1 Mafumu 20:1-43

20  Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya anasonkhanitsa gulu lake lonse lankhondo ndiponso mahatchi+ ndi magaleta.+ Atatero ananyamuka pamodzi ndi mafumu ena 32,+ n’kupita kukazungulira+ mzinda wa Samariya+ kuti amenyane nawo.  Kenako anatumiza amithenga+ kumzindawo, kwa Ahabu mfumu ya Isiraeli, kuti akamuuze kuti: “Beni-hadadi wanena kuti,  ‘Siliva ndi golide wako akhala wanga, ndipo akazi ako ndi ana ako aamuna ooneka bwino kwambiri, akhala anga.’”+  Pamenepo mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Mogwirizana ndi mawu anu mbuyanga mfumu, ine ndi zanga zonse tili m’manja mwanu.”+  Pambuyo pake amithenga aja anabweranso n’kudzanena kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, ‘Ndinakutumizira uthenga wonena kuti, “Undipatse siliva wako, golide wako, akazi ako, ndi ana ako aamuna.  Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatumiza atumiki anga kwa iwe. Iwo adzafufuza paliponse m’nyumba mwako ndi m’nyumba za atumiki ako, ndipo adzatenga chilichonse chamtengo wapatali+ kwa iwe.”’”  Mfumu ya Isiraeli itamva mawu amenewa, inaitanitsa akulu onse a m’dzikolo+ n’kuwauza kuti: “Taonani, munthu uyu akufuna kutibweretsera tsoka.+ Ananditumizira uthenga woti akufuna akazi anga, ana anga aamuna, siliva wanga, ndi golide wanga, ndipo ine sindinamukanize ayi.”  Pamenepo, akulu onse ndi anthu onse anauza mfumuyo kuti: “Musamvere zimenezo, ndipo musagwirizane nazo.”  Choncho Ahabu anauza amithenga a Beni-hadadi kuti: “Mukauze mbuyanga mfumu kuti, ‘Zonse zimene munandiuza poyamba paja, ine mtumiki wanu ndichita. Koma zimene mwanena kachiwirizi, sindingathe kuchita.’” Atumiki a Beni-hadadi aja atamva zimenezi, ananyamuka kukapereka uthengawo kwa mfumu yawo. 10  Tsopano Beni-hadadi anatumizira Ahabu uthenga wakuti: “Milungu+ yanga indilange mowirikiza,+ ngati fumbi la ku Samariya lidzakwanire kuti anthu onse onditsatira atape lodzaza manja.”+ 11  Mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Amuna inu mukamuuze kuti, ‘Musayambe kudzitama nkhondo isanayambe ngati kuti mwapambana kale nkhondoyo.’”+ 12  Beni-hadadi atangomva mawu amenewa, pamene iye ndi mafumu amene anali naye anali kumwa mowa+ m’misasa, anauza antchito ake kuti: “Konzekerani nkhondo!” Choncho iwo anayamba kukonzekera kukachita nkhondo ndi mzindawo. 13  Ndiyeno mneneri wina anapita kwa Ahabu mfumu ya Isiraeli,+ n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Kodi waona khamu lalikulu lonseli? Ndilipereka m’manja mwako lero, ndipo udziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+ 14  Ahabu anafunsa kuti: “Kudzera mwa ndani?” Mneneriyo anayankha kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kudzera mwa anyamata otumikira akalonga oyang’anira zigawo.’” Pomalizira Ahabu anafunsa kuti: “Ndani akayambitse nkhondoyo?” Mneneriyo anayankha kuti: “Inuyo!” 15  Ahabu anawerenga anyamata otumikira akalonga oyang’anira zigawo, ndipo anakwana 232.+ Atatha kuwerenga amenewa, anawerenga asilikali onse a ana a Isiraeli, omwe anakwana 7,000. 