1 Mafumu 12:1-33
12 Rehobowamu+ anapita ku Sekemu,+ chifukwa kumeneko n’kumene Aisiraeli onse anasonkhana kuti akamulonge ufumu.
2 Yerobowamu+ mwana wa Nebati anamva zimenezi akadali ku Iguputo, (pajatu anathawa Mfumu Solomo n’kukakhala ku Iguputo),+
3 ndipo anthu anatumiza uthenga womuitana. Kenako Yerobowamu ndi mpingo wonse wa Isiraeli anabwera n’kuyamba kulankhula ndi Rehobowamu kuti:+
4 “Bambo anu anaumitsa goli lathu. Tsopano inuyo mufewetse+ ntchito yowawa ya bambo anu ndi goli lawo lolemera+ limene anatisenzetsa, ndipo tidzakutumikirani.”+
5 Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Pitani kaye kwa masiku atatu, ndipo mukabwerenso kwa ine.”+ Anthuwo anapitadi.
6 Ndiyeno Mfumu Rehobowamu inafunsira nzeru kwa akulu+ amene anali kutumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Inawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?”+
7 Iwo anaiuza kuti: “Ngati lero mukufuna kuti mukhale mtumiki wa anthuwa ndi kuwatumikira,+ muwayankhe ndi mawu abwino,+ ndipo iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”+
8 Koma iye sanamvere malangizo ochokera kwa akulu aja, m’malomwake anayamba kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi,+ omwe anali kumutumikira.+
9 Iye anawafunsa kuti: “Kodi mungapereke malangizo+ otani kuti tiwayankhe anthuwa amene andipempha kuti, ‘Fewetsani goli limene bambo anu anatisenzetsa’?”+
10 Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Izi n’zimene mukanene+ kwa anthu awa amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsireko.’ Muwauze kuti, ‘Chala changa chaching’ono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga.+
11 Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo.+ Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndikukwapulani ndi zikoti zaminga.’”+
12 Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, monga momwe mfumuyo inanenera kuti: “Mukabwerenso kwa ine pa tsiku lachitatu.”+
13 Mfumuyo inayamba kuyankha anthuwo mwaukali+ ndipo sinamvere malangizo ochokera kwa akulu amene anailangiza aja.+
14 Iyo inayamba kulankhula kwa anthuwo motsatira malangizo amene achinyamata aja+ anaipatsa. Inati: “Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera, koma ine ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”+
15 Mfumuyo sinamvere anthuwo+ chifukwa zinthu zinatembenuka chonchi mwa kufuna kwa Yehova,+ kuti akwaniritse mawu amene Yehovayo analankhula+ kwa Yerobowamu mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya+ Msilo.
16 Aisiraeli onse ataona kuti mfumuyo sinawamvere, anaiyankha kuti: “Tili ndi gawo lanji mwa Davide?+ Ife tilibe cholowa mwa mwana wa Jese. Pitani kwa milungu yanu+ Aisiraeli. Tsopano iwe Davide,+ uzisamalira nyumba yako yokha.” Aisiraeliwo atatero, anayamba kubwerera kumahema awo.
17 Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira ana a Isiraeli amene anali kukhala m’mizinda ya ku Yuda.+
18 Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Adoramu+ amene anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yokakamiza,+ koma Aisiraeli onse anam’ponya miyala+ n’kumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inatha kukwera galeta n’kuthawira ku Yerusalemu.
19 Ndipo Aisiraeli anapitiriza kuukira+ nyumba ya Davide mpaka lero.+
20 Aisiraeli onse atangomva kuti Yerobowamu wabwera, nthawi yomweyo anatumiza uthenga womuitanira kumene anasonkhana, ndipo anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse.+ Palibenso amene ankatsatira nyumba ya Davide kupatula fuko la Yuda lokha.+
21 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu,+ nthawi yomweyo anasonkhanitsa amuna ochita kusankhidwa odziwa kumenya nkhondo okwanira 180,000 a nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi nyumba ya Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu mwana wa Solomo.
22 Kenako mawu a Mulungu woona anafikira Semaya+ munthu wa Mulungu woona,+ kuti:
23 “Kauze Rehobowamu mwana wa Solomo, mfumu ya Yuda, ndi nyumba yonse ya Yuda ndi Benjamini, ndi anthu ena onse kuti,
24 ‘Yehova wati: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, ana a Isiraeli.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”’”+ Choncho anamvera mawu a Yehova+ n’kubwerera kwawo malinga ndi mawu a Yehova.+
25 Yerobowamu anamanga mzinda wa Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, n’kuyamba kukhala kumeneko. Kenako anachoka kumeneko n’kupita kukamanga mzinda wa Penueli.+
26 Ndiyeno Yerobowamu anayamba kunena mumtima mwake kuti:+ “Tsopano ufumuwu ubwerera kunyumba ya Davide.+
27 Anthu awa akapitiriza kupita kukapereka nsembe kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu,+ mtima wawo ubwerera kwa mbuye wawo Rehobowamu mfumu ya Yuda, ndipo ineyo adzandipha+ n’kubwerera kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.”
28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+
29 Ndiyeno chifaniziro cha ng’ombe chimodzi anakachiika ku Beteli,+ china anakachiika ku Dani.+
30 Chinthu chimenechi chinakhala chochimwitsa anthu.+ Anthuwo anali kukafika mpaka ku Dani kukaima pamaso pa chifaniziro cha mwana wa ng’ombecho.
31 Yerobowamu anayamba kumanga akachisi m’malo okwezeka.+ Ndiyeno anasankha anthu wamba, anthu amene sanali ana a Levi, n’kuwaika kuti akhale ansembe.+
32 M’mwezi wa 8, pa tsiku la 15 la mweziwo, Yerobowamu anachita chikondwerero chofanana ndi cha ku Yuda.+ Anachita chikondwererochi kuti apereke nsembe kwa ana a ng’ombe amene anawapanga, paguwa lansembe limene analimanga ku Beteli.+ M’malo okwezeka a ku Beteli amene anamanga, anaikako ansembe kuti azitumikira.
33 Yerobowamu anapereka nsembe pa tsiku la 15, m’mwezi wa 8 womwe anausankha yekha.+ Anapereka nsembezo paguwa limene anamanga ku Beteli. Ndipo anakonzera chikondwerero ana a Isiraeli ndi kupereka nsembe zautsi kuti afukize paguwalo.+