayi, mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!” Ndipo mayi woyamba uja anali kunena kuti: “Ayi, mwana wako ndi wakufayo, wanga ndi wamoyoyu.” Iwo anapitiriza kulankhula choncho pamaso pa mfumu.+ 23  Pomaliza mfumuyo inati: “Uyu akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!’ Ndipo uyo akuti, ‘Ayi, mwana wako ndi wakufayo, wanga ndi wamoyoyu!’” 24  Ndiyeno mfumuyo inati:+ “Amuna inu, ndibweretsereni lupanga.” Choncho anabweretsa lupanga pamaso pa mfumu. 25  Mfumuyo inati: “Amuna inu, dulani mwana wamoyoyu pakati. Mupereke hafu ya mwanayo kwa mayi mmodzi ndi hafu inayo kwa mayi winayo.” 26  Popeza mtima wa mayi yemwe mwana wake anali wamoyoyo unayamba kugunda kwambiri+ chifukwa cha mwana wakeyo,+ nthawi yomweyo anauza mfumuyo kuti: “Pepani+ mbuyanga! Amuna inu, m’patseni mayiyu mwana wamoyoyu. Musamuphe ayi.” Apa n’kuti mayi wina uja akunena kuti: “Mwanayu sakhala wanga kapena wako. Amuna inu, m’duleni!”+ 27  Mfumuyo itamva zimenezi inati: “Amuna inu, perekani mwana wamoyoyu kwa mayi uyu. Musamuphe ayi. Ameneyu ndiye mayi wake.” 28  Aisiraeli onse anamva za chigamulo+ chimene mfumu inapereka, ndipo anachita mantha chifukwa cha mfumuyo,+ popeza anaona kuti nzeru+ za Mulungu zinali mwa iye kuti azipereka zigamulo.

Mawu a M'munsi