1 Mafumu 13:1-34

13  Tsopano panali munthu+ wa Mulungu amene anatumidwa+ ndi Yehova kuchokera ku Yuda kupita ku Beteli. Kumeneko iye anapeza Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa lansembe+ kuti afukize nsembe yautsi.+  Ndiyeno anafuulira guwa lansembelo mawu ochokera kwa Yehova oitanira tsoka, kuti: “Guwa lansembe iwe! Guwa lansembe iwe! Yehova wanena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake Yosiya.+ Ndithu adzatenga ansembe a malo okwezeka amene akufukiza nsembe yautsi pa iwe, n’kuwapereka nsembe pa iwe. Iye adzawotcha mafupa a anthu pa iwe.’”+  Kenako munthu wa Mulunguyo anapereka chizindikiro cholosera zam’tsogolo+ pa tsikulo. Iye anati: “Nachi chizindikiro cholosera zam’tsogolo chimene Yehova wanena: Guwa lansembeli ling’ambika pakati, ndipo phulusa losakanizika ndi mafuta limene lili paguwali litayika.”  Mfumu Yerobowamu itangomva mawu oitanira tsoka amene munthu wa Mulunguyo ananena kwa guwa lansembe la ku Beteli, nthawi yomweyo inatambasula dzanja lake kulichotsa paguwa lansembe, n’kunena kuti: “Amuna inu, m’gwireni uyu!”+ Itangotero dzanja limene inatambasula kuloza munthu wa Mulungu uja linauma, ndipo sinathenso kulibweza.+  Guwa lansembelo linang’ambika pakati moti phulusa losakanizika ndi mafuta linatayika kuchokera paguwalo. Izi zinachitika mogwirizana ndi chizindikiro cholosera zam’tsogolo chimene munthu wa Mulungu woonayo anapereka, malinga ndi mawu a Yehova.+  Tsopano mfumuyo inauza munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Chonde! Khazikani pansi mtima wa Yehova Mulungu wanu. Mundipempherere kuti dzanja langa libwerere mwakale.”+ Choncho munthu wa Mulungu woona uja anakhazikadi pansi+ mtima wa Yehova, moti dzanja la mfumu linabwerera mwakale, n’kukhala ngati mmene linalili poyamba.+  Kenako mfumuyo inauza munthuyo kuti: “Tiyeni kunyumba mukadye chakudya,+ ndiponso ndikakupatseni mphatso.”+  Koma munthu wa Mulungu woona uja anayankha mfumuyo kuti: “Ngakhale mutandipatsa hafu ya nyumba yanu,+ sindingapite nanu+ kukadya chakudya kapena kumwa madzi kwanu kuno.  Chifukwa mawu a Yehova andilamula kuti: ‘Usakadye chakudya+ kapena kumwa madzi, ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.’” 10  Iye anadutsadi njira ina. Sanadutse njira imene anadzera popita ku Beteliko. 11  Ndiyeno panali mneneri wina wokalamba+ yemwe anali kukhala ku Beteli. Ana ake anabwera n’kuyamba kumufotokozera zonse zimene munthu wa Mulungu woona uja anachita pa tsikulo ku Beteli. Anamuuzanso mawu amene munthuyo anauza mfumu. 12  Pamenepo bamboyu anafunsa anawo kuti: “Munthuyo wadzera njira iti?” Anawo analozera bamboyu njira imene munthu wa Mulungu woona wochokera ku Yuda uja anadzera. 13  Kenako bamboyu anauza anawo kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Anawo anawamangiradi chishalocho,+ ndipo iwo anakwera buluyo. 14  Atatero, analondola munthu wa Mulungu woona uja, ndipo anam’peza atakhala pansi pa mtengo waukulu.+ Ndiyeno anafunsa munthuyo kuti: “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu woona amene wachokera ku Yuda?”+ Munthuyo anayankha kuti: “Ndine amene.” 15  Kenako anamuuza munthuyo kuti: “Tiye kunyumba ukadye chakudya.” 16  Koma munthuyo anati: “Sindingabwerere nanu kapena kupita kunyumba kwanu, ndipo sindingadye nanu chakudya kapena kumwa madzi kwanu kuno.