1 Mafumu 18:1-46

18  Patapita masiku ambiri,+ mawu a Yehova anafikira Eliya m’chaka chachitatu, kuti: “Pita ukaonekere kwa Ahabu, chifukwa ndikufuna kubweretsa mvula padziko lapansi.”+  Chotero Eliya anapita kukaonekera kwa Ahabu. Pa nthawiyi n’kuti njala itafika poipa kwambiri+ ku Samariya.  Pa nthawi imeneyo Ahabu anaitana Obadiya, yemwe anali woyang’anira banja la Ahabuyo.+ (Obadiya anali atasonyeza kuti anali munthu woopa Yehova kwambiri.+  Choncho pamene Yezebeli+ anapha aneneri a Yehova,+ Obadiya anatenga aneneri 100 n’kuwagawa m’magulu awiri, gulu lililonse aneneri 50. Atatero anakawabisa kuphanga ndipo anali kuwapatsa mkate ndi madzi.)+  Ndiyeno Ahabu anauza Obadiya kuti: “Pita m’dzikoli, ukayendere akasupe onse a madzi ndi zigwa* zonse. Mwina tikhoza kupeza udzu wobiriwira+ woti tidyetse mahatchi ndi nyulu, kuti nyamazi zisapitirize kufa.”+  Choncho anagawana koti aliyense alowere. Ahabu analowera njira ina, Obadiyanso analowera njira ina.+  Obadiya akuyenda, anangoona Eliya akubwera kudzakumana naye.+ Nthawi yomweyo anamuzindikira ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Kodi ndinu mbuyanga+ Eliya?”  Iye anamuyankha kuti: “Ndinedi. Pita ukanene kwa mbuye wako kuti,+ ‘Eliya wabwera.’”  Koma Obadiya anati: “Kodi ndachita tchimo lanji+ kuti mupereke mtumiki wanune m’manja mwa Ahabu kuti andiphe? 10  Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo,+ palibe mtundu kapena ufumu kumene mbuye wanga sanatumize anthu kuti akakufunefuneni. Akanena kuti, ‘Kuno kulibe,’ ankauza ufumuwo ndi mtunduwo kuti ulumbire kuti walephera kukupezani.+ 11  Kodi tsopano mukundiuza kuti, ‘Pita ukanene kwa mbuye wako kuti: “Eliya wabwera”’? 12  Zimene zichitike n’zakuti ine ndikasiyana nanu, mzimu+ wa Yehova ubwera n’kukutengani kupita nanu kwina kumene ine sindikukudziwa. Ineyo ndikhala nditamuuza kale Ahabu, koma iyeyo sadzakupezani choncho adzandipha ndithu.+ Komatu mtumiki wanune ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ubwana wanga.+ 13  Kodi mbuye wanga simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli anapha aneneri a Yehova? Ndinabisa aneneri 100 a Yehova m’phanga.+ Ndinawagawa m’magulu awiri a aneneri 50 gulu lililonse, ndipo ndinali kuwapatsa mkate ndi madzi.+ 14  Kodi tsopano mukunena kuti, ‘Pita, ukanene kwa mbuye wako kuti: “Eliya wabwera”’? Ndithu akandipha.”+ 15  Koma Eliya anati: “Pali Yehova wa makamu,+ Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira, lero ndionekera kwa Ahabu.” 16  Choncho Obadiya anapita kukakumana ndi Ahabu n’kumuuza zimenezi. Ndiyeno Ahabuyo anapita kukakumana ndi Eliya. 17  Ahabu atangomuona Eliya, anati: “Ndiwe eti! Iwe ndiwe munthu amene wachititsa kuti Isiraeli anyanyalidwe.”+ 18  Eliya anayankha kuti: “Ine sindinachititse kuti Isiraeli anyanyalidwe,+ koma inu ndi nyumba ya bambo anu ndi amene mwachititsa kuti anyanyalidwe,+ chifukwa anthu inu munasiya kutsatira malamulo a Yehova+ n’kuyamba kutsatira Abaala.+ 19  Tsopano tumizani uthenga ndipo musonkhanitse Aisiraeli onse kwa ine paphiri la Karimeli.+ Musonkhanitsenso aneneri 450 a Baala+ ndi aneneri 400 a mzati wopatulika,+ amene amadya patebulo la Yezebeli.”+ 20  Choncho Ahabu anatumiza uthenga kwa ana onse a Isiraeli, n’kusonkhanitsanso aneneri+ paphiri la Karimeli. 21  Kenako Eliya anayandikira anthu onsewo n’kunena kuti: “Kodi mukayikakayika* mpaka liti?+ Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni,+ koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatirani ameneyo.” Koma anthuwo sanamuyankhe chilichonse. 22  Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Ndilipo ndekha mneneri wa Yehova amene watsala,+ ndekhandekha basi, koma aneneri a Baala alipo 450. 23  Tsopano iwowo apeze ng’ombe zamphongo ziwiri zing’onozing’ono. Asankhepo ng’ombe imodzi n’kuiduladula. Ndiyeno aiike pankhuni koma asayatsepo moto. Ineyo ndikonza ng’ombe inayo n’kuiika pankhuni, koma sindiyatsapo moto. 24  Kenako muitane dzina la mulungu wanu.+ Inenso ndiitana dzina la Yehova, ndipo Mulungu amene ayankhe potumiza moto+ ndiye Mulungu woona.”+ Anthu onsewo atamva zimenezi anayankha kuti: “Zili bwino.” 25  Tsopano Eliya anauza aneneri a Baala kuti: “Yambani ndinu kusankha ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi ndi kuikonza, chifukwa mulipo ambiri. Muitane dzina la mulungu wanu koma musayatse moto.” 26  Choncho anatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo imene Eliya anawapatsa, n’kuikonza. Kenako anayamba kuitana dzina la Baala kuyambira m’mawa mpaka masana. Ankaitana kuti: “Inu a Baala, tiyankheni!” Koma sipanamveke mawu alionse,+ ndipo palibe anayankha.