16  Iwo ananyamuka masana pamene Beni-hadadi anali kumwa ndi kuledzera+ m’misasa, pamodzi ndi mafumu ena 32 amene anali kumuthandiza aja. 17  Anyamata+ otumikira akalonga oyang’anira zigawo ndiwo anatsogolera. Iwo atangofika, Beni-hadadi anatumizako anthu ndipo anabwera kudzamuuza kuti: “Kwabwera anthu ochokera ku Samariya.” 18  Iye atamva anati: “Agwireni amoyo, kaya abwerera mtendere kapena abwerera nkhondo.”+ 19  Anali kunena za anyamata otumikira akalonga oyang’anira zigawo, amene anabwera kuchokera kumzinda pamodzi ndi gulu lankhondo limene linali m’mbuyo mwawo. 20  Kenako aliyense anayamba kupha mdani wake. Asiriyawo+ anayamba kuthawa+ ndipo Aisiraeli anawathamangitsa. Koma Beni-hadadi mfumu ya Siriya anathawa atakwera hatchi, pamodzi ndi amuna ena okwera pamahatchi. 21  Mfumu ya Isiraeli inawatsatira n’kumapha mahatchi ndi kuwononga magaleta+ awo, ndipo inapha Asiriya ochuluka zedi. 22  Pambuyo pake mneneri uja+ anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Pitani, kalimbitseni gulu lanu lankhondo+ ndi kuganizira zomwe mudzachite,+ popeza kumayambiriro kwa chaka chamawa mfumu ya Siriya ija idzabweranso kudzamenyana nanu.”+ 23  Atumiki a mfumu ya Siriya anauza mfumu yawo kuti: “Mulungu wawo ndi Mulungu wa mapiri.+ N’chifukwa chake anatiposa mphamvu, choncho tiyeni tikamenyane nawo m’chigwa tione ngati sitiwaposa mphamvu. 24  Tsopano muchite izi: Muchotse mafumu onse+ pa maudindo awo ndipo muike abwanamkubwa m’malo mwawo.+ 25  Inuyo musonkhanitse gulu lankhondo, chiwerengero chake chofanana ndi gulu limene linagonja lija. Chiwerengero cha mahatchi ndi magaleta chikhalenso chofanana ndi choyamba chija, ndipo tipite tikamenyane nawo m’chigwa kuti tikaone ngati sitikawaposa mphamvu.”+ Choncho mfumuyo inamvera mawu awo n’kuchitadi zimenezo. 26  Kumayambiriro kwa chaka, Beni-hadadi anasonkhanitsa Asiriya+ n’kupita ku Afeki+ kuti akamenyane ndi Aisiraeli. 27  Ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi n’kutenga zonse zofunikira+ ndipo ananyamuka kupita kukakumana nawo. Ana a Isiraeliwo anamanga msasa kutsogolo kwa Asiriya. Iwo anali ngati timagulu tiwiri ting’onoting’ono ta mbuzi pamene Asiriyawo anadzaza dziko lonse.+ 28  Kenako munthu wa Mulungu woona+ uja anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza Asiriya anena kuti: “Yehova ndi Mulungu wa mapiri, osati Mulungu wa zigwa,” ndipereka khamu lalikulu lonseli m’manja mwako,+ ndipo anthu inu mudziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+ 29  Magulu awiriwa anakhala moyang’anizana m’misasa masiku 7.+ Pa tsiku la 7 nkhondo inayambika, ndipo ana a Isiraeli anapha asilikali oyenda pansi a Asiriya okwanira 100,000 tsiku limodzi. 30  Anthu amene anatsala anathawira kumzinda wa Afeki,+ ndipo khoma linagwera amuna 27,000 amene anatsala.+ Beni-hadadi anathawa+ ndipo pomalizira pake anafika mumzindawo n’kulowa m’chipinda chamkati.+ 31  Ndiyeno atumiki ake anamuuza kuti: “Tamva kuti mafumu a nyumba ya Isiraeli ndiwo mafumu amene amasonyeza kukoma mtima kosatha.