1 Akorinto 6:1-20

6  Kodi wina wa inu akakhala ndi mlandu+ ndi mnzake, amalimba mtima bwanji kupita kukhoti kwa anthu osalungama,+ osati kwa oyerawo?+  Kapena simukudziwa kuti oyerawo adzaweruza+ dziko?+ Ndipo ngati mudzaweruza dziko, kodi simungathe kuzenga milandu yaing’ono kwambiri+ ngati imeneyo?  Kodi simukudziwa kuti tidzaweruza angelo?+ Ndiye tingalephere bwanji kuweruza nkhani za m’moyo uno?  Chotero, ngati muli ndi nkhani zofuna kuweruza+ m’moyo uno, kodi anthu amene mpingo suwayesa kanthu ndiwo mukuwaika kukhala oweruza?+  Ndikulankhula choncho kuti ndikuchititseni manyazi.+ Kodi zoona palibe wanzeru ndi mmodzi yemwe+ pakati panu amene angaweruze mlandu pakati pa abale ake?  Kodi m’bale azitengera m’bale wake kukhoti, kwa anthu osakhulupirira?+  Kunena zoona, ndiye kuti mwalephereratu ngati mukutengerana kukhoti.+ Bwanji osangolola kulakwiridwa?+ Bwanji osalola kuberedwa?+  M’malomwake, inuyo mumachita zolakwa ndiponso mumabera ena, ndipo abale anu ndi amene mumawachitira zimenezi.+  Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu?+ Musasocheretsedwe. Adama,+ opembedza mafano,+ achigololo,+ amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo,+ amuna ogona amuna anzawo,+ 10  akuba, aumbombo,+ zidakwa,+ olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.+ 11  Ndipo ena mwa inu munali otero.+ Koma mwasambitsidwa kukhala oyera,+ mwapatulidwa,+ mwayesedwa olungama+ m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu,+ komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.+ 12  Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka+ kwa ine, koma sindidzalola kuti chinthu china chizindilamulira.+ 13  Chakudya ndi cha mimba, ndipo mimba ndi ya chakudya,+ koma Mulungu adzawononga mimba ndi chakudya chomwe.+ Choncho thupi silochitira dama koma ndi la Ambuye,+ ndipo Ambuye ndiye mwini thupi.+ 14  Koma Mulungu anaukitsa Ambuye+ kwa akufa+ ndipo adzaukitsanso ife mwa mphamvu yake.+ 15  Kodi simukudziwa kuti matupi anu ndiwo ziwalo+ za Khristu?+ Ndiye kodi ine nditenge ziwalo za Khristu n’kuzisandutsa ziwalo za hule?+ Zosatheka zimenezo! 16  Kodi zoona inu simukudziwa kuti amene wadziphatika kwa hule amakhala thupi limodzi ndi hulelo? Pakuti anati, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 17  Koma amene waphatikana ndi Ambuye wakhala mzimu+ umodzi ndi iye.+ 18  Thawani dama.+ Tchimo lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita dama amachimwira thupi lake.+ 19  Kodi zoona inu simukudziwa kuti thupi lanu ndilo kachisi+ wa mzimu woyera umene uli mwa inu,+ umene munapatsidwa ndi Mulungu? Ndiponso mwiniwake wa inuyo si inu,+ 20  pakuti munagulidwa pa mtengo wokwera.+ Mulimonse mmene zingakhalire, lemekezani Mulungu+ ndi matupi anu.+

Mawu a M'munsi