1 Mafumu 22:1-53

22  Kwa zaka zitatu, panalibe nkhondo pakati pa Siriya ndi Isiraeli.  M’chaka chachitatucho, Yehosafati+ mfumu ya Yuda inapita kwa mfumu ya Isiraeli.  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza atumiki ake kuti: “Kodi mukudziwa kuti mzinda wa Ramoti-giliyadi+ ndi wathu? Koma tikuzengereza kuulanda m’manja mwa mfumu ya Siriya.”  Kenako inafunsa Yehosafati kuti: “Kodi upita nane kunkhondo ku Ramoti-giliyadi?”+ Yehosafati anayankha mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu ako ndi amodzi.+ Mahatchi anga n’chimodzimodzi ndi mahatchi ako.”  Komabe Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, umve kaye mawu a Yehova.”+  Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri pamodzi.+ Analipo amuna pafupifupi 400, ndipo inawafunsa kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena ndisapite?” Iwo anayankha kuti: “Pitani,+ ndipo Yehova akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”  Koma Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene watsala? Ngati alipo, tiyeni tifunsire kwa Mulungu kudzera mwa ameneyo.”+  Poyankha, mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Pali munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye,+ koma ineyo ndimadana naye kwambiri,+ chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa.+ Munthuyo dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Musalankhule choncho mfumu.”+  Chotero mfumu ya Isiraeli inaitana nduna ina ya panyumba ya mfumu,+ n’kuiuza kuti: “Kaitane Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye msangamsanga.”+ 10  Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anali atakhala pabwalo* la pachipata cha Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu.+ Pamaso pawo panali aneneri onse ndipo anali kuchita zinthu monga mmene aneneri amachitira.+ 11  Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Ndi nyanga izi mudzakankha Asiriya mpaka kuwatha.’”+ 12  Aneneri ena onse analinso kulosera zofanana ndi zomwezo, ndipo anali kunena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana. Yehova akaperekadi mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+ 13  Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Tamvera, mawu amene aneneri onse alankhula kwa mfumu ndi abwino. Nawenso mawu ako akakhale ngati mawu a mmodzi wa iwo, ndipo ukalankhule zabwino.”+ 14  Koma Mikaya anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ zimene Yehova anene kwa ine n’zimene ndikalankhule.”+ 15  Kenako anafika kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana. Mosakayikira, Yehova akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+ 16  Ndiyeno mfumuyo inamuuza kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti uzilankhula kwa ine zoona zokhazokha m’dzina la Yehova?”+ 17  Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika+ m’mapiri ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe atsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mu mtendere.’”+ 18  Mfumu ya Isiraeli itamva zimenezi inauza Yehosafati kuti: “Pajatu ndinakuuza kuti, ‘Adzalosera zoipa za ine, osati zabwino.’”+ 19  Mikaya anapitiriza kunena kuti: “Choncho imvani mawu a Yehova:+ Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu,+ makamu onse akumwamba ataimirira kudzanja lake lamanja ndi kumanzere kwake.+ 20  Kenako Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu, kuti apite ku Ramoti-giliyadi n’kukafa?’ Choncho uyu anayamba kunena zakutizakuti, uyunso n’kumanena zakutizakuti.+ 21  Pomalizira pake, mzimu wina+ unabwera kudzaima pamaso pa Yehova n’kunena kuti, ‘Ine ndikam’pusitsa.’ Ndipo Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukam’pusitsa motani?’+ 22  Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukam’pusitsadi ndipo zikakuyendera bwino.+ Pita kachite momwemo.’+ 23  Choncho Yehova waika mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anu onsewa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+ 24  Tsopano Zedekiya mwana wa Kenaana anayandikira Mikaya ndipo anam’menya mbama,+ n’kunena kuti: “Kodi mzimu wa Yehova wachoka bwanji kwa ine n’kukalankhula ndi iwe?”+ 25  Pamenepo Mikaya anati: “Udzadziwa zimenezo tsiku limene udzalowe m’chipinda chamkati+ kukabisala.”+ 26  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Tengani Mikaya mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu.+ 27  Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti:+ “Kam’tsekereni munthu uyu.