+ Iwo anapitiriza kudumphadumpha ngati akuvina, kuzungulira guwa lansembe limene anamanga. 27  Pofika masana Eliya anayamba kuwaseka+ ndipo anali kunena kuti: “Muitaneni mokuwa kwambiri chifukwa iye ndi mulungu.+ Mwina watanganidwa ndi zinazake, kapena wapita kuchimbudzi.+ Mwinanso wagona, ndipo muyenera kum’dzutsa.”+ 28  Iwo anayamba kuitana mokuwa kwambiri n’kumadzicheka+ ndi mipeni ndi mikondo ing’onoing’ono malinga ndi mwambo wawo, mpaka magazi anayamba kutuluka ndi kuyenderera pamatupi awo. 29  Iwo anapitiriza kuchita ngati aneneri+ mpaka dzuwa linapendeka. Anapitirizabe mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu, koma sipanamveke mawu alionse. Palibe anawayankha kapena kuwamvera.+ 30  Patapita nthawi, Eliya anauza anthu onsewo kuti: “Bwerani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo anabweradi. Kenako iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linagumuka.+ 31  Choncho Eliya anatenga miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Yakobo, yemwe mawu a Yehova anam’fikira,+ akuti: “Dzina lako lidzakhala Isiraeli.”+ 32  Ndi miyalayo, Eliya anamanga guwa lansembe+ kuti dzina la Yehova+ lilemekezedwe. Anakumbanso ngalande kuzungulira guwa lansembe lonselo. Ngalandeyo kukula kwake inali ngati malo amene angafesepo mbewu zokwana miyezo iwiri ya seya.* 33  Kenako anayalapo nkhuni,+ ndipo anaduladula ng’ombe yaing’ono yamphongo ija, n’kuiika pamwamba pa nkhunizo. Tsopano iye anati: “Tungani madzi odzaza mitsuko inayi ikuluikulu. Muwathire pansembe yopserezayo ndiponso pankhunizo.” 34  Kenako iye anati: “Thiraninso madzi ena.” Anthuwo anathiranso. Ndiyeno Eliya anati: “Thiraninso kachitatu.” Choncho anthuwo anathiranso kachitatu. 35  Chotero madziwo anayenderera pansi ponse paguwa lansembelo. Iye anathiranso madzi m’ngalande muja mpaka kudzaza. 36  Pa nthawi+ yopereka nsembe yambewu, Eliya mneneri anayandikira guwa lansembelo n’kunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Isiraeli,+ lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli,+ ndi kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+ 37  Ndiyankheni Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe kuti inu Yehova+ ndinu Mulungu woona, ndiponso kuti mwabweza mitima yawo.”+ 38  Atatero, moto+ wa Yehova unatsika n’kunyeketsa nsembe yopsereza+ ija, nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali m’ngalande muja.+ 39  Anthu onsewo ataona zimenezo, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo ananena kuti: “Yehova ndiye Mulungu woona! Yehova ndiye Mulungu woona!” 40  Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Gwirani aneneri a Baala! Muonetsetse kuti pasapezeke wothawa!” Nthawi yomweyo anawagwira, ndipo Eliya anatsetserekera nawo kuchigwa cha Kisoni,+ n’kukawapha kumeneko.+ 41  Tsopano Eliya anauza Ahabu kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa,+ chifukwa kukumveka mkokomo wa chimvula.”+ 42  Ahabu anapitadi kukadya ndi kukamwa. Koma Eliya anapita pamwamba pa phiri la Karimeli. Ndiyeno anakhala chogwada+ ataika nkhope yake pakati pa mawondo ake.+ 43  Kenako anauza mtumiki wake kuti: “Pita ukayang’ane mbali ya kunyanja.” Mtumikiyo anapita n’kukayang’anadi, ndiyeno anati: “Kulibe kalikonse.” Koma Eliya anamubweza n’kumuuza kuti, “Pita ukayang’anenso.” Anachita zimenezi mpaka maulendo 7.+ 44  Pa ulendo wa 7, mtumikiyo anati: “Taonani! Kuli kamtambo kakang’ono ngati chikhatho cha dzanja la munthu, ndipo kakukwera m’mwamba kuchokera m’nyanja.”+ Tsopano Eliya anauza mtumiki wakeyo kuti: “Pita ukauze Ahabu kuti, ‘Mangirirani mahatchi kugaleta,+ ndipo tsetserekani kuti chimvula chisakutsekerezeni.’” 45  Pa nthawiyo kumwamba kunachita mdima wa mitambo ndipo kunja kunawomba mphepo.+ Kenako kunayamba kugwa chimvula chambiri.+ Ahabu anali akuyenda pagaleta mpaka anakafika ku Yezereeli.+ 46  Dzanja la Yehova linali ndi Eliya,+ moti iye anakokera chovala chake m’chiuno n’kuchimanga,+ ndipo anayamba kuthamanga n’kupitirira Ahabu mpaka kukafika ku Yezereeli.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mawu ake enieni, “mudumphiradumphira maganizo awiri osiyana.”
Onani Zakumapeto 12.