+ 17  Chifukwa mawu ochokera kwa Yehova+ andiuza kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko, ndipo pobwerera usakadzere njira imene udzere popita.’”+ 18  Mneneri wokalambayo atamva zimenezi, anati: “Inenso ndine mneneri ngati iweyo. Mngelo+ wandiuza mawu ochokera kwa Yehova akuti, ‘Kam’bweze upite naye kunyumba kwako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’” (Anamunamiza.)+ 19  Choncho anabwerera naye kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi kunyumba kwake.+ 20  Akudya patebulo, mawu+ a Yehova anafikira mneneri yemwe anabweza munthu wa ku Yuda uja. 21  Ndiyeno anayamba kuuza munthu wa Mulungu woona yemwe anachokera ku Yuda uja, kuti: “Nazi zimene Yehova wanena, ‘Chifukwa chakuti wapandukira+ lamulo la Yehova, ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakulamula,+ 22  koma wabwerera kuti udye chakudya ndi kumwa madzi kumalo amene iye anakuuza kuti: “Usakadye chakudya kapena kumwa madzi,” mtembo wako sudzaikidwa m’manda a makolo ako.’”+ 23  Mneneri wa ku Yuda uja atatha kudya ndi kumwa, nthawi yomweyo mneneri wokalamba uja anamanga chishalo pabulu wa mneneri wa ku Yuda, yemwe anam’bweza uja. 24  Kenako mneneri wa ku Yudayo ananyamuka n’kumapita. Pambuyo pake mkango+ unam’peza panjira n’kumupha,+ ndipo mtembo wake unali pamsewu. Kumbali ina ya mtembowo kunaima bulu uja, ndipo mbali inayi kunaima mkangowo. 25  Tsopano anthu ena amene anali kudutsa, anaona mtembowo uli pamsewupo, mkango utaima pambali pake. Anthuwo atafika mumzinda womwe munali kukhala mneneri wokalamba uja, anafotokoza zomwe anaonazo. 26  Mneneri amene anakabweza munthu uja atamva nkhaniyo, nthawi yomweyo anati: “Ndi munthu wa Mulungu woona uja amene anapandukira lamulo la Yehova.+ Choncho Yehova wam’pereka kwa mkango kuti umugwire n’kumupha, malinga ndi mawu amene Yehova anamuuza.”+ 27  Ndiyeno anauza ana ake kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Choncho ana akewo anam’mangiradi chishalocho.+ 28  Mneneri wokalambayo ananyamuka n’kukapeza mtembo wa munthu uja uli pamsewu, bulu ndi mkango zitaima pambali pake. Mkangowo sunadye mtembowo kapena kupha buluyo.+ 29  Ndiyeno mneneriyo ananyamula mtembo wa munthu wa Mulungu woona uja. Anaukweza pabulu n’kubwerera nawo mpaka kukafika mumzinda wa mneneri wokalambayo, kuti akamulire ndi kumuika m’manda munthuyo. 30  Atatero, mneneri wokalambayo anakaika mtembowo m’manda ake. Ndipo anapitiriza kumulira+ kuti: “Kalanga ine, m’bale wanga!” 31  Atamuika m’manda, mneneri wokalambayo anauza ana ake kuti: “Ine ndikadzamwalira mudzandiike m’manda amene taika munthu wa Mulungu woona uja. Mudzaike mafupa anga pambali pa mafupa ake,+ 32  chifukwa mawu a Yehova oitanira tsoka amene munthu wa Mulungu uja ananena kwa guwa lansembe+ limene lili ku Beteli, ndi kwa akachisi onse a m’malo okwezeka+ amene ali m’mizinda ya ku Samariya,+ ndithu adzakwaniritsidwa.”+ 33  Pambuyo pa zimenezi, Yerobowamu sanasiyebe njira yake yoipa. Iye anapitiriza kuika anthu wamba kukhala ansembe a malo okwezeka.+ Aliyense wofuna unsembewo, iye anali kum’patsa mphamvu+ mwa kunena kuti: “Uyu akhale wansembe wa malo okwezeka.” 34  Zimenezi zinachimwitsa nyumba yonse ya Yerobowamu,+ ndipo inayenera kuwonongedwa ndi kufafanizidwa padziko lapansi.+

Mawu a M'munsi