1 Mafumu 11:1-43

11  Mfumu Solomo inakonda akazi ambiri achilendo+ kuphatikiza pa mwana wamkazi wa Farao.+ Inakonda akazi achimowabu,+ achiamoni,+ achiedomu,+ achisidoni,+ ndi achihiti.+  Akaziwa anali ochokera m’mitundu imene Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Musamapite pakati pawo+ ndipo iwonso asamabwere pakati panu, chifukwa ndithu adzapotoza mitima yanu kuti itsatire milungu yawo.”+ Amenewa ndi amene Solomo anaumirira+ kuwakonda.  Choncho iye anali ndi akazi olemekezeka 700, ndi akazi ena apambali 300. M’kupita kwa nthawi,+ akazi amenewa anapotoza mtima wa Solomo.  Pamene iye anali kukalamba,+ akazi ake anali atapotoza+ mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina.+ Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu+ monga mmene anachitira Davide bambo ake.  Solomo anayamba kutsatira Asitoreti,+ mulungu wamkazi wa Asidoni, ndi Milikomu,+ chonyansa cha Aamoni.  Chotero Solomo anayamba kuchita zinthu zimene zinali zoipa+ m’maso mwa Yehova, ndipo sanatsatire Yehova ndi mtima wonse ngati Davide bambo ake.+  Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni.  Izi n’zimene anachitira akazi ake onse achilendo+ amene anali kupereka nsembe zautsi ndi nsembe zina kwa milungu yawo.+  Koma Yehova anamukwiyira kwambiri+ Solomo chifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene anamuonekera kawiri konse.+ 10  Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatire milungu ina,+ koma iye sanasunge zimene Yehova analamula. 11  Tsopano Yehova anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiponso sunasunge pangano langa ndi malamulo amene ndinakulamula, ndidzang’amba ufumuwu kuuchotsa kwa iwe, ndipo ndithu ndidzaupereka kwa mtumiki wako.+ 12  Komabe, sindichita zimenezi iwe uli ndi moyo+ chifukwa cha bambo ako Davide.+ Ufumuwu ndidzaung’amba ndi kuuchotsa m’manja mwa mwana wako,+ 13  koma sindidzauchotsa wonse.+ Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga+ ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha.”+ 14  Kenako Yehova anasankha munthu woti azilimbana+ ndi Solomo.+ Munthuyo dzina lake linali Hadadi, Mwedomu, mbadwa ya mfumu, ndipo anali kukhala ku Edomu.+ 15  Pa nthawi imene Davide anawononga Edomu,+ Yowabu, mkulu wa asilikali, anapita kukafotsera anthu amene anaphedwa. Kumeneko anayambanso kupha mwamuna aliyense wa ku Edomu.+ 16  (Yowabu ndi Aisiraeli onse anakhala kumeneko miyezi 6, kufikira atapha mwamuna aliyense mu Edomu.) 17  Koma Hadadi pamodzi ndi amuna ena achiedomu omwe anali atumiki a bambo ake, anathawira ku Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Hadadi ali kamnyamata. 18  Iwo ananyamuka ku Midiyani+ n’kukafika ku Parana.+ Kumeneko anatenga anthu ena n’kukafika ku Iguputo kwa Farao mfumu ya Iguputo. Faraoyo anam’patsa nyumba Hadadi, ndiponso chakudya ndi malo. 19  Farao anapitiriza kum’komera mtima Hadadi,+ moti mpaka anam’patsa mkazi.+ Mkaziyo anali mng’ono wake wa Takipenesi, mkazi wa Farao. 20  M’kupita kwa nthawi, mng’ono wake wa Takipenesi anaberekera Hadadi mwana wamwamuna dzina lake Genubati. Takipenesi anamusiyitsa kuyamwa+ mwanayo n’kuyamba kumusamalira m’nyumba ya Farao. Genubati anapitiriza kukhala m’nyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao. 21  Hadadi ali ku Iguputo, anamva kuti Davide anamwalira ndipo anagona m’manda pamodzi ndi makolo ake,+ ndiponso kuti Yowabu mkulu wa asilikali anamwalira.+ Choncho Hadadi anauza Farao kuti: “Ndiloleni ndizipita+ kwathu.” 22  Koma Farao anamufunsa kuti: “Kodi ukusowa chiyani pamene ukukhala ndi ine kuti ufune kupita kwanu?” Hadadi anayankha kuti: “Palibe chimene ndikusowa, koma chonde ndiloleni ndizipita.” 23  Mulungu anasankha munthu winanso woti azilimbana+ ndi Solomo. Munthuyo anali Rezoni mwana wa Eliyada, yemwe anathawa kwa mbuye wake Hadadezeri,+ mfumu ya Zoba.+ 24  Davide atapha+ anthu a ku Zoba, Rezoni anayamba kusonkhanitsa anthu kumbali yake, ndipo anakhala mtsogoleri wa gulu la achifwamba. Chotero iye ndi gulu lakelo anapita kukakhala ku Damasiko,+ n’kuyamba kulamulira kumeneko. 25  Rezoni analimbana ndi Isiraeli masiku onse a Solomo,+ ndipo anali kuchitira Aisiraeli zoipa monga momwe ankachitira Hadadi. Rezoni ankaipidwa kwambiri+ ndi Isiraeli pa nthawi imene iye anali kulamulira ku Siriya. 26  Panalinso Yerobowamu,+ mwana wa Nebati, wa fuko la Efuraimu, wa ku Zereda. Iye anali mtumiki wa Solomo.+ Mayi ake anali mkazi wamasiye dzina lake Zeruwa. Nayenso Yerobowamu anayamba kuukira mfumu.+ 27  Iye anaukira mfumu pa chifukwa ichi: Solomo anamanga Chimulu cha Dothi*+ ndiponso anatseka mpata umene unali pampanda wa Mzinda wa Davide bambo ake.+ 28  Yerobowamu anali mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima.+ Solomo ataona kuti mnyamatayo anali wogwira ntchito molimbika,+ anamuika kukhala woyang’anira+ ntchito yonse yokakamiza+ ya kunyumba ya Yosefe.+ 29  Pa nthawi imeneyo, Yerobowamu anatuluka mu Yerusalemu, ndipo Ahiya+ Msilo+ yemwe anali mneneri, anam’peza panjira. Ahiya anali atavala chovala chatsopano. Awiriwo anali okhaokha kumeneko. 30  Ndiyeno Ahiya anatenga chovala chatsopano chimene anavala chija n’kuching’ambang’amba+ zidutswa zokwana 12.+ 31  Atatero, anamuuza Yerobowamu kuti: “Tengapo zidutswa 10, pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wati, ‘Ndikung’amba ufumuwu kuuchotsa m’manja mwa Solomo, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko 10.+ 32  Fuko limodzi+ lipitiriza kukhala lake chifukwa cha mtumiki wanga Davide,+ ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu+ umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli. 33  Ndichita zimenezi chifukwa iwo andisiya ine+ n’kuyamba kugwadira Asitoreti+ mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi+ mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu+ mulungu wa ana a Amoni. Sanayende m’njira zanga mwa kuchita choyenera pamaso panga ndi kutsatira malamulo anga ndi zigamulo zanga monga anachitira Davide bambo a Solomo. 34  Koma sindidzachotsa ufumu wonse m’manja mwake. Ndidzamuika kukhala mtsogoleri masiku onse a moyo wake chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndinamusankha,+ pakuti Davide anasunga malamulo anga ndi zigamulo zanga. 35  Ndidzachotsadi ufumuwu m’manja mwa mwana wake ndi kuupereka kwa iwe, ndithu ndidzakupatsa mafuko 10.+ 36  Mwana wake ndidzam’patsa fuko limodzi kuti Davide mtumiki wanga apitirize kukhala ndi nyale pamaso panga mu Yerusalemu,+ mzinda umene ndausankha kuti ndiikepo dzina langa.+ 37  Ndidzasankha iweyo, ndipo udzalamuliradi zonse zimene moyo wako umakhumba.+ Udzakhaladi mfumu ya Isiraeli. 38  Ukamvera malamulo anga onse, ndipo ukayenda m’njira zanga ndi kuchita zoyenera pamaso panga, mwa kusunga malamulo anga monga anachitira Davide mtumiki wanga,+ inenso ndidzakhala nawe.+ Ana ako adzalamulira kwa nthawi yaitali mofanana ndi ana a Davide,+ ndipo ndidzakupatsa Isiraeli. 39  Ndidzachititsa manyazi ana a Davide chifukwa cha zoipa zimene anachita,+ koma osati nthawi zonse.’”+ 40  Chotero Solomo anayamba kufunafuna kupha Yerobowamu.+ Choncho Yerobowamu ananyamuka n’kuthawira+ ku Iguputo kwa Sisaki,+ mfumu ya Iguputo. Anakhala ku Iguputoko mpaka Solomo atamwalira. 41  Nkhani zina zokhudza Solomo ndi zonse zimene anachita, ndiponso nzeru zake, zinalembedwa m’buku lonena za Solomo. 42  Masiku onse amene Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu anakwana zaka 40.+ 43  Kenako Solomo anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide+ bambo ake. Kenako mwana wake Rehobowamu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.