1 Akorinto 9:1-27

9  Kodi sindine mfulu?+ Kodi sindine mtumwi?+ Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu?+ Kodi inu sindinu ntchito yanga mwa Ambuye?  Ngati sindine mtumwi kwa ena, mosakayikira ndine mtumwi kwa inu, popeza ndinu chidindo chotsimikizira+ utumwi wanga mwa Ambuye.  Yankho langa kwa amene amandikayikira ndi ili:+  Tili ndi ufulu wa kudya+ ndi kumwa, si choncho kodi?  Tili ndi ufulu wotenga alongo amene ndi akazi athu+ pa maulendo, mmene amachitira atumwi ena onse ndiponso abale a Ambuye+ komanso Kefa,+ si choncho kodi?  Kapena kodi ine ndi Baranaba+ ndife tokha amene tilibe ufulu wosiya kugwira ntchito yakuthupi?+  Alipo kodi msilikali amene amatumikira, koma n’kumadzilipira yekha? Ndani amalima munda wa mpesa koma osadya zipatso zake?+ Kapena ndani amaweta ziweto koma osamwako mkaka wake?+  Kodi ndikulankhula zinthu izi mwa nzeru za anthu?+ Kodi Chilamulo+ sichinenanso zinthu zimenezi?  Pakuti m’chilamulo cha Mose muli mawu akuti: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+ Kodi ndi ng’ombe zimene Mulungu akusamalira? 10  Kapena kodi mawu amenewo kwenikweni akunenera ife? Ndithudi, mawu amenewo analembera ife,+ chifukwa wolima ayenera kulima ndi chiyembekezo ndipo munthu wopuntha mbewu azipuntha ndi chiyembekezo chodzadya nawo.+ 11  Ngati tabzala zinthu zauzimu+ mwa inu, kodi ndi nkhani yaikulu ngati tikukolola zinthu zakuthupi mwa inu?+ 12  Ngati anthu ena amagwiritsa ntchito ufulu umenewu pa inu,+ kodi ife sitili oyenera kutero kuposa amenewo? Ngakhale zili choncho, sitinagwiritse ntchito ufulu umenewo,+ koma timadzichitira tokha zinthu zonse, kuti tisapereke chododometsa chilichonse ku uthenga wabwino+ wonena za Khristu. 13  Kodi simukudziwa kuti anthu ochita ntchito zopatulika amadya+ za m’kachisi, ndipo amene amatumikira+ kuguwa lansembe nthawi zonse amagawana gawo ndi guwa lansembe? 14  Momwemonso, Ambuye anakonza+ kuti olengeza uthenga wabwino azipeza zodzisamalira pa moyo kudzera mwa uthenga wabwino.+ 15  Koma sindinagwiritse ntchito dongosolo lililonse loterolo.+ Ndiponso, sikuti ndalemba zimenezi kuti dongosolo limeneli liyambe kugwira ntchito kwa ine ayi, pakuti zingakhale bwino kuti ineyo ndife kusiyana ndi kuti . . . ndipo palibe munthu angatsutse chifukwa chimene ndikudzitamira!+ 16  Tsopano ngati ndikulengeza uthenga wabwino,+ chimenechi si chifukwa chodzitamira, pakuti ndinalamulidwa kutero.+ Ndithudi, tsoka+ kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino! 17  Ndikachita zimenezi mwaufulu,+ ndili ndi mphoto.+ Koma ndikachita motsutsana ndi kufuna kwanga, sindingachitire mwina, ndinebe woyang’anira mogwirizana ndi udindo+ umene unaikidwa m’manja mwanga. 18  Choncho mphoto yanga ndi chiyani? Ndi yakuti polengeza uthenga wabwino ndipereke uthengawo kwaulere,+ kuti ndisagwiritse ntchito molakwa ufulu wanga pa zinthu zokhudzana ndi uthenga wabwino. 19  Pakuti ngakhale ndine womasuka kwa anthu onse, ndadzipanga kapolo+ kwa onse, kuti ndipindule+ anthu ochuluka. 20  Motero kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda,+ kuti ndipindule Ayuda. Kwa anthu otsatira chilamulo+ ndinakhala ngati wotsatira chilamulo+ kuti ndipindule anthu otsatira chilamulo, ngakhale kuti sindili pansi pa chilamulo. 21  Kwa anthu opanda chilamulo+ ndinakhala ngati wopanda chilamulo,+ kuti ndipindule anthu opanda chilamulo. Ngakhale zili choncho, sikuti ndine wopanda chilamulo+ kwa Mulungu koma ndili pansi pa chilamulo kwa Khristu.+ 22  Kwa ofooka ndinakhala wofooka, kuti ndipindule ofooka.+ Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana,+ kuti mulimonse mmene zingakhalire ndipulumutseko ena. 23  Koma ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso+ kwa ena. 24  Kodi simukudziwa kuti ochita mpikisano wa liwiro+ amathamanga onse, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto?+ Thamangani+ m’njira yoti mukalandire mphotoyo.+ 25  Ndiponso, munthu aliyense wochita nawo mpikisano amakhala wodziletsa+ pa zinthu zonse. Iwo amachita zimenezo kuti apeze nkhata ya kumutu imene imawonongeka,+ koma ife, kuti tikapeze nkhata ya kumutu yosakhoza kuwonongeka.+ 26  Motero, sikuti ndikungothamanga+ osadziwa kumene ndikulowera. Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi,+ 27  koma ndikumenya thupi langa+ ndi kulitsogolera ngati kapolo, kuopera kuti, pambuyo poti ndalalikira kwa ena, ineyo ndingakhale wosayenera+ m’njira inayake.

Mawu a M'munsi