1 Mafumu 16:1-34

16  Tsopano mawu a Yehova otsutsana ndi Basa anafikira Yehu+ mwana wa Haneni,+ kuti:  “Ngakhale kuti ndinakukweza kukuchotsa kufumbi+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli,+ iwe wayenda m’njira ya Yerobowamu+ n’kuchimwitsa anthu anga Aisiraeli mwa kundikwiyitsa ndi machimo awo.+  Tsopano ine ndidzaseseratu Basa ndi nyumba yake, ndipo ndidzachititsa nyumba yake kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati.+  Munthu aliyense wa m’banja la Basa amene adzafere mumzinda, agalu adzamudya ndipo amene adzafere kuthengo, mbalame zam’mlengalenga zidzamudya.”+  Nkhani zina zokhudza Basa ndi zimene anachita ndiponso zochita zake zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.  Pomalizira pake, Basa anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anamuika m’manda ku Tiriza.+ Kenako Ela mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.  Mawu a Yehova otsutsana ndi Basa ndi nyumba yake+ anafikira Yehu mwana wa Haneni mneneri. Mawuwo anali otsutsana naye chifukwa cha zoipa zonse zimene Basayo anachita pamaso pa Yehova mwa kumukwiyitsa+ ndi ntchito ya manja ake,+ ndiponso chifukwa chakuti iye anapha+ Nadabu. Mawuwo anali akuti nyumba yake idzakhala ngati nyumba ya Yerobowamu.  M’chaka cha 26 cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa anakhala mfumu ya Isiraeli ku Tiriza kwa zaka ziwiri.  Kenako mtumiki wake Zimiri,+ mkulu woyang’anira hafu ya magaleta, anayamba kum’konzera chiwembu. Anam’konzera chiwembucho pamene Ela anali kumwa+ mowa mpaka kuledzera kunyumba+ ya Ariza ku Tiriza. Ariza anali woyang’anira banja la mfumu ku Tirizako. 10  Ndiyeno Zimiri anafika n’kukantha+ Ela mpaka kumupha, ndipo iye anayamba kulamulira m’malo mwake. Zimenezi zinachitika m’chaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. 11  Iye atangokhala pampando wachifumu n’kuyamba kulamulira, anapha anthu onse a m’nyumba ya Basa. Sanasiye ndi moyo munthu aliyense wokodzera khoma+ wa m’banja la Basa kapena abale ake amene akanatha kubwezera magazi ake,+ kapenanso anzake. 12  Choncho Zimiri anafafaniza nyumba yonse ya Basa,+ malinga ndi mawu a Yehova+ otsutsana ndi Basa amene analankhula kudzera mwa Yehu mneneri.+ 13  Anawafafaniza chifukwa cha machimo onse a Basa ndi machimo amene Ela+ mwana wake anachita, ndiponso chifukwa cha machimo amene anachimwitsa nawo Aisiraeli. Iwo anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mafano awo opanda pake.+ 14  Nkhani zina zokhudza Ela ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 15  M’chaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anakhala mfumu ku Tiriza kwa masiku 7.+ Pa nthawiyo anthu anali atamanga msasa pafupi ndi mzinda wa Gebetoni,+ umene unali wa Afilisiti, kuti authire nkhondo. 16  Patapita nthawi, anthu mumsasawo anamva kuti: “Zimiri wachitira chiwembu mfumu ndipo waipha.” Choncho tsiku limenelo, Aisiraeli onse omwe anali kumsasako anaveka ufumu Omuri,+ mkulu wa asilikali, kuti akhale mfumu ya Isiraeli. 17  Kenako Omuri ndi Aisiraeli onse amene anali naye, anachoka ku Gebetoni n’kupita kukaukira+ mzinda wa Tiriza. 18  Zimiri atangoona kuti mzindawo walandidwa, anakalowa munsanja yomwe inali panyumba ya mfumu n’kuyatsa nyumbayo iye ali mkati mwake, moti anafera momwemo.+ 19  Anafa chifukwa cha machimo ake amene anachita mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndiponso mwa kuyenda m’njira ya Yerobowamu ndi m’tchimo limene iyeyo anachita mwa kuchimwitsa Isiraeli.+ 20  Nkhani zina zokhudza Zimiri ndi chiwembu chimene anakonza, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 21  Pa nthawi imeneyi m’pamene anthu a ku Isiraeli anayamba kugawikana m’magulu awiri.+ Gulu limodzi linayamba kutsatira Tibini mwana wa Ginati kuti amuveke ufumu, ndipo gulu linalo linayamba kutsatira Omuri. 22  Pomalizira pake, anthu amene anali kutsatira Omuri anagonjetsa otsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa, ndipo Omuri anayamba kulamulira. 23  M’chaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli ndipo analamulira zaka 12. Ku Tiriza analamulirako zaka 6. 24  Kenako anagula phiri la Samariya* kwa Semeri ndi matalente* awiri a siliva. Ndiyeno anayamba kumanga mzinda paphiripo n’kuutcha dzina la Semeri mbuye wa phirilo, loti Samariya.+ 25  Omuri anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anachita zoipa kwambiri kuposa onse amene anakhalapo iye asanakhale.+ 26  Iye anali kuyenda m’njira zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati,+ ndi m’tchimo lake limene anachimwitsa nalo Isiraeli mwa kukwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mafano awo opanda pake.+ 27  Nkhani zina zokhudza Omuri, zimene anachita ndi zochita zake zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 28  Pomalizira pake Omuri anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anamuika m’manda ku Samariya. Kenako Ahabu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 29  Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli m’chaka cha 38 cha Asa mfumu ya Yuda. Iye analamulira Isiraeli ku Samariya+ zaka 22. 30  Ahabu mwana wa Omuri anachita zoipa kwambiri pamaso pa Yehova kuposa onse amene anakhalapo iye asanakhale.+ 31  Komanso, ngati kuti kuyenda m’machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati inali nkhani yaing’ono,+ Ahabu anakwatira+ Yezebeli+ mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni,+ ndipo anayamba kukatumikira Baala+ ndi kum’gwadira. 32  Kuwonjezera apo, anamanga guwa lansembe la Baala m’kachisi+ wa Baala amene iye anamanga ku Samariya. 33  Ahabu anaimikanso mzati wopatulika,+ ndipo iye anachita zinthu zambiri zokwiyitsa+ Yehova Mulungu wa Isiraeli kuposa mafumu onse a Isiraeli amene anakhalapo iye asanakhale. 34  M’masiku ake, Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko. Atangoyala maziko ake, Abiramu mwana wake woyamba anafa, ndipo atangoika zitseko zake za pachipata, Segubu mwana wake wotsiriza anafa. Izi zinachitika mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “Samariya” akutanthauza kuti “la Fuko la Semeri.”
Onani Zakumapeto 12.