1 Mafumu 14:1-31

14  Pa nthawi imeneyo, Abiya mwana wamwamuna wa Yerobowamu anadwala.+  Choncho Yerobowamu anauza mkazi wake kuti: “Nyamuka, udzisinthe+ kuti anthu asadziwe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu ndipo upite ku Silo. Kumeneko n’kumene kuli mneneri Ahiya.+ Ameneyo ndiye anandiuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthuwa.+  Utenge mitanda 10 ya mkate,+ makeke, ndi botolo+ la uchi, ndipo ukafike kwa iyeyo.+ Iye ndiye akakuuze zimene zichitikire mnyamatayu.”+  Mkazi wa Yerobowamu anachitadi zimenezo. Choncho ananyamuka kupita ku Silo+ n’kukafika kunyumba kwa Ahiya. Ahiyayo sankatha kuona chifukwa maso ake anachita khungu ndi ukalamba.+  Yehova anali atauza Ahiya kuti: “Kukubwera mkazi wa Yerobowamu kudzakufunsa za mwana wake, chifukwa mwanayo akudwala. Umuuze zakutizakuti. Zomwe zichitike n’zakuti, akangofika adzisintha kuti asadziwike.”+  Choncho Ahiya atangomva phokoso la mapazi a mkazi wa Yerobowamu pamene anali kulowa pakhomo, anayamba kulankhula kuti: “Lowa mkazi wa Yerobowamu.+ N’chifukwa chiyani ukudzisintha kuti usadziwike pamene ine ndatumidwa kwa iwe ndi uthenga wopweteka?  Pita, kauze Yerobowamu kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndinakukweza pakati pa anthu ako, kuti ndikuike kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli,+  ndipo ndinang’amba+ ufumuwo kuuchotsa kunyumba ya Davide ndi kuupereka kwa iwe, koma iwe sunakhale ngati Davide mtumiki wanga. Iyeyo anasunga malamulo anga ndi kunditsatira ndi mtima wake wonse mwa kuchita zinthu zoyenera zokhazokha m’maso mwanga.+  Koma iweyo unayamba kuchita zinthu zoipa kwambiri kuposa onse amene anakhalapo iwe usanakhale. Unadzipangiranso mulungu wina+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula+ kuti undikwiyitse,+ ndipo wandikankhira ineyo kumbuyo kwako.+ 10  Pa chifukwa chimenechi, ndibweretsa tsoka panyumba ya Yerobowamu. Ndithu ndidzapha munthu aliyense wokodzera khoma*+ wa m’nyumba ya Yerobowamu, ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake mu Isiraeli.+ Komanso ndidzaseseratu nyumba ya Yerobowamu,+ monga momwe munthu amasesera ndowe mpaka atakazitaya.+ 11  Munthu wa m’banja la Yerobowamu wofera mumzinda, agalu adzamudya,+ ndipo wofera kuthengo, mbalame zam’mlengalenga zidzamudya,+ chifukwa choti Yehova wanena.”’ 12  “Iweyo nyamuka pita kunyumba kwako. Mapazi ako akakangolowa mumzinda, mwanayo akamwalira ndithu. 13  Ndipo Aisiraeli onse akamulira+ ndi kumuika m’manda. Iwo akamulira popeza m’banja lonse la Yerobowamu, uyu yekha ndiye adzaikidwe m’manda chifukwa chakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli, wapeza chinachake chabwino mwa yekhayu m’nyumba yonse ya Yerobowamu.+ 14  Yehova adzaika yekha mfumu+ ina yolamulira Isiraeli, yomwe idzafafanize nyumba ya Yerobowamu tsiku limenelo, ndipo ngati atafuna akhoza kuchita zimenezi pompano.+ 15  Yehova adzawonongadi Isiraeli, ndipo zidzakhala ngati mmene bango limagwedezekera m’madzi,+ ndiponso adzazuladi+ Aisiraeli, kuwachotsa padziko labwinoli+ limene anapatsa makolo awo. Ndiyeno adzawabalalitsira+ kutsidya lina la Mtsinje,*+ popeza iwo anapanga mizati yawo yopatulika,+ n’kukwiyitsa+ nayo Yehova. 16  Iye adzasiya Isiraeli+ chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita, ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli.”+ 17  Atamva zimenezi, mkazi wa Yerobowamu ananyamuka n’kumapita ndipo anafika ku Tiriza.+ Atangofika pakhomo la nyumba yawo, mnyamatayo anamwalira. 18  Choncho anamuika m’manda ndipo Aisiraeli onse anamulira, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya. 19  Nkhani zina zokhudza Yerobowamu, momwe anamenyera nkhondo+ ndi momwe analamulirira, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 20  Yerobowamu analamulira zaka 22, kenako anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Nadabu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 21  Rehobowamu+ mwana wa Solomo anali atakhala mfumu ku Yuda. Rehobowamu anali ndi zaka 41 pamene anayamba kulamulira, ndipo kwa zaka 17 analamulira ku Yerusalemu, mzinda+ umene Yehova anasankha pakati pa mafuko onse+ a Isiraeli kuti aike dzina lake kumeneko.+ Mayi ake dzina lawo linali Naama Muamoni.+ 22  Ayuda anapitiriza kuchita zoipa m’maso mwa Yehova,+ moti anamuchititsa+ nsanje kuposa mmene makolo awo anamuchititsira nsanje ndi machimo awo onse amene makolowo anachita.+ 23  Ndipo nawonso anapitiriza kudzimangira malo okwezeka,+ zipilala zopatulika,+ ndi mizati yopatulika+ pamwamba pa phiri lililonse lalitali,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+ 24  Ngakhalenso mahule aamuna a pakachisi ankapezeka m’dzikomo.+ Anthuwo anachita zinthu zonse zonyansa zimene inkachita mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+ 25  Ndiyeno m’chaka chachisanu cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki+ mfumu ya Iguputo anaukira Yerusalemu. 26  Iye anatenga chuma cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse+ kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+ 27  Choncho Mfumu Rehobowamu inapanga zishango zamkuwa m’malomwake, ndipo inazipereka kwa akulu a asilikali othamanga,+ omwe anali alonda a pakhomo la nyumba ya mfumu, kuti aziziyang’anira.+ 28  Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikali othamangawo ankanyamula zishangozo, ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda.+ 29  Nkhani zina zokhudza Rehobowamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’nthawi ya mafumu a Yuda. 30  Ndipo nkhondo inkachitika nthawi zonse pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.+ 31  Pomalizira pake, Rehobowamu anagona ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Mayi ake dzina lawo linali Naama Muamoni.+ Kenako Abiyamu+ mwana wa Rehobowamu anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Mawuwa ndi mkuluwiko wachiheberi wotanthauza mwamuna.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.