1 Mafumu 2:1-46

2  Davide atatsala pang’ono kumwalira,+ anaitana mwana wake Solomo n’kumulamula kuti:  “Ine ndatsala pang’ono kufa,+ choncho iweyo uchite zinthu mwamphamvu+ ndipo ukhale wolimba mtima.+  Uzimvera Yehova Mulungu wako mwa kuyenda m’njira zake,+ kusunga malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi maumboni* ake, malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Uzitero kuti udzakhale wanzeru m’zochita zako zonse, ndiponso kulikonse kumene udzapite.  Komanso kuti Yehova adzakwaniritse mawu ake okhudza ine amene analankhula,+ akuti, ‘Ana ako+ akadzasamalira njira zawo, mwa kuyenda+ mokhulupirika*+ pamaso panga ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+  “Iweyo ukudziwa bwino kwambiri zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichita,+ mwa kupha akulu awiri a asilikali a Isiraeli, Abineri+ mwana wa Nera ndi Amasa+ mwana wa Yeteri.+ Mwakutero, anakhetsa magazi+ ankhondo pa nthawi yamtendere. Ndipo anadetsa ndi magazi ankhondo lamba amene anali m’chiuno mwake ndiponso nsapato zimene zinali kuphazi kwake.  Iweyo uchite zinthu monga mwa nzeru zako,+ ndipo usalole kuti imvi zake zitsikire ku Manda*+ mwamtendere.+  “Ana a Barizilai+ Mgiliyadi uwasonyeze kukoma mtima kosatha. Azikhala pakati pa anthu odyera nawe limodzi patebulo,+ chifukwa anandithandiza+ pa nthawi imene ndinali kuthawa m’bale wako Abisalomu.+  “Taona, ukukhala pafupi ndi Simeyi+ wa ku Bahurimu,+ mwana wa Gera M’benjamini. Iyeyu ananditemberera temberero lopweteka+ tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu.+ Ndi iyeyu amene anabwera kudzakumana nane pa Yorodano,+ choncho ndinamulumbirira pamaso pa Yehova kuti: ‘Sindidzakupha ndi lupanga.’+  Tsopano usangomusiya, um’lange,+ poti ndiwe munthu wanzeru+ ndipo ukudziwa bwino zimene uyenera kumuchita. Utsitsire imvi zake+ ku Manda zili ndi magazi.”+ 10  Kenako Davide anagona limodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ 11  Davide analamulira Isiraeli zaka 40.+ Ku Heburoni+ analamulira zaka 7,+ ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.+ 12  Solomo anakhala pampando wachifumu wa Davide bambo ake,+ ndipo m’kupita kwa nthawi, ufumu wake unakhazikika.+ 13  Patapita nthawi, Adoniya mwana wa Hagiti anapita kwa Bati-seba,+ amayi a Solomo. Iwo atamuona, anam’funsa kuti: “Kodi mwabwerera mtendere?”+ Iye anayankha kuti: “Inde, ndabwerera mtendere.” 14  Kenako iye anapitiriza kuti: “Ndili nanu mawu.” Ndiyeno Bati-seba anati: “Lankhulani.”+ 15  Adoniya anapitiriza kuti: “Inu mukudziwa bwino kuti ufumu unayenera kukhala wanga, ndipo Aisiraeli onse maso awo anali pa ine kuti ndikhala mfumu.+ Koma ufumuwo unatembenuka n’kukhala wa m’bale wanga, chifukwa Yehova ndiye anam’patsa ufumuwo kuti ukhale wake.+ 16  Tsopano ndili ndi pempho limodzi kwa inu. Musandikanire pempho langa.”+ Choncho Bati-seba anamuyankha kuti: “Lankhulani.” 17  Adoniya anapitiriza kuti: “Chonde, mukauze Mfumu Solomo kuti andipatse Abisagi+ Msunemu+ akhale mkazi wanga. Ndikudziwa kuti inuyo sakakukanirani.” 18  Bati-seba atamva anati: “Chabwino. Ndikakulankhulirani kwa mfumu.” 19  Choncho Bati-seba anapita kwa Mfumu Solomo kuti akauze mfumuyo zofuna za Adoniya.+ Nthawi yomweyo mfumu inaimirira+ kuti ikumane naye ndipo inamuweramira.+ Kenako inakhala pampando wake wachifumu n’kuitanitsa mpando wina ndipo inauika kumbali yake yakumanja kuti amayi a mfumu akhalepo.+ 20  Ndiyeno Bati-seba anati: “Pali kanthu kakang’ono kamodzi kamene ndikufuna kupempha. Musandikanire pempho langa.” Mfumuyo inamuuza kuti: “Pemphani mayi anga, sindikukanirani.” 21  Choncho Bati-seba anapitiriza kuti: “Perekani Abisagi Msunemu kwa m’bale wanu Adoniya kuti akhale mkazi wake.” 22  Mfumu Solomo itamva zimenezi inafunsa mayi ake kuti: “N’chifukwa chiyani mukum’pemphera Adoniyayu Abisagi Msunemu? M’pemphereninso ufumu+ (chifukwa iye ndi mkulu wanga).+ Mupemphereni ufumu Adoniyayo. Mupempherenso wansembe Abiyatara+ ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya.”+ 23  Mfumu Solomo itatero, inalumbira pamaso pa Yehova kuti: “Mulungu andilange mowirikiza+ ngati Adoniya sanaike moyo wake pangozi mwa kupempha zimenezi.+ 24  Tsopano m’dzina la Yehova Mulungu wamoyo,+ amene wandichititsa kukhazikika,+ amene wandiika pampando wachifumu wa Davide bambo anga,+ ndiponso amene anandipatsa mzere wa banja lachifumu+ monga ananenera,+ lero Adoniya aphedwa.”+ 25  Nthawi yomweyo Mfumu Solomo inatumiza lamulo kudzera mwa Benaya+ mwana wa Yehoyada. Iye anapita kukakantha Adoniya, n’kumupha.+ 26  Kwa wansembe Abiyatara,+ mfumuyo inati: “Pita kuminda yako ku Anatoti+ chifukwa ukuyenera kufa.+ Koma lero sindikupha, poti unanyamula likasa la Yehova Ambuye Wamkulu Koposa+ pamaso pa Davide bambo anga,+ ndiponso chifukwa chakuti unavutika nthawi yonse imene bambo anga anavutika.”+ 27  Choncho Solomo anathamangitsa Abiyatara n’kumusiyitsa kutumikira monga wansembe wa Yehova, pokwaniritsa mawu amene Yehova analankhula ku Silo,+ otsutsana ndi nyumba ya Eli.+ 28  Nkhaniyo inam’fika Yowabu,+ ndipo iye anathawira kuchihema+ cha Yehova n’kukagwira nyanga za guwa lansembe.+ Paja Yowabu ankatsatira Adoniya,+ ngakhale kuti sanatsatire+ Abisalomu. 29  Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova, ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, kuti: “Pita ukamuphe!”+ 30  Benaya anapitadi kuchihema cha Yehova n’kukamuuza Yowabu kuti: “Mfumu yanena kuti, ‘Tuluka!’” Koma iye anati: “Ayi! Ndifera mom’muno.”+ Benaya atamva zimenezo anakauza mfumu kuti: “Yowabu wanena zimenezi, ndipo wandiyankha choncho.” 31  Mfumuyo inamuuza kuti: “Chita zimene wakuuzazo. Umuphe n’kumuika m’manda ndi kundichotsera ine ndi nyumba ya bambo anga magazi+ amene Yowabu anakhetsa+ popanda chifukwa. 32  Ukatero, Yehova adzabwezeradi pamutu pake magazi ake,+ chifukwa anakantha amuna awiri olungama ndi abwino kuposa iyeyo,+ ndipo anawapha ndi lupanga. Anachita zimenezi Davide bambo anga osadziwa.+ Amuna ake anali Abineri+ mwana wa Nera mkulu wa asilikali a Isiraeli,+ ndi Amasa+ mwana wa Yeteri mkulu wa asilikali a Yuda.+ 33  Magazi awo ayenera kubwerera pamutu pa Yowabu ndi pamutu pa mbumba yake mpaka kalekale.+ Koma kwa Davide,+ mbumba yake, nyumba yake, ndi mpando wake wachifumu, kudzakhala mtendere wochokera kwa Yehova mpaka kalekale.”+ 34  Kenako Benaya mwana wa Yehoyada anapita+ kuchihemako n’kukakantha Yowabu ndi kumupha,+ ndipo anaikidwa m’manda panyumba pake m’chipululu. 35  Zitatero, mfumu inaika Benaya+ mwana wa Yehoyada m’malo mwa Yowabu kuti akhale mkulu wa asilikali,+ ndipo inaika wansembe Zadoki m’malo mwa Abiyatara.+ 36  Pomaliza mfumu inatuma anthu kukaitana Simeyi,+ ndipo inamuuza kuti: “Udzimangire nyumba ku Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko. Usachoke kumeneko kupita kwina ndi kwina. 37  Zikadzachitika kuti tsiku lina wachoka n’kudutsa chigwa* cha Kidironi,+ udziwiretu kuti udzafa ndithu.+ Mlandu wa magazi ako udzakhala pamutu pako.”+ 38  Simeyi atamva zimenezi anauza mfumu kuti: “Mwanena bwino. Mmene mbuyanga mfumu mwanenera, ndi mmenenso mtumiki wanu achitire.” Ndipo Simeyi anakhala ku Yerusalemu masiku ambiri. 39  Pamapeto pa zaka zitatu, akapolo awiri+ a Simeyi anathawira kwa Akisi+ mwana wa Maaka, mfumu ya Gati.+ Kenako anthu anabwera kudzauza Simeyi kuti: “Tamvera! Akapolo ako ali ku Gati.” 40  Nthawi yomweyo, Simeyi anaimirira n’kukwera bulu wake kupita ku Gati kwa Akisi, kukafunafuna akapolo akewo. Choncho Simeyi anapita ku Gati n’kukabwerako ndi akapolo ake. 41  Ndiyeno Solomo anauzidwa kuti: “Simeyi anatuluka mu Yerusalemu kupita ku Gati, ndipo wabwerako.” 42  Mfumuyo itamva inatuma anthu kukaitana+ Simeyi. Atafika, inam’funsa kuti: “Kodi sindinakulumbiritse pamaso pa Yehova n’kukuchenjeza+ kuti, ‘Tsiku limene udzatuluke kunja n’kupita kwina ndi kwina, udziwiretu kuti udzafa ndithu’? Ndipo kodi iwe sunandiuze kuti, ‘Mawu mwanenawa ndi abwino’?+ 43  Nangano n’chifukwa chiyani sunasunge lumbiro limene unapanga pamaso pa Yehova,+ ndi lamulo limene ndinakulamula mwamphamvu?”+ 44  Ndiyeno mfumuyo inapitiriza kuuza Simeyi kuti: “Iweyo wekha ukudziwa bwino mumtima mwako zoipa zonse zimene unachitira Davide bambo anga.+ Yehova akubwezera ndithu pamutu pako zoipa zimene unachita.+ 45  Koma Mfumu Solomo idzadalitsidwa,+ ndipo mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika kwamuyaya pamaso pa Yehova.”+ 46  Itatero, mfumuyo inalamula Benaya mwana wa Yehoyada amene ananyamuka n’kukakantha Simeyi, ndipo anafa.+ Choncho ufumuwo unakhazikika m’manja mwa Solomo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “zikumbutso; zilimbikitso.”
Mawu ake enieni, “m’choonadi.”
Onani Zakumapeto 5.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.