1 Atesalonika 2:1-20

2  Kunena zoona, inuyo mukudziwa abale, kuti ulendo+ wathu kwa inu sunali wopanda phindu.+  Koma mukudziwa kuti choyamba titavutika+ ndi kuchitidwa zachipongwe+ ku Filipi,+ tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula+ kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.  Pakuti sitikukudandaulirani chifukwa cha maganizo olakwika kapena odetsedwa,+ kapenanso mwachinyengo ayi.  Koma popeza Mulungu wationa kuti ndife oyenera kupatsidwa+ ntchito yolalikira uthenga wabwino, tikulankhula monga anthu okondweretsa+ Mulungu, yemwe amavomereza mitima+ yathu, osati monga okondweretsa anthu.  Ndipotu, sitinayambe talankhulapo mawu okuyamikirani mwachinyengo,+ (monga mukudziwira), kapena kuchita zachiphamaso+ chifukwa cha kusirira kwa nsanje.+ Mulungu ndiye mboni yathu.  Sitinali kungodzifunira ulemerero kwa anthu+ ayi, kaya kwa inu kapena kwa anthu ena. Sitinatero, ngakhale kuti monga atumwi a Khristu, tikanatha kupempha kuti mutilipirire+ zinthu zina kuti mutithandize.  M’malomwake, tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira+ ana ake.  Choncho popeza timakukondani kwambiri,+ tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo+ yathu yeniyeniyo, chifukwa tinakukondani kwambiri.+  Ndithudi abale, mukukumbukira ntchito+ yathu imene tinagwira mwakhama ndi thukuta lathu. Mwa kugwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza,+ tinalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu. 10  Inu ndinu mboni, Mulungunso ndi mboni, za mmene tinakhalira okhulupirika, olungama, ndi opanda chifukwa chotinenezera,+ kwa inu okhulupirira. 11  Mogwirizana ndi zimenezi, inu mukudziwa bwino mmene tinali kudandaulira kwa aliyense wa inu, monga mmene bambo+ amachitira ndi ana ake, kukulimbikitsani+ ndi kukuchondererani, 12  n’cholinga choti mupitirize kuyenda+ m’njira imene Mulungu, amene akukuitanani+ ku ufumu+ wake ndi ulemerero, amafuna. 13  Ndithudi, n’chifukwa chake ifenso timayamikadi+ Mulungu mosalekeza. Pakuti pamene munalandira mawu a Mulungu+ amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu+ ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. Mawu amenewa akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira.+ 14  Pakuti inu abale munatsanzira mipingo ya Mulungu yogwirizana ndi Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Munatero chifukwa inunso munayamba kuvutitsidwa+ ndi anthu akwanu, ngati mmene iwonso akuvutitsidwira ndi Ayuda, 15  amene anapha ngakhale Ambuye Yesu+ ndi aneneri+ ndi kuzunzanso ifeyo.+ Ndipo iwo sakukondweretsa Mulungu, koma akutsekereza zinthu zopindulitsa anthu onse. 16  Akutero pamene akuyesa kutiletsa+ kulankhula kwa anthu a mitundu ina kuti angapulumutsidwe.+ Chotsatira chake n’chakuti, pochita zimenezi nthawi zonse akudzazitsa+ machimo awo. Koma tsopano mkwiyo wake wawafikira.+ 17  Koma ifeyo abale, pamene tinakakamizika kusiyana nanu kwa nthawi yochepa, tinapitiriza kukukumbukirani ngakhale kuti sitinali kukuonani, ndipo tinayesetsa kwambiri kuti tikwaniritse chilakolako+ chachikulu chimene tinali nacho chofuna kuona nkhope zanu. 18  Pa chifukwa chimenechi, tinafuna kubwera kwa inu. Ineyo Paulo ndinafuna kubwera kawiri konse, koma Satana anatchinga njira yathu. 19  Kodi chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe chathu n’chiyani? Inde, mphoto*+ yathu yoinyadira pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake n’chiyani? Si inu amene kodi? 20  Ndithudi, inu ndinudi ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Onani Zakumapeto 8.