+ Tiyeni tivale ziguduli*+ m’chiuno mwathu+ ndi kumanga zingwe kumutu kwathu, kuti tipite kwa mfumu ya Isiraeli. Mwina sikakuphani.”+ 32  Choncho anavala ziguduli m’chiuno n’kumanga zingwe kumutu kwawo. Atatero anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kunena kuti: “Kapolo wanu Beni-hadadi wati, ‘Chonde musandiphe.’” Ahabu anati: “Kodi akadali ndi moyo? Amene uja ndi m’bale wanga.” 33  Choncho anthuwo+ anaona kuti chimenechi ndi chizindikiro choti zinthu zikhala bwino, ndipo atangomva zimenezi, anaona kuti mfumuyo ikunenadi zochokera mumtima mwake. Kenako anati: “Beni-hadadi ndi m’bale wanu.” Ahabu atamva zimenezi anati: “Pitani mukam’tenge.” Choncho Beni-hadadi anabwera kwa Ahabu ndipo nthawi yomweyo Ahabu anauza anthu kuti akweze Beni-hadadi m’galeta.+ 34  Tsopano Beni-hadadi anauza Ahabu kuti: “Ndibweza mizinda+ imene bambo anga analanda bambo anu, ndipo inuyo mutenga misewu ku Damasiko mofanana ndi mmene bambo anga anatengera misewu ku Samariya.” Ahabu anayankha kuti: “Tikapanga pangano+ loti udzachitadi zimenezi, ndikusiya kuti uzipita kwanu.” Atatero anachita naye pangano ndipo anamuuza kuti azipita kwawo. 35  Munthu wina wochokera pakati pa ana a aneneri,*+ pomvera mawu+ a Yehova anauza mnzake kuti: “Ndimenye!” Koma mnzakeyo anakana kum’menya. 36  Choncho mneneriyo anauza mnzakeyo kuti: “Popeza sunamvere mawu a Yehova, ukachoka pano ukumana ndi mkango ndipo ukupha ndithu.” Kenako mnzakeyo anachoka ndipo mkango+ unamupeza n’kumupha.+ 37  Ndiyeno anapita kwa munthu wina n’kumuuza kuti: “Ndimenye!” Munthuyo anam’menyadi mpaka kumuvulaza. 38  Kenako, mneneriyo anakaima m’mphepete mwa msewu n’kumakadikirira mfumu ija, atadzimanga kansalu kumaso kuti asadziwike.+ 39  Pamene mfumu inali kudutsa, mneneriyo analankhula mofuula kwa mfumuyo kuti:+ “Ine mtumiki wanu ndinapita pakatikati pa nkhondo. Munthu wina yemwe anali kuchoka kunkhondoko anandisungitsa munthu n’kundiuza kuti, ‘Uyang’anire munthu uyu. Akangosowa, moyo wako+ ulowa m’malo mwa moyo wake,+ apo ayi ulipira siliva wolemera talente* imodzi.’+ 40  Koma mtumiki wanune nditatanganidwa ndi zina, munthu uja anasowa.” Pamenepo mfumu ya Isiraeliyo inamuuza kuti: “Chiweruzo chako n’chomwecho. Wagamula wekha.”+ 41  Mfumuyo itangonena zimenezi, mneneriyo anachotsa msangamsanga kansalu kamene kanali kumaso kwake kaja, ndipo mfumu ya Isiraeliyo inamuzindikira kuti anali mmodzi wa aneneri.+ 42  Tsopano mneneriyo anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza wamasula munthu woyenera kuwonongedwa ndi ine,+ moyo wako ulowa m’malo mwake+ ndipo anthu ako alowa m’malo mwa anthu ake.’”+ 43  Mfumu ya Isiraeliyo itamva zimenezi, inanyamuka n’kumapita kunyumba kwake ili yachisoni ndi yokhumudwa,+ ndipo inafika ku Samariya.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”
Mawu akuti “ana a aneneri” mwina akutanthauza sukulu yopereka malangizo kwa aneneri, kapena bungwe la aneneri.
Onani Zakumapeto 12.