+ Muzim’patsa chakudya chochepa+ ndi madzinso ochepa, kufikira ine nditabwerera mu mtendere.”’”+ 28  Pamenepo Mikaya ananena kuti: “Mukakabwereradi mu mtendere, ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Anatinso: “Imvani anthu nonsenu.”+ 29  Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 30  Tsopano mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha kuti ndisadziwike, ndipo ndimenya nawo nkhondo.+ Koma iweyo uvale zovala zako zachifumu.”+ Chotero mfumu ya Isiraeli inadzisintha+ n’kuyamba kumenya nawo nkhondo.+ 31  Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu ake 32+ oyang’anira asilikali okwera magaleta, kuti: “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamng’ono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.”+ 32  Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Ndithu iyi ndiyo mfumu ya Isiraeli.”+ Choncho anatembenuka kuti amenyane naye, koma Yehosafati anayamba kukuwa popempha thandizo.+ 33  Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, nthawi yomweyo anasiya kum’thamangitsa ndi kubwerera.+ 34  Ndiyeno munthu wina anakoka uta n’kuponya muvi wake chiponyeponye, koma analasa mfumu ya Isiraeli pampata umene unali pakati pa chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo, ndi zovala zake zina zodzitetezera. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti:+ “Tembenuza dzanja lako ndipo unditulutse m’bwalo lankhondoli, chifukwa ndavulala kwambiri.” 35  Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo, ndipo mfumuyo anaiimiritsa m’galeta moyang’anizana ndi Asiriya. Potsirizira pake inafa+ madzulo, ndipo magazi ochokera pachilonda chake anali kuyenderera mkati mwa galeta lankhondolo.+ 36  Kenako, dzuwa litatsala pang’ono kulowa, mumsasamo munamveka mfuu yaikulu, yakuti: “Aliyense azipita kumzinda wake, ndi kudziko lake!”+ 37  Chotero mfumuyo inafa. Ataibweretsa ku Samariya, anaiika m’manda ku Samariyako.+ 38  Kenako anayamba kutsuka galeta lankhondolo padziwe la ku Samariya ndipo agalu anayamba kunyambita magazi a mfumuyo,+ mogwirizana ndi mawu amene Yehova ananena.+ (Mahule ankasambanso padziwe limeneli.) 39  Nkhani zina zokhudza Ahabu ndi zochita zake zonse, komanso nyumba yaminyanga ya njovu+ imene anamanga, ndi mizinda yonse imene anamanga, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 40  Pomalizira pake Ahabu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Ahaziya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 41  Yehosafati+ mwana wa Asa anakhala mfumu ya Yuda m’chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya Isiraeli. 42  Yehosafati anali ndi zaka 35 pamene anayamba kulamulira. Iye analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba mwana wa Sili. 43  Yehosafati anayenda m’njira zonse za Asa bambo ake. Sanapatuke panjirazo, ndipo anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Koma sanachotse malo okwezeka. Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+ 44  Yehosafati anakhala mwamtendere ndi mfumu ya Isiraeli.+ 45  Nkhani zina zokhudza Yehosafati ndi zochita zake zamphamvu ndiponso momwe anamenyera nkhondo, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 46  Mahule aamuna a pakachisi+ amene anatsalira m’masiku a Asa bambo ake, Yehosafati anawachotsa m’dzikolo.+ 47  Pa nthawi imeneyo ku Edomu+ kunalibe mfumu. Nduna ndi imene inali kulamulira monga mfumu.+ 48  Yehosafati anapanga zombo za ku Tarisi+ kuti zizipita ku Ofiri kukatenga golide, koma sizinapite chifukwa zinasweka ku Ezioni-geberi.+ 49  Panali pa nthawi imeneyo pamene Ahaziya mwana wa Ahabu anapempha Yehosafati kuti: “Bwanji antchito anga apite pamodzi ndi antchito anu m’zombozo?” Koma Yehosafati anakana.+ 50  Pomalizira pake, Yehosafati anagona ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide+ kholo lake. Kenako Yehoramu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 51  Ahaziya+ mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya m’chaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 52  Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova. Anayenda m’njira ya bambo ake,+ m’njira ya mayi ake,+ ndiponso m’njira ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Isiraeli.+ 53  Ahaziya anapitiriza kutumikira Baala+ ndi kum’gwadira, ndipo anapitiriza kukwiyitsa+ Yehova Mulungu wa Isiraeli, malinga ndi zonse zimene bambo ake anachita.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “popunthira mbewu.”