1 Mafumu 17:1-24

17  Eliya+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi+ analankhula ndi Ahabu kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli+ amene ndimam’tumikira,+ sikugwa mame kapena mvula+ zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.”+  Kenako mawu+ a Yehova anafika kwa iye, akuti:  “Choka kuno, lowera chakum’mawa ukabisale+ m’chigwa* cha Keriti, chimene chili kum’mawa kwa Yorodano.  Uzikamwa+ madzi mumtsinje umene uli m’chigwacho, ndipo ndidzalamula akhwangwala+ kuti azikakupatsa chakudya.”+  Nthawi yomweyo, Eliya anachita mogwirizana ndi mawu a Yehova.+ Anapita kukakhala m’mphepete mwa chigwa cha Keriti chimene chili kum’mawa kwa Yorodano.  Akhwangwala ankamubweretsera mkate ndi nyama m’mawa ndi madzulo, ndipo iye ankamwa madzi mumtsinje umene unali m’chigwacho.+  Koma patapita masiku angapo, mtsinjewo unauma,+ chifukwa padziko lapansi sipanabwere mvula.  Tsopano mawu a Yehova anafika kwa iye, akuti:+  “Nyamuka, upite ku Zarefati+ m’dziko la Sidoni ukakhale kumeneko. Ine ndikalamula mayi wina wa kumeneko, mkazi wamasiye, kuti azikakupatsa chakudya.” 10  Chotero Eliya ananyamuka kupita ku Zarefati n’kulowa pachipata cha mzindawo. Kenako anaona mayi, mkazi wamasiye, akutola nkhuni. Ndiyeno anamuitana n’kumuuza kuti: “Undipatseko madzi pang’ono m’chikho kuti ndimwe.”+ 11  Atanyamuka kuti akatenge madziwo, anamuitananso n’kumuuza kuti: “Undibweretserekonso mkate pang’ono+ m’manja mwako.” 12  Atamva zimenezi mayiyo anati: “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo,+ ndilibe mkate,+ koma ufa pang’ono+ mumtsuko waukulu ndi mafutanso pang’ono+ mumtsuko waung’ono. Panopa ndikutola tinkhuni kuti ndipite kukaphika chakudya choti ineyo ndi mwana wanga tidye. Tikadya, tiziyembekezera kufa.”+ 13  Ndiyeno Eliya anamuuza kuti: “Usachite mantha.+ Pita ukachite mogwirizana ndi mawu ako. Koma pa zimene uli nazozo, ukayambe wandikonzera mtanda waung’ono wa mkate,+ n’kubwera nawo kwa ine. Kenako, ukakonze chakudya chako ndi cha mwana wako. 14  Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ufa umene uli mumtsuko waukulu siutha, ndipo mafuta amene ali mumtsuko waung’ono saatha, kufikira tsiku limene Yehova adzagwetse mvula padziko lapansi.’”+ 15  Choncho mayiyo anapita n’kukachita monga mmene Eliya ananenera. Ndipo iye, banja lake, ndi Eliya anadya kwa masiku ambiri.+ 16  Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe,+ ndipo mafuta amene anali mumtsuko waung’ono sanathe, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Eliya. 17  Pambuyo pa zimenezi, mwana wamwamuna wa mayi wa m’nyumbamo, anadwala. Matenda ake anakula kwambiri mpaka anamwalira.+ 18  Mayiyo ataona zimenezi, anauza Eliya kuti: “Ndili nanu chiyani+ inu munthu wa Mulungu woona? Mwabwera kwa ine kudzandikumbutsa cholakwa changa+ ndi kudzapha mwana wanga.” 19  Koma Eliya anauza mayiyo kuti: “Bweretsa kuno mwana wakoyo.” Ndiyeno anatenga mwanayo m’manja mwa mayi ake n’kupita naye kuchipinda chapadenga.+ Chipinda chimenechi n’chimene Eliya anali kukhalamo, ndipo anagoneka mwanayo pabedi lake.+ 20  Atatero, anayamba kufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga,+ kodi mukuchitiranso zoipa mkazi wamasiye amene ndikukhala naye monga mlendo wake, mwa kupha mwana wake?” 21  Ndiyeno anakumbatira mwanayo+ katatu ali pabedipo n’kufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo+ wa mwanayu ubwerere mwa iye.” 22  Kenako Yehova anamva mawu a Eliya,+ moti moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye, ndipo anakhala wamoyo.+ 23  Tsopano Eliya anatenga mwanayo n’kutsika naye kuchokera kuchipinda chapadenga chija, n’kumupereka kwa mayi ake. Ndiyeno anati: “Taona, mwana wako ali moyo.”+ 24  Mayiyo ataona zimenezi anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu+ ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.