1 Mafumu 19:1-21

19  Kenako Ahabu+ anauza Yezebeli+ zonse zimene Eliya anachita, ndiponso mmene anaphera aneneri onse ndi lupanga.+  Yezebeli atamva zimenezo, anatuma munthu kwa Eliya kuti akamuuze kuti: “Milungu yanga indilange+ mowirikiza,+ ngati pofika nthawi ino mawa sindidzachititsa moyo wako kukhala ngati moyo wa aliyense wa aneneriwo.”  Choncho Eliya anachita mantha moti ananyamuka n’kuyamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake,+ mpaka anakafika ku Beere-seba+ wa ku Yuda.+ Mtumiki wake anamusiya kumeneko,  ndipo iyeyo analowa m’chipululu n’kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake,+ ndipo anakhala pansi pake. Ndiyeno anayamba kupempha kuti afe, ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga+ Yehova, pakuti sindine woposa makolo anga.”  Kenako anagona pansi mpaka tulo tinam’peza pansi pa kamtengo kaja.+ Tsopano kunabwera mngelo+ amene anamukhudza,+ n’kumuuza kuti: “Dzuka udye.”  Atayang’ana, anaona kuti kumutu kwake kuli chikho cha madzi ndi mkate wozungulira+ uli pamiyala yotentha. Ndipo Eliya anayamba kudya ndi kumwa, kenako anagonanso.  Patapita kanthawi, mngelo+ wa Yehova uja anabweranso kachiwiri n’kumukhudza, ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye, popeza ulendowu wakukulira.”+  Choncho anadzuka ndipo anadya ndi kumwa. Atatero, anapeza mphamvu zokwanira moti anatha kuyenda masiku 40,+ usana ndi usiku, mpaka kukafika kuphiri la Mulungu woona la Horebe.+  Atafika kumeneko, analowa m’phanga+ kuti usiku agone mmenemo. Kenako anamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Ukufuna chiyani kuno Eliya?”+ 10  Iye anayankha kuti: “Ndachitira nsanje kwambiri+ inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe,+ ndipo apha aneneri anu ndi lupanga,+ moti ine ndatsala ndekhandekha.+ Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.”+ 11  Koma Mulungu anati: “Tuluka, kaime paphiri pamaso pa Yehova.”+ Kenako Yehova anadutsa,+ ndipo kunawomba chimphepo champhamvu chomwe chinali kung’amba mapiri ndi kuphwanya matanthwe pamaso pa Yehova.+ (Yehova sanali mumphepoyo.) Pambuyo pa chimphepocho, kunachita chivomezi.+ (Yehova sanali m’chivomezicho.) 12  Pambuyo pa chivomezicho, kunabuka moto.+ (Yehova sanali m’motowo.) Pambuyo pa motowo, panamveka mawu achifatse apansipansi.+ 13  Eliya atangomva mawuwo, nthawi yomweyo anaphimba nkhope yake ndi chovala chake,+ ndipo anatuluka kukaima pakhomo la phangalo. Pamenepo panamveka mawu olankhula naye, ndipo mawuwo anam’funsa kuti: “Ukufuna chiyani kuno Eliya?”+ 14  Iye anayankha kuti: “Ndachitira nsanje kwambiri inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.”+ 15  Kenako Yehova anamuuza kuti: “Nyamuka, bwerera udzere kuchipululu cha Damasiko.+ Pita ukadzoze+ Hazaeli+ kuti akhale mfumu ya Siriya. 16  Ukadzozenso Yehu+ mdzukulu wa Nimusi+ kuti akhale mfumu ya Isiraeli, ndipo Elisa+ mwana wa Safati wa ku Abele-mehola,+ ukam’dzoze kuti akhale mneneri m’malo mwa iwe.+ 17  Zomwe zidzachitike n’zakuti, wothawa lupanga la Hazaeli,+ adzaphedwa ndi Yehu,+ ndipo wothawa lupanga la Yehu, adzaphedwa ndi Elisa.+ 18  Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli,+ amene mawondo awo sanagwadirepo Baala,+ ndiponso pakamwa pawo sipanapsompsonepo Baala.”+ 19  Chotero Eliya anachoka kumeneko n’kupita kwa Elisa mwana wa Safati, ndipo anam’peza akulima ndi pulawo+ yokokedwa ndi ng’ombe ziwiri zamphongo. Panali mapulawo 12 oterowo ndipo pulawo yake inali kumbuyo kwa onsewo. Choncho Eliya anapita pamene panali Elisa n’kumuponyera chovala chake chauneneri.+ 20  Zitatero, Elisa anasiya ng’ombe zamphongozo n’kuthamangira Eliya ndipo anamuuza kuti: “Ndiloleni ndipite ndikapsompsone kaye bambo anga ndi mayi anga,+ kenako ndidzakutsatirani.” Eliya anamuyankha kuti: “Pita, sindingakuletse.” 21  Choncho anabwerera n’kutenga ng’ombe zamphongo ziwiri n’kuzipha.*+ Anatenga mitengo ya pulawo+ ya ng’ombezo n’kuphikira nyama yake. Kenako anaipereka kwa anthu kuti adye. Atatero, iye ananyamuka n’kutsatira Eliya ndipo anayamba kum’tumikira.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “n’kuzipereka nsembe.”