1 Akorinto 7:1-40

7  Tsopano pa nkhani imene munalemba ija, ndi bwino kuti mwamuna asakhudze+ mkazi.  Koma chifukwa cha kuwanda kwa dama,*+ mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake+ ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.  Mwamuna azipereka kwa mkazi wake mangawa ake,+ mkazinso achite chimodzimodzi kwa mwamuna wake.+  Mkazi asachite ulamuliro pathupi lake. Ulamulirowo ukhale ndi mwamuna wake.+ Mwamunanso asachite ulamuliro pathupi lake, koma ulamulirowo ukhale ndi mkazi wake.+  Musamanane,+ kupatulapo ngati mwagwirizana kuimitsa kaye mangawawo kwa nthawi yodziwika,+ kuti muthere nthawi pa kupemphera, kenako mukhalenso mwa nthawi zonse, kuopera kuti Satana angapitirize kumakuyesani+ mukalephera kudzigwira.+  Komabe, ndikunena zimenezi mokupatsani ufulu wozitsatira,+ osati mokulamulani.+  Koma ndikanakonda amuna onse akanakhala ngati ineyo.+ Komabe, aliyense ali ndi mphatso+ yake yochokera kwa Mulungu. Wina m’njira iyi, winanso m’njira inayo.  Tsopano ndikunena kwa osakwatira+ ndi kwa akazi amasiye kuti, ndi bwino akhalebe mmene ineyo ndililimu.+  Koma ngati sangathe kudziletsa,+ akwatire, pakuti ndi bwino kukwatira+ kusiyana ndi kuvutika ndi chilakolako.+ 10  Kwa okwatira ndikupereka malangizo awa, kwenikweni osati ineyo koma Ambuye,+ kuti mkazi asasiye mwamuna wake,+ 11  koma ngati angamusiye, akhale choncho wosakwatiwa. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna wakeyo. Mwamunanso asasiye mkazi wake. 12  Koma kwa enawa, ineyo, osati Ambuye,+ ndikunena kuti: Ngati pali m’bale amene ali ndi mkazi wosakhulupirira, ndipo mkaziyo akulola kukhala naye, asamusiye mkaziyo. 13  Ndiponso mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo. 14  Pakuti mwamuna wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wake, ndiponso mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha m’baleyo, apo ayi, ana anu akanakhala osayera,+ koma tsopano ndi oyera.+ 15  Koma ngati wosakhulupirirayo wachoka,+ achoke. M’bale kapena mlongo sakhala womangika zinthu zikatero, koma Mulungu anakuitanani kuti mukhale mu mtendere.+ 16  Pakuti mkaziwe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mwamuna wako?+ Kapena mwamunawe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mkazi wako?+ 17  Munthu aliyense akhale mmene Yehova wamugawira gawo lake,+ mmene Mulungu wamuitanira.+ Izi n’zimene ndikukhazikitsa+ m’mipingo yonse. 18  Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wodulidwa?+ Akhalebe wodulidwa. Alipo kodi amene anaitanidwa ali wosadulidwa?+ Asadulidwe.+ 19  Mdulidwe+ sutanthauza kalikonse, ndipo kusadulidwa+ sikutanthauza kanthu, koma kusunga malamulo a Mulungu ndiko kofunika.+ 20  Wina aliyense akhalebe+ mmene analili poitanidwa.+ 21  Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usade nazo nkhawa zimenezo,+ koma ngati ungathenso kumasuka, tengerapo mwayi pamenepo. 22  Pakuti aliyense amene ali mwa Ambuye amene anaitanidwa ali kapolo ndi womasulidwa wa Ambuye,+ momwemonso amene anaitanidwa ali mfulu+ ndi kapolo+ wa Khristu. 23  Munagulidwa pa mtengo wokwera,+ lekani kukhala akapolo+ a anthu. 24  Abale, wina aliyense akhalebe mmene analili+ poitanidwa, ndipo akhalebe pa ubwenzi ndi Mulungu. 25  Tsopano kunena za amene sali pabanja,* ndilibe lamulo lililonse la Ambuye, koma ndikupereka maganizo anga+ monga munthu amene ndinasonyezedwa chifundo ndi Ambuye+ kuti ndikhale wokhulupirika.+ 26  Chotero ndikuganiza kuti zingakhale bwino, malinga ndi mavuto amene tili nawo, kuti mwamuna akhalebe mmene alili.+ 27  Kodi ndiwe womangika kwa mkazi?+ Leka kufunafuna njira yomasukira.+ Kodi ndiwe womasuka kwa mkazi? Leka kufunafuna mkazi. 28  Koma ngakhale utakwatira, sikuti uchimwa.+ Ndipo ngati amene sali pabanja* walowa m’banja, sikuti wachimwa. Komabe, olowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.+ Choncho ine ndikukutetezani. 29  Komanso abale dziwani izi: Nthawi yotsalayi yafupika.+ Choncho amene ali ndi akazi azikhala ngati alibe,+ 30  ndipo amene akulira azikhala ngati amene sakulira. Amene akusangalala azikhala ngati amene sakusangalala, ndipo amene amagula zinthu azikhala ngati opanda kanthu. 31  Amene amagwiritsira ntchito dzikoli+ azikhala ngati amene sakuligwiritsira ntchito mokwanira, pakuti zochitika za padzikoli zikusintha.+ 32  Ndithudi, ndikufuna kuti mukhale opanda nkhawa.+ Mwamuna wosakwatira amadera nkhawa zinthu za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuye. 33  Koma mwamuna wokwatira amadera nkhawa+ zinthu za dziko, mmene angakondweretsere mkazi wake,+ 34  ndipo amakhala wogawanika. Nayenso mkazi wosakwatiwa, komanso namwali, amadera nkhawa zinthu za Ambuye,+ kuti akhale woyera m’thupi lake ndi mu mzimu wake. Koma mkazi wokwatiwa amadera nkhawa zinthu za dziko, mmene angakondweretsere mwamuna wake.+ 35  Ndikunenatu zimenezi kuchitira ubwino wanu, osati kuti ndikuchititseni kukhala omangika, koma kuti ndikulimbikitseni kuchita choyenera+ ndiponso kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.+ 36  Koma ngati wina akuona kuti zikumuvuta kukhalabe yekha,*+ ngati wapitirira pachimake pa unyamata, ndipo ngati ziyenera kutero, achite mmene akufunira, sachimwa. Akwatire.+ 37  Koma ngati wina ndi wokhazikika mumtima mwake ndipo alibe chomuvutitsa, koma amatha kulamulira mtima wake, ndipo wasankha mumtima mwake kukhalabe wosakwatira,* wachita bwino.+ 38  Nayenso amene walekana ndi moyo wokhala yekha* n’kulowa m’banja wachita bwino,+ koma amene sanalowe m’banja wachita bwino koposa.+ 39  Mkazi ndi womangika pa nthawi yonse imene mwamuna wake ali moyo.+ Komano mwamuna wake akamwalira, mkaziyo ndi womasuka kukwatiwa ndi aliyense amene akufuna, koma akwatiwe mwa Ambuye.+ 40  Komabe angakhale wosangalala kwambiri ngati apitiriza mmene alili.+ Ndi mmene ine ndikuonera. Ndipo ndine wotsimikiza mtima kuti ndilinso ndi mzimu wa Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Mawu ake enieni, “anamwali.”
Mawu ake enieni, “namwali.”
Mawu ake enieni, “kusungabe unamwali wake.”
Mawu ake enieni, “kusunga unamwali wake.”
Onani mawu a m’munsi pavesi 36.