1 Mafumu 15:1-34

15  M’chaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu+ mwana wa Nebati,+ Abiyamu anakhala mfumu ya Yuda.+  Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu.*+  Abiyamu anapitiriza kuyenda m’machimo onse amene bambo ake anachita. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu+ ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+  Chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anam’patsa nyale+ mu Yerusalemu mwa kukweza mwana wake pambuyo pake, ndiponso kuchititsa kuti Yerusalemu akhalepobe.+  Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo sanapatuke pa chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake,+ kupatulapo pa nkhani ya Uriya Mhiti.+  Pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu pankachitika nkhondo masiku onse a moyo wa Rehobowamu.+  Nkhani zina zokhudza Abiyamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. Pakati pa Abiyamu ndi Yerobowamu, panachitikanso nkhondo.+  Pomalizira pake, Abiyamu anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Asa+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.  M’chaka cha 20 cha Yerobowamu mfumu ya Isiraeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda. 10  Analamulira ku Yerusalemu zaka 41. Agogo ake aakazi dzina lawo linali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu.+ 11  Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake.+ 12  Choncho iye anachotsa mahule aamuna a pakachisi m’dzikolo,+ ndiponso mafano onse onyansa*+ amene makolo ake anapanga.+ 13  Anachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu,+ chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri+ lopembedzera mzati wopatulika. Pambuyo pake Asa anagwetsa fanolo n’kukalitentha+ m’chigwa* cha Kidironi.+ 14  Koma iye sanachotse+ malo okwezeka.+ Komabe, Asa anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu masiku ake onse.+ 15  Iye anayamba kubweretsa kunyumba ya Yehova zinthu zimene bambo ake anaziyeretsa, komanso zinthu zimene iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide, ndi ziwiya zina.+ 16  Pakati pa Asa ndi Basa+ mfumu ya Isiraeli, panali kuchitika nkhondo masiku awo onse. 17  Choncho Basa mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda. Kenako anayamba kumanga mpanda wolimba kwambiri kuzungulira mzinda wa Rama,+ kuti anthu asamapite kwa Asa mfumu ya Yuda kapena kubwera kuchokera kwa Asa.+ 18  Asa ataona zimenezi anatenga siliva ndi golide yense amene anatsala pa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi pa chuma cha m’nyumba ya mfumu, n’kumupereka kwa atumiki ake. Kenako Mfumu Asa inatumiza atumiki akewo kwa Beni-hadadi+ mwana wa Tabirimoni, mwana wa Hezioni, mfumu ya Siriya,+ amene anali kukhala ku Damasiko.+ Inawatuma kuti akamuuze Beni-hadadi kuti: 19  “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Taona, ndakutumizira mphatso+ ya siliva ndi golide. Bwera udzaphwanye pangano lako ndi Basa mfumu ya Isiraeli kuti achoke kwa ine.”+ 20  Choncho Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a gulu lake lankhondo kuti akamenyane ndi mizinda ya Isiraeli. Iwo anawononga mizinda ya Iyoni,+ Dani,+ Abele-beti-maaka,+ ndi Kinereti yense mpaka dziko lonse la Nafitali.+ 21  Basa atangomva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama+ ndipo anapitiriza kukhala ku Tiriza.+ 22  Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse,+ moti palibe amene sanaitanidwe, ndipo iwo anatenga miyala ya ku Rama ndi matabwa ake, zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa inatenga zinthu zimenezo n’kuyamba kukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini, ndi mzinda wa Mizipa.+ 23  Nkhani zina zonse zokhudza Asa, ndi zochita zake zonse zamphamvu, ndiponso zonse zimene anachita, ndi mizinda imene anamanga, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. Koma mu ukalamba wake,+ mapazi ake anachita matenda.+ 24  Pomalizira pake, Asa anagona ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake.+ Ndiyeno Yehosafati+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 25  Nadabu+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli m’chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo anapitiriza kulamulira Isiraeli kwa zaka ziwiri. 26  Iye anali kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova, ndipo anapitiriza kutsatira njira ya bambo ake+ ndi machimo awo amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 27  Ndiyeno Basa+ mwana wa Ahiya wa nyumba ya Isakara, anayamba kuchitira chiwembu Nadabu. Iye anapha Nadabu kumzinda wa Gebetoni,+ womwe unali m’manja mwa Afilisiti, pa nthawi imene Nadabu ndi Aisiraeli onse anali kuukira Gebetoni. 28  Choncho Basa anapha Nadabu m’chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 29  Basa atangokhala mfumu, anapha anthu onse a m’nyumba ya Yerobowamu. Sanasiye wa m’banja la Yerobowamu aliyense ali ndi moyo kufikira atawatha onse, malinga ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Ahiya Msilo.+ 30  Izi zinachitika chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita,+ ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli, komanso chifukwa cha zinthu zokwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli zimene Yerobowamu anachita.+ 31  Nkhani zina zokhudza Nadabu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 32  Pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Isiraeli pankachitika nkhondo masiku awo onse.+ 33  M’chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Basa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Isiraeli yense ku Tiriza kwa zaka 24.+ 34  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndiponso anapitiriza kuyenda m’njira ya Yerobowamu+ ndi m’tchimo lake limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Pa 2Mb 11:20, 21, akutchedwa Abisalomu.
Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.