1 Mafumu 21:1-29

21  Ndiyeno panali munda wa mpesa wa Naboti Myezereeli, umene unali ku Yezereeli,+ pafupi ndi nyumba yachifumu ya Ahabu mfumu ya Samariya.  Ahabu anauza Naboti kuti: “Ndipatse+ munda wako wa mpesawu+ kuti ukhale munda+ wanga woti ndizilimamo masamba,+ chifukwa uli pafupi ndi nyumba yanga. M’malo mwa munda wakowu ndikupatsa munda wina wa mpesa, wabwino kuposa umenewu. Ngati ungafune,+ ndiugula ndi ndalama.”  Koma Naboti anayankha Ahabu kuti: “Sindingachite zimenezo+ pamaso pa Yehova,+ kupereka cholowa cha makolo anga kwa inuyo.”+  Choncho Ahabu analowa m’nyumba mwake ali wachisoni ndi wokhumudwa chifukwa cha mawu amene Naboti Myezereeli anamuuza, onena kuti: “Sindikupatsani cholowa cha makolo anga.” Ndiyeno anakagona pabedi lake n’kutembenukira kukhoma,+ ndipo sanadye chakudya.  Kenako Yezebeli+ mkazi wake anabwera n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simukusangalala+ komanso simukudya chakudya?”  Ahabu anamuyankha kuti: “N’chifukwa chakuti ndinalankhula ndi Naboti Myezereeli kuti, ‘Ndigulitse munda wako wa mpesa. Kapena ngati ukufuna, ndikupatsa munda wina wa mpesa m’malo mwa umenewu.’ Koma anandiyankha kuti, ‘Sindikupatsani munda wanga wa mpesa.’”+  Ndiyeno Yezebeli mkazi wake anamuuza kuti: “Kodi muziwalamulira chonchi Aisiraeliwa?+ Dzukani, idyani chakudya, mtima wanu usangalale. Ineyo ndikupatsani munda wa mpesa wa Naboti Myezereeli.”+  Choncho Yezebeli analemba makalata+ m’dzina la Ahabu n’kuwadinda ndi chidindo cha Ahabu.+ Kenako anatumiza makalatawo kwa akulu+ ndi anthu olemekezeka amene anali kukhala mumzinda umodzi ndi Naboti.  M’makalatamo analembamo kuti:+ “Uzani anthu kuti asale kudya, ndipo muike Naboti patsogolo pa anthu onse. 10  Ndiyeno mupeze anthu awiri+ opanda pake+ adzakhale patsogolo pake ndi kupereka umboni wotsutsana naye.+ Adzanene kuti, ‘Iwe watemberera Mulungu ndi mfumu!’+ Kenako mukamutulutse kunja ndi kum’ponya miyala kuti afe.”+ 11  Choncho amuna a mumzinda wake, akulu ndi anthu olemekezeka amene anali kukhala mumzindawo, anachita zimene Yezebeli anawatuma, mogwirizana ndi zimene iye analemba m’makalata amene anawatumizira.+ 12  Iwo anauza anthu kuti asale kudya+ ndipo anauza Naboti kuti akhale patsogolo pa anthuwo. 13  Kenako amuna awiri opanda pake anabwera n’kukhala patsogolo pa Naboti. Ndiyeno amuna opanda pakewo anayamba kupereka umboni wotsutsana ndi Naboti pamaso pa anthuwo, wakuti: “Naboti watemberera Mulungu ndi mfumu!”+ Pambuyo pake anamutulutsira kunja kwa mzindawo n’kumuponya miyala mpaka anafa.+ 14  Atatero anatumiza uthenga kwa Yezebeli, wakuti: “Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa.”+ 15  Yezebeli atangomva kuti Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa, nthawi yomweyo anauza Ahabu kuti: “Nyamukani, katengeni munda wa mpesa wa Naboti Myezereeli+ umene anakana kukugulitsani uja, popeza Naboti salinso moyo koma wafa.” 16  Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, nthawi yomweyo ananyamuka n’kupita kumunda wa mpesa wa Naboti Myezereeli, kukautenga kuti ukhale wake.+ 17  Tsopano mawu a Yehova+ anafikira Eliya+ wa ku Tisibe, kuti: 18  “Nyamuka, pita ku Samariya+ ukakumane ndi Ahabu mfumu ya Isiraeli. Iye ali m’munda wa mpesa wa Naboti, ndipo wapita kumeneko kukautenga kuti ukhale wake. 19  Ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi wapha munthu+ n’kutenganso munda wake?”’+ Ukamuuzenso kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pamalo+ amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako, a iweyo.”’”+ 20  Ndiyeno Ahabu anafunsa Eliya kuti: “Wandipeza kodi mdani wanga?”+ Eliya anayankha kuti: “Inde ndakupezani. ‘Popeza watsimikiza mtima kuti uchite zoipa pamaso pa Yehova,+ 21  ndikubweretsera tsoka+ ndipo ndithu ndidzaseseratu nyumba yako,+ ndi kupha munthu aliyense wokodzera khoma+ wa m’banja la Ahabu, ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake mu Isiraeli. 22  Ndithu ndidzachititsa nyumba yako kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya, chifukwa chakuti wandikwiyitsa n’kuchimwitsanso Isiraeli.’+ 23  Komanso ponena za Yezebeli, Yehova wanena kuti, ‘Agalu adzamudya Yezebeli m’munda wa ku Yezereeli.+ 24  Munthu wa m’banja la Ahabu wofera mumzinda, agalu adzamudya, ndipo wofera kuthengo, mbalame zam’mlengalenga zidzamudya.+ 25  Palibenso munthu wina wofanana ndi Ahabu.+ Iye anadzipereka kuti achite zoipa pamaso pa Yehova ndiponso mkazi wake Yezebeli+ anamulimbikitsa+ kuchita zimenezo. 26  Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri mwa kutsatira mafano onyansa+ monga momwe Aamori, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, anachitira.’”+ 27  Ahabu atangomva mawu amenewa, anang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli.+ Iye anayamba kusala kudya, kugona pachiguduli ndipo anali kuyenda mwachisoni.+ 28  Ndiyeno mawu a Yehova anafikira Eliya wa ku Tisibe, kuti: 29  “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?+ Popeza wadzichepetsa chifukwa cha ine, sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake.+ M’malomwake, ndidzalibweretsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.”+

Mawu a M'munsi