1 Atesalonika 5:1-28
5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo+ abale, simukufunika kukulemberani kanthu.
2 Pakuti inu eni mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.+
3 Pamene azidzati:+ “Bata ndi mtendere!”+ chiwonongeko+ chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati,+ ndipo sadzapulumuka.+
4 Koma inu abale simuli mu mdima ayi,+ kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.+
5 Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala+ ndiponso ana a usana.+ Si ife a usiku kapena a mdima ayi.+
6 Chotero tisapitirize kugona+ ngati mmene enawo akuchitira,+ koma tikhalebe maso+ ndipo tikhalebe oganiza bwino.+
7 Pakuti ogona+ amagona usiku,+ ndipo amene amaledzera amakonda kuledzera usiku.
8 Koma ife amene tili a usana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa+ chachikhulupiriro+ ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo chachipulumutso+ monga chisoti,+
9 chifukwa Mulungu sanatisankhe kuti tidzaone mkwiyo.+ Anatisankha kuti tipeze chipulumutso+ kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+
10 Iye anatifera,+ kuti kaya tikhala maso kapena tigona, tikhale ndi moyo limodzi ndi iye.+
11 Choncho pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana+ monga mmene mukuchitira.+
12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani+ mwa Ambuye ndi kukulangizani.
13 Muwapatse ulemu waukulu mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo.+ Khalani mwamtendere pakati panu.+
14 Komanso tikukudandaulirani abale kuti, langizani ochita zosalongosoka,+ lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni,+ thandizani ofooka, khalani oleza+ mtima kwa onse.
15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense,+ koma nthawi zonse yesetsani kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.+
16 Muzikhala okondwera nthawi zonse.+
17 Muzipemphera mosalekeza.+
18 Muziyamika+ pa chilichonse, pakuti chimenechi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
19 Musazimitse moto wa mzimu.+
20 Musanyoze mawu aulosi.+
21 Tsimikizirani zinthu zonse.+ Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.+
22 Pewani zoipa zamtundu uliwonse.+
23 Mulungu wamtendere+ mwiniyo akupatuleni+ kuti muchite utumiki wake. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, ndi thupi lanu, zisungidwe zopanda chilema ndi zopanda cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+
24 Amene akukuitanani ndi wokhulupirika, ndipo adzachitadi zimenezi.
25 Abale, pitirizani kutipempherera.+
26 Perekani moni kwa abale onse ndi kupsompsonana kwaubale.+
27 Ndikukulamulani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.+
